Pitani ku nkhani yake

JULY 26, 2019
SPAIN

Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Madrid, Spain

Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Madrid, Spain
  • Masiku: 19 mpaka 21 July, 2019

  • Malo: Wanda Metropolitano Stadium ku Madrid, Spain

  • Zinenero: Chingelezi, Chisipanishi, Chinenero Chamanja cha ku Spain

  • Chiwerengero cha Osonkhana: 52,516

  • Chiwerengero cha Obatizidwa: 434

  • Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 6,300

  • Nthambi Zoitanidwa: Albania, Argentina, Bulgaria, Canada, Central America, Dominican Republic, Ghana, Hungary, Korea, Netherlands, Peru, Slovenia, Taiwan, Turkey, ndi United States

  • Zina Zimene Zinachitika: A César López, omwe ndi mkulu wa imodzi mwa mahotela amene alendo omwe anapita kumsonkhano ankakhala, anati: “Taona zinthu zochititsa chidwi kwambiri. Chinthu chimodzi chimene anthu athu ogwira ntchito ankakambirana nthawi zambiri chinali chokhudza anthu amene anabwera kumsonkhanowu, kumwetulira kwawo, khalidwe lawo labwino komanso anali aubwenzi. Ndikuganiza kuti uthenga wanu [wakuti “Chikondi Sichitha”] ndi umene alendowa anali ataphunzira kale asanabwere kuno. Chikondichi chinasonyezedwa ndi aliyense amene anakhala pahotela yathu. Tingakonde alendo anu atadzabweranso kuno.”

 

Abale ndi alongo a ku Spain akupereka moni mosangalala kwa alendo omwe afika pabwalo la ndege la Adolfo Suárez Madrid-Barajas Airport

Mlongo wa ku Spain akulalikira ku Madrid limodzi ndi mlongo wochokera kudziko lina pogwiritsa ntchito timapepala toitanira anthu kumsonkhano

Alendo akukhamukira kumalo a msonkhano kukamvetsera chigawo cham’mawa cha msonkhano

Alendo ochokera kumayiko ena akumwetulira komanso kubayibitsa msonkhano utatha pa tsiku Lachisanu

Achinyamata awiri a Mboni omwe ali ku amodzi mwa malo amene msonkhanowu unalumikizidwa, anyamula mafoni ndipo akuonetsa Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso la Chisipanishi. Baibuloli linatulutsidwa ku Madrid komanso m’malo ena 11 m’dziko la Spain Lachisanu pa nthawi yofanana

Mmodzi mwa abale ndi alongo 434 atsopano akumwetulira atangobatizidwa

Abale ndi alongo ochokera m’mayiko ena omwe ali muutumiki wanthawi zonse akubayibitsa anthu m’bwalo la malo a msonkhano pa tsiku lomaliza la msonkhanowu

Abale ndi alongo akuomba m’manja mosangalala msonkhano uli mkati

M’bale Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira akupatsana moni ndi mmodzi mwa alongo omwe ali muutumiki a nthawi zonse pambuyo pa msonkhanowu

Alongo akuvina gule wachikhalidwe cha ku Spain atavala madiresi okongola pa nthawi ya zochitika zamadzulo