Pitani ku nkhani yake

DECEMBER 2, 2019
TOGO

Madzi Asefukira Kwambiri ku Togo

Madzi Asefukira Kwambiri ku Togo

Mvula yamphamvu kwambiri yomwe yakhala ikugwa mowirikiza m’nyengo yamvula ya mu 2019 ku Togo, yachititsa kuti madzi asefukire m’madera ena mumzinda wa Lomé m’dzikolo. Ofalitsa 257 a m’mipingo 7 anakhudzidwa ndi madzi osefukirawa ndipo ntchito yopereka chithandizo ili mkati.

M’madera ena omwe anakhudzidwa ndi mvulayi, madzi omwe analowa m’nyumba zina ankafika mita imodzi, ndipo abale ndi alongo athu 51 anathawa m’nyumba zawo. Ofalitsa apafupi analandira m’nyumba zawo abale ndi alongo omwe akusowa pokhala.

Madzi osefukirawa anachititsa kuti madzi awonongeke m’malo ena omwe anthu amatungamo madzi. Komiti ya Nthambi ya Benin yomwe imayang’anira ntchito yathu ku Togo, yakonza dongosolo lopereka zinthu zofunika kwa abale ndi alongo omwe akhudzidwa kudzera mwa oyang’anira madera ndi akulu. Zina mwa zinthuzi ndi mankhwala ophera majeremusi m’madzi, ophera tizilombo toyambitsa matenda komanso ophera majeremusi pochapa zovala ndi zinthu zina.

Tikupemphera kuti Yehova apitirize kudalitsa abale athu ku Togo pamene akuyesetsa kudzimana posonyezana chikondi.—Yohane 13:34, 35.