Pitani ku nkhani yake

JANUARY 16, 2020
UNITED KINGDOM

Banja la Beteli ku Britain Likusamukira ku Chelmsford

Banja la Beteli ku Britain Likusamukira ku Chelmsford

Pa 1 January, 2020, banja la Beteli ku Britain linayamba ntchito yosamukira ku Beteli yatsopano yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Chelmsford ku Essex. Pofika kumayambiriro kwa March 2020, atumiki onse a pa Beteli omwe akukhala ku nthambi yakale adzayamba kukhala komanso kugwira ntchito ku maofesi a nthambi yatsopanoyi.

Ofesi ya nthambi ya Britain yakhala ili ku Mill Hill mumzinda wa London kuyambira mu 1959. Pamene ntchito yolalikira komanso ntchito zina zinkawonjezereka, nyumba zina zinagulidwa m’madera osiyanasiyana ku London. Zimenezi zinachititsa kuti pakhale ntchito yaikulu yokonzanso nyumbazi komanso atumiki a pa Beteli ankafunika kumayendayenda kwambiri. Ofesi ya nthambiyi inkasindikizanso mabuku. Pa nthawi ina, nthambiyi inkasindikiza mabuku oposa 10 peresenti ya chiwerengero cha mabuku omwe timasindikiza padziko lonse. Mu March 2018, makina osindikizira mabuku omwe anagwira ntchito kwa zaka 92 anasiya kuwagwiritsa ntchito ndipo anawagulitsa. *

Abale ndi alongo omwe anathandiza nawo pa ntchito yomanga nthambi yatsopanoyi akulandira atumiki a pa Beteli omwe akusamukira kumalowa pa 1 January, 2020

Ntchito yomanga nthambi yatsopano ya Britain inatenga zaka 5. Ntchito zonse zofunika zizichitikira pamalo amodzi ndipo zimenezi zithandiza kusunga nthawi komanso kupulumutsa ndalama. Pa nthambiyi pali nyumba ziwiri zogwirira ntchito zosiyanasiyana, maofesi, ndiponso nyumba zogonamo 6 zomwe muzikhala anthu oposa 400. Nyumba ina izigwiritsidwa ntchito ngati holo, chipinda chodyera ndiponso muzichitikira zinthu zosiyanasiyana.

Panopa, ofesi ya nthambi ya Britain imayang’anira ntchito yolalikira ya magawo angapo kuphatikizapo Falkland Islands, Guernsey, Ireland, Isle of Man, Jersey, ndi Malta. Nthambi yatsopanoyi izigwira ntchito yopanga mavidiyo ndi zinthu zongomvetsera komanso mabuku a pazipangizo zamakono. Kuwonjezera pamenepa, nthambiyi ipitiriza kuyendetsa ntchito zokhudza kulambira monga kulalikira ndi kuphunzitsa, zomwe ofalitsa oposa 150,000 amagwira m’mipingo yopitirira 1,800.

Kuyambira pa 6 April, 2020, alendo adzayamba kuona malo pa Beteli yatsopanoyi. Alendo ayembekezere kudzasangalala ndi kuona malo ofotokoza nkhani zokhudza mbiri ya Baibulo m’dziko la Britain ndi Ireland komanso mmene Beteli imathandizira gulu la Yehova lomwe likukula mwamsanga.

M’bale Stephen Hardy, wa m’Komiti ya Nthambi ya Britain wakhala akuthandiza pa ntchito yomangayi kungoyambira pamene inayamba. Iye anafotokoza mmene abale ndi alongo ambiri anamvera pambuyo pogwira nawo ntchitoyi. Iye anati: “Yehova walimbikitsa abale ndi alongo ambiri amtima wofunitsitsa a ku Britain kuno ndi kumayiko ena kuti adzagwire nawo ntchitoyi. Zotsatirapo zake zaposa zomwe tinkayembekezera ndipo zachititsa kuti Yehova alemekezeke.”​—Aefeso 3:20.

^ Panopa ofesi ya nthambi ya Central Europe yomwe ili ku Selters m’dziko la Germany ndi imene imagwira ntchito yosindikiza mabuku a m’gawo la nthambi ya Britain

 

Chithunzi chojambulidwa kuchokera m’mwamba chosonyeza malo okongola a ofesi ya nthambi yatsopano ya Britain

Mlongo akuika mabuku pamashelefu a pamalo olandirira alendo

Abale ndi alongo omwe ayamba kumene kuyendera pabeteli akumvetsera pamene akupatsidwa malangizo m’chipinda china chochitira misonkhano

Abale ndi alongo akusangalala ndi chakudya chamasana m’chipinda chodyera chomwe chizigwiritsidwa ntchito pa zinthu zinanso zosiyanasiyana

Chikwangwani cholozera msewu wotchedwa “Kingdom Way,” chomwe chili polowera ku Beteli