Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | BANJA

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Woleza Mtima?

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Woleza Mtima?

 “Tsiku lililonse mwamuna ndi mkazi wokwatira amakumana ndi zinthu zokhumudwitsa zofunika kukhala woleza mtima. Munthu amene sali pabanja sangamvetse kufunika koleza mtima, koma khalidwe limeneli ndi lofunika kwambiri m’banja.”—John.

 N’chifukwa chiyani muyenera kukhala woleza mtima?

  •   Mukakwatirana m’pamene umayamba kuona kwambiri zimene mnzakoyo amalakwitsa.

     “Pakapita nthawi kuchokera pamene munakwatirana, umayamba kuyang’ana kwambiri zimene mnzakoyo amalakwitsa. Ndiyeno maganizo olakwikawo akakula umalephera kuugwira mtima.”—Jessena.

  •   Kusaleza mtima kungakuchititseni kuti mulankhule musanaganize.

     “Ndimafulumira kufotokoza mmene ndikumvera koma pamapeto pake ndimapezeka kuti ndalankhula zosakhala bwino. Ndikanakhala woleza mtima bwenzi ndikumayamba ndaganiza kaye, n’kuona ngati zili zoyenera kulankhula.”—Carmen.

     Baibulo limanena kuti: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.” (1 Akorinto 13:4) Mwina mungaganize kuti anthu awiri amene amakondana kwambiri sizingawavute kukhala oleza mtima. Koma si mmene zimakhalira. John tamutchula koyambirira kuja ananena kuti: “Mofanana ndi makhalidwe ena onse abwino, zimakhala zovuta kuti munthu ukhale woleza mtima, koma khalidweli silichedwa kutha. Umafunika kuchita khama kwambiri kuti khalidweli lipitirizebe kukula.”

 Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu woleza mtima?

  •   Pakachitika zinazake zomwe sizinakusangalatseni.

     Mwachitsanzo: Ngati mwamuna kapena mkazi wanu sanakulankhuleni bwino, chimene chimabwera mofulumira m’maganizo mwanu ndi kubwezera.

     Lemba lothandiza:Usamafulumire kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.”—Mlaliki 7:9.

     Mmene mungasonyezere kuleza mtima: Musanayankhe, muzidikira kaye. Musamafulumire kuganiza kuti cholinga cha mnzanuyo polankhula mawuwo chinali kukukhumudwitsani. Buku lina linanena kuti: “Ambirife timakhumudwa ndi zomwe mnzathu wanena chifukwa chongoganiza kuti akutanthauza zinazake zolakwika, pomwe nthawi zina amakhala kuti sakutanthauza zimene tikuganizazo.”—Fighting for Your Marriage.

     Ngakhale mwamuna kapena mkazi wanu atachitira dala zinthu zokukhumudwitsani, mungapewe kukangana ngati mutasonyeza kuti ndinu woleza mtima popewa kubwezera. Baibulo limanena kuti: “Popanda nkhuni moto umazima.”—Miyambo 26:20.

     “Mukangoyamba kuganiza kuti mkazi wanu ndi mdani wanu, nthawi yomweyo muziganizira chifukwa chimene mumamukondera ndipo muzimuchitira zinazake zabwino.”—Ethan.

     Zoti muganizire:

    •  Kodi mumatani ngati mwamuna kapena mkazi wanu wachita kapena kulankhula zinthu zomwe sizinakusangalatseni?

    •  Nanga ulendo wina akadzachitanso zomwezo, mungadzasonyeze bwanji kuti ndinu woleza mtima?

  •   Ngati mnzanuyo amalakwitsa zinazake mobwerezabwereza

     Mwachitsanzo: Nthawi zonse mwamuna kapena mkazi wanu amachedwa kuchita zinthu moti mumafunika kumudikira nthawi yaitali.

     Lemba lothandiza: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.”—Akolose 3:13.

     Mmene mungasonyezere kuleza mtima: Muziganizira kwambiri zimene zingathandize banja lanu, m’malo mongoganiza zofuna zanu zokha. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikakhumudwa ndi zimene mnzangayu wachita, ndilimbitsa kapena kusokoneza banja langa?’ Muzikumbukiranso kuti “tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yakobo 3:2) Zimenezi zikusonyeza kuti palinso zinthu zina zimene inuyo mumalakwitsa.

     “Nthawi zina ndimatha kuleza mtima mnzanga akalakwitsa zinazake kusiyana ndi mwamuna wanga. Mwina n’chifukwa choti nthawi zambiri ndimakhala ndi mwamuna wangayo, moti ndimadziwa mavuto ake. Koma kuleza mtima kumasonyeza kuti ndimamukonda komanso kumulemekeza ndipo zinthu zimenezi n’zofunika kwambiri kuti banja lathu liziyenda bwino.”—Nia.

     Zoti muganizire:

    •  Kodi mumaleza mtima mwamuna kapena mkazi wanu akalakwitsa zinazake?

    •  Nanga mungatani kuti m’tsogolo muzidzasonyeza kwambiri khalidwe limeneli?