Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani Anthu Amafa?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amafa?

Yankho la m’Baibulo

 Mwachibadwa anthufe timadabwa, makamaka wachibale wathu akamwalira, kuti n’chifukwa chiyani anthu amafa. Baibulo limanena kuti: “Mphamvu imene imabala imfa ndiyo uchimo.”—1 Akorinto 15:56.

N’chifukwa chiyani anthu onse amachimwa komanso kufa?

 Adamu ndi Hava, omwe anali anthu oyambirira kulengedwa, anafa chifukwa anachimwira Mulungu. (Genesis 3:17-19) Anthu anayamba kufa chifukwa Adamu ndi Hava anakana kumvera Mulungu, yemwe ndi “kasupe wa moyo.”—Salimo 36:9; Genesis 2:17.

Adamu anapatsira uchimo ana ake onse. Baibulo limanena kuti: “Monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Choncho anthu onse amafa chifukwa onse anachimwa.—Aroma 3:23.

Zimene Mulungu adzachite pothetsa imfa

 Mulungu watilonjeza kuti “adzameza imfa kwamuyaya.” (Yesaya 25:8) Iye adzachita zimenezi pochotsa chinthu chimene chimayambitsa imfayo chomwe ndi uchimo. Mulungu adzachita zimenezi kudzera mwa Yesu Khristu, amene “akuchotsa uchimo wa dziko.”—Yohane 1:29; 1 Yohane 1:7.