Kodi Ndingatchule Zinthu Ziti Popemphera?
Yankho la m’Baibulo
Popemphera mukhoza kutchula chinthu chilichonse chogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Pa mfundo imeneyi, Baibulo limati: “Chilichonse chimene tingamupemphe [Mulungu] mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yohane 5:14) Kodi muyenera kutchulanso mavuto anu? Inde. Baibulo limati: “Mukhuthulireni [Mulungu] za mumtima mwanu.”—Salimo 62:8.
Zinthu zimene tingapemphe
Kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu.—Luka 17:5.
Kuti mzimu woyera, kapena kuti mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito, uzitithandiza kuchita zabwino.—Luka 11:13.
Kuti atipatse mphamvu zoti tithe kulimbana ndi mavuto athu komanso tipirire mayesero.—Afilipi 4:13.
Kuti atipatse mtendere wamumtima.—Afilipi 4:6, 7.
Kuti atipatse nzeru zotithandiza kuti tizitha kusankha bwino zochita.—Yakobo 1:5.
Kuti atipatse zinthu zofunikira pa moyo wa tsiku ndi tsiku.—Mateyu 6:11.
Kuti atikhululukire machimo athu.—Mateyu 6:12.