Pitani ku nkhani yake

Kodi Yesu Anali Munthu Wabwino Basi?

Kodi Yesu Anali Munthu Wabwino Basi?

Yankho la m’Baibulo

 Yesu sikuti anangokhala munthu wabwino basi. Ngakhale kuti anthu ena amamunyoza koma zimene iye ankachita ndiponso kulankhula zakhudza moyo wa anthu ambiri, kuposa zimene anthu ena otchuka ankachita komanso kunena. Taonani zimene akatswiri otchuka a mbiri yakale ananena zokhudza Yesu:

 “M’mbiri yonse ya anthu, sipanapezekepo munthu wotchuka kuposa Yesu wa ku Nazareti.”—H. G. Wells, katswiri wa mbiri yakale wa ku England.

 “Zochita za Yesu zakhudza anthu ambiri padzikoli kuposa munthu wina aliyense ndipo mpaka pano, anthu ambiri akukhudzidwabe ndi moyo wake.”—Kenneth Scott Latourette, katswiri wolemba mbiri yakale wa ku America.

 Baibulo limanena chifukwa chake zochita za Yesu zinakhudza moyo wa anthu ambiri kuposa zochita za anthu onse amene anakhalapo padzikoli, omwe angadziwike kuti ndi anthu abwino. Pamene Yesu anafunsa otsatira ake omwe ankayenda naye nthawi zonse kuti afotokoze maganizo awo pa nkhani yakuti iyeyo anali ndani, m’modzi mwa anthuwo anayankha molondola kuti: “Ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”—Mateyu 16:16.