Pitani ku nkhani yake

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Mmene Mano a Nkhono Ina Yam’madzi Anapangidwira

Mmene Mano a Nkhono Ina Yam’madzi Anapangidwira

Nkhono ina yam’madzi ya chigoba chozungulira, ili ndi mano a mphamvu kwambiri. Manowa amapangidwa ndi timaulusi ting’onoting’ono tothithikana tomwe timakhala tolimba kwambiri ngati mwala wotchedwa goethite.

 Taganizirani izi: Kukamwa kwa nkhonoyi kumakhala chinachake chooneka ngati lilime, chomwe chimakhala ndi timano tambiri topindika. Kutalika kwa dzino lililonse kumakhala kosakwana milimita imodzi. Koma dzino lililonse limafunika kukhala lolimba kwambiri kuti lizitha kupala ndere zomwe zakakamira pamiyala kuti nkhonozi zidye.

 Akatswiri ofufuza anagwiritsa ntchito makina a microscope amphamvu kwambiri pofufuza kulimba kwa mano a nkhonowa. Iwo anapeza kuti mano a nkhonoyi ndi olimba kwambiri kuposa a zamoyo zina zomwe anazifufuzapo. Ndipo ndi olimba kuposanso ulusi wa kangaude. Katswiri amene anatsogolera pochita kafukufuyu ananena kuti: “Tikuona kuti tikhoza kupanga zinthu zolimba potengera mmene mano a nkhono ya m’madziyi anapangidwira.”

 Akatswiriwa akufuna kugwiritsa ntchito zinthu zimene zimachititsa dzino la nkhonoyi kukhala lolimba popanga zinthu monga magalimoto, maboti, ndege ngakhalenso mano ochita kupanga.

 Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti mano a nkhonoyi apangidwe olimba kwambiri? Kapena pali winawake amene anawalenga?