Cikondi ca Mpeni Kumphasa
Cikondi ca Mpeni Kumphasa
Tiyelekezele kuti muli na mnzanu amene munadziŵana naye kuyambila muli mwana. Iye anali kukuthandizani kucita zinthu ngati munthu wamkulu komanso kuti muzigwilizana na anzanu ena. Mukakhala na nkhawa, munkangopita kwa iye kuti akuthandizeni ndipo munafika pomudalila pa zinthu zambili.
Koma patapita nthawi munazindikila kuti mnzanuyo si wabwino. Iye amakukakamilani kuti muziyenda naye kulikonse, ngakhale kumalo amene simungamasuke kupita naye. Ndipo ngakhale kuti nthawi zina munkaona kuti amakuthandizani kucita zinthu mocangamuka, iye wakuwonongelani thanzi lanu. Kuwonjezela pamenepo, iye wakhalanso akukubelani ndalama zanu.
M’zaka zaposacedwapa, mwakhala mukuyesetsa kuti musiye kuceza naye koma iye akukukakamilanibe. Inuyo mwafika pokhala kapolo wake ndipo mumadandaula kuti zinalakwika kudziŵana naye.
FODYA ali ngati bwenzi loteleli kwa anthu ambili amene amasuta. Mayi wina dzina lake Earline, yemwe anakhala akusuta fodya kwa zaka 50, ananena kuti: “N’nali kuona kuti kusuta fodya n’kothandiza kwambili. Fodya anafika pokhala ngati mnzanga wapamtima ndipo nthawi zambili nikasowa woceza naye n’nali kungoyamba kusuta.” Koma kenako Earline anazindikila kuti fodya ni woipa komanso woopsa kwambili. Akanapanda kusiya, bwenzi mawu oyambilila a nkhaniyi akunena za iyeyo. Iye anasiya atadziŵa kuti Mulungu sasangalala na anthu amene amasuta fodya, cifukwa fodya amawononga thupi limene Iye anatipatsa.—2 Akorinto 7:1.
Bambo wina dzina lake Frank anasiya kusuta n’colinga coti asangalatse Mulungu. Koma patangopita tsiku limodzi kucokela pamene anasiya, anapezeka kuti akukwawa m’nyumba mwake n’kumafufuza tindudu totsalila. Frank anati: “N’taona kuti nafika pomakwawa pansi n’kumatoleza tindudu ta fodya, ninadzimvela cisoni kwambili ndipo ninaganiza zosiyilatu kusuta fodya. Kucokela tsiku limenelo sininasutenso fodya.”
Kodi n’cifukwa ciani fodya amavuta kusiya? Akatswili ofufuza apeza kuti zinthu zotsatilazi n’zimene zimacititsa kuti anthu azivutika kusiya kusuta fodya: (1) Fodya amamulowelela munthu ngati mmene mankhwala osokoneza bongo amacitila. (2) Mu fodya muli mankhwala ochedwa nikotini omwe amafika ku ubongo m’masekondi 7 okha kucokela pamene munthu wasuta. (3) Munthu ukamasuta fodya thupi limazolowela monga mmene limacitila na kudya cakudya, kumwa, kulankhula, na zina zotelo.
Komabe, monga mmene zinalili na Earline ndiponso Frank, n’zotheka kusiya cizolowezi cimeneci. Ngati inuyo mumasuta ndipo mukufuna kusiya, nkhani yotsatilayi ikuthandizani kuti muyambe moyo watsopano.