Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nzelu Zotithandiza Kukhala na Banja Lacimwemwe

Nzelu Zotithandiza Kukhala na Banja Lacimwemwe

Cikwati komanso ana ni mphatso zamtengo wapatali zocokela kwa Mlengi wathu. Iye amafuna kuti tizikhala acimwemwe m’banja. Conco kupitila m’buku lakale lopatulika, watipatsa malangizo amene angatithandize kukhala na mabanja abwino komanso acimwemwe. Ganizilani malangizo anzelu otsatilawa.

Amuna, Muzikonda Akazi Anu

“Amuna akonde akazi awo monga matupi awo. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.” —AEFESO 5:28, 29.

Mwamuna ndiye mutu wa banja. (Aefeso 5:23) Koma mwamuna wabwino sakhala wankhanza kapena woumitsa zinthu. Amaona kuti mkazi wake ni wofunika, ndipo amam’samalila bwino mwakuthupi na kumuonetsa cikondi. Amacitanso zonse zotheka kuti am’kondweletse, osati nthawi zonse kuumilila pa kucita zofuna zake. (Afilipi 2:4) Amakambilana na mkazi wake momasuka, ndipo amamumvetsela akamakamba. ‘Samupsela mtima kwambili’ kapena kumumenya, ngakhale kumukambila mawu oipa.—Akolose 3:19.

Akazi, Muzilemekeza Amuna Anu

“Mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.”—AEFESO 5:33.

Ngati mkazi amalemekeza mwamuna wake na kucilikiza zisankho zake, m’banja mumakhala mtendele. Mwamuna akalakwitsa, iye samupeputsa. Koma amakhalabe wofatsa ndiponso waulemu. (1 Petulo 3:4) Mkazi akafuna kufotokoza vuto linalake kwa mwamuna wake, amasankha nthawi yabwino yocita zimenezo, ndipo amakamba naye mwaulemu.—Mlaliki 3:7.

Khalani Wokhulupilika kwa Mnzanu Wam’cikwati

‘Mwamuna. . . adzadziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.’—GENESIS 2:24.

Mwamuna na mkazi akakwatilana, amapanga mgwilizano wa banja wolimba kwambili. Conco mwamuna na mkazi ayenela kucita khama kuti cikwati cawo cikhalebe colimba. Angacite zimenezi mwa kukambilana mocokela pansi pa mtima na kucitilana zinthu zabwino. Ayenelanso kukhala okhulupilika kwa wina na mnzake mwa kupewa kugonana na munthu amene si mkazi kapena mwamuna wawo. Kusakhulupilika m’banja ni nkhanza. Kumapangitsa kuti okwatilana asamakhulupililane, ndipo kungathetse banja.—Aheberi 13:4.

Makolo, Phunzitsani Ana Anu

“Phunzitsa mwana m’njila yomuyenelela. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”—MIYAMBO 22:6.

Mulungu anapatsa makolo udindo wophunzitsa ana awo. Izi ziphatikizapo kuwaphunzitsa makhalidwe abwino, komanso kuwapatsa citsanzo cabwino. (Deuteronomo 6:6, 7) Mwana akacita zosayenela, kholo lanzelu silikalipa mopitilila malile. Ilo limakhala ‘lofulumila kumva, lodekha polankhula, losafulumila kukwiya.’ (Yakobo 1:19) Kholo likaona kuti m’pofunika kupeleka cilango kwa mwana, limacita zimenezo mwacikondi osati mwaukali.

Ana, Muzimvela Makolo Anu

“Ananu, muzimvela makolo anu . . . ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’” —AEFESO 6:1, 2.

Ana ayenela kumvela makolo awo na kuwalemekeza kwambili. Ngati ana amalemekeza makolo awo, m’banja mumakhala cimwemwe cacikulu, ndipo zimathandiza kuti mukhale mtendele na mgwilizano. Ana akulu-akulu amalemekeza makolo awo mwa kuonetsetsa kuti makolowo akusamalidwa bwino. Zimenezi zingaphatikizepo kuwathandiza kusamalila panyumba kapena kuwapatsa thandizo la ndalama.—1 Timoteyo 5:3, 4.