Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pezani Mabwenzi a Mitundu Yosiyana-siyana

Pezani Mabwenzi a Mitundu Yosiyana-siyana

Cifukwa Cake Zingakhale Zovuta

Ngati timapewa kupanga ubwenzi na ŵanthu amene timawaona ngati si abwino, tsankho lathu limakulila-kulila. Ndipo ngati tili na mabwenzi okha-okha amene amafanana na ife, tingayambe kuganiza kuti ife cabe ndiye timaganiza na kucita zinthu m’njila yoyenela.

Mfundo ya m’Baibo

“Futukulani mtima wanu.” —2 AKORINTO 6:13.

Kodi mfundo imeneyi itanthauza ciani? “Mtima” wathu ungatanthauze cikondi cimene tili naco. Ngati timakonda anthu okhawo amene amafanana na ife, cikondi cathu cimacepa. Kuti tipewe vuto limeneli, tifunika kukhala okonzeka kupanga ubwenzi na ŵanthu amene ni osiyana na ife.

Kodi kupeza mabwenzi a mitundu yosiyana-siyana kumathandiza bwanji?

Anthu tikawadziŵa bwino, timayamba kumvetsa cifukwa cake amacita zinthu mosiyana na mmene ife timacitila. Ndipo tikayamba kuwakonda, timaona kuti iwo na ife ndife amodzi. Timayamba kuwakonda kwambili na kuwamvelela cifundo.

Ganizilani citsanzo ca Nazaré. Poyamba iye anali kuona kuti anthu ocokela ku maiko ena si abwino. Iye anafotokoza cimene cinam’thandiza. Anati: “N’nali kuceza nawo na kuseŵenza nawo. N’nakumana na ŵanthu amene ena anali kuwanenela zoipa. Koma zimene n’napeza zinali zosiyana kwambili na zimene n’namvela. Ukapanga ubwenzi na ŵanthu acikhalidwe cina, umathetsa maganizo a tsankho amene unali nawo pa iwo, ndipo umayamba kuwakonda na kuona aliyense wa iwo kukhala wofunika.”

Zimene Mungacite

Sakilani mipata yokamba na ŵanthu ocokela ku maiko ena, a mtundu wina, kapena okamba citundu cosiyana na canu. Mungacite izi:

  • Mungawapemphe kuti akuuzenkoni zina zokhudza umoyo wawo.

  • Mungawapemphe kuti akadye namwe cakudya.

  • Mvetselani mwachelu pamene akamba zokhudza umoyo wawo. Yesetsani kudziŵa zimene amaona kuti n’zofunika kwambili pa umoyo wawo.

Mukadziŵa zimene iwo akumana nazo pa umoyo na mmene zakhudzila khalidwe lawo, mungayambe kuwaona moyenela anthu amenewo komanso ena a mtundu wawo.