Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Tsogolo Lanu Limadalila Ciani Maka-maka?

Kodi Tsogolo Lanu Limadalila Ciani Maka-maka?

Ambili amakhulupilila kuti pali mphamvu inayake yosaoneka imene imalamulila zocitika pa umoyo wawo. Cifukwa cokhulupilila zimenezi, amacita zinthu zosiyanasiyana zimene amaganiza kuti zingawathandize kukhalako na tsogolo labwino.

ZIMENE AMBILI AMAKHULUPILILA

KUPENDA NYENYEZI: Anthu ena amakhulupilila kuti tsogolo lawo linalinganizidwa kale, ndipo limadalila mmene nyenyezi zinali kuonekela kumwamba panthawi imene anali kubadwa. Conco, amafunsila kwa openda nyenyezi kapena kuyang’ana pa chati yopendela nyenyezi kuti adziŵe zimene zidzawacitikila kutsogolo. Kenako amacitapo kanthu kuti apewe mavuto kapena kuti zinthu ziwayendele bwino.

CIKHULUPILILO COCHEDWA FENG SHUI: Anthu ena amakhulupilila kuti ngati amanga nyumba kapena kuika zinthu mwanjila inayake pa nyumbapo, ndiye kuti zinthu zingawayendele bwino. Lo Wing, * amene amakhala ku Hong Kong anati, “Katswili wina wa feng shui ananiuza kuti, kuika kamwala kapadela konyezimila pamalo enaake m’shopu yanga kunganithandize kupeza ndalama zambili.”

KULAMBILA MIZIMU YA MAKOLO: Palinso anthu ena amene amakhulupilila kuti ayenela kulemekeza makolo awo akufa kapena milungu, kuti apeze citetezo na madalitso. Van, amene amakhala ku Vietnam anati, “N’nali kukhulupilila kuti nikamalambila mizimu ya makolo anga, ningakhale na umoyo wabwino palipano. Ndipo tsogolo langa komanso la ana anga lidzakhala lowala.”

KUBADWANSO CINTHU CINA KAPENA MUNTHU WINA: Ambili amakhulupilila kuti munthu akafa amakabadwanso cinthu cina kapena munthu wina, ndipo zimenezi zimacitika mobweleza-bweleza. Amakhulupilila kuti zabwino kapena zoipa zimene amakumana nazo masiku ano zimawacitikila cifukwa ca zimene anacita mu umoyo wawo wakale.

Komabe, anthu ambili amakhulupilila kuti zimenezi ni zikhulupililo zabodza. Ngakhale n’telo, amacitabe zinthu monga kupenda zikhatho, kupenda nyenyezi, kuwombeza, na zina zaconco. Amacita izi poganiza kuti mwina zingawathandize kudziŵa za tsogolo lawo.

KODI ZOTULUKAPO ZAKE ZAKHALA ZOTANI?

Kodi anthu amene amadalila zikhulupililo zimenezi na miyambo yake amakhala na umoyo wabwino kapena tsogolo labwino?

Ganizilani zimene zinacitikila Hào, wa ku Vietnam. Pofuna kuti zinthu zimuyendele bwino, iye anali kupenda nyenyezi, kukhulupilila feng shui, na kulambila mizimu ya makolo. Kodi kucita zimenezi kunamuthandiza? Hào anati, “Bizinesi yanga inaloŵa pansi, n’nagwa m’nkhongole, tinali kungokangana m’banja, ndipo n’nali na nkhawa kwambili.”

Nayenso Qiuming wa ku Taiwan anali kupenda nyenyezi, kukhulupilila za kubadwanso kukhala cinthu cina, komanso zakuti zocitika zonse mu umoyo wathu zinalinganizidwilatu. Iye anali kukhulupililanso feng shui, na kulambila mizimu ya makolo akale. Koma pambuyo popenda mosamala zikhulupililo zimenezi, Qiuming anati: “N’nazindikila kuti ziphunzitso zimenezi na miyambo yake zimatsutsana komanso n’zosokoneza. N’naonanso kuti zimene n’nali kupeza nikapenda nyenyezi, nthawi zambili sizinali zolondola. Nimaonanso kuti cikhulupililo cakuti munthu akafa amakabadwanso kukhala cinthu cina n’cosathandiza. Cifukwa ngati munthu sukumbukila ciliconse cokhudza umoyo wako wakale, ungadziŵe bwanji zoyenela kusintha kuti ukacite bwino mu umoyo wakutsogolo?”

“N’nazindikila kuti ziphunzitso zimenezi na miyambo yake zimatsutsana komanso n’zosokoneza.”—QIUMING, TAIWAN

Monga mmene Hào, Qiuming, na ena ambili aonela, tsogolo lathu silinalinganizidwiletu. Silidalila pa nyenyezi, makolo akale amene anamwalila, kapena pa kubadwanso kukhala cinthu cina. Kodi izi zitanthauza kuti basi palibe cimene tingacite kuti tikhale na tsogolo labwino?

Ambili amaona kuti njila yabwino yokhalila na tsogolo labwino ni kuyesetsa kucita maphunzilo apamwamba na kukhala na cuma. Koma kodi anthu ena amene anasankha kucita zimenezi zinthu zinawayendela bwanji?

^ ndime 5 M’nkhani ino na zotsatila, maina ena asinthidwa.

^ ndime 16 Mawu amenewa apezeka m’Buku Lopatulika pa Agalatiya 6:7. Mfundo ya pa lembali ilingana na mwambi wina wochuka wa ku Asia wakuti, Ukabzala mavwembe udzakolola mavwembe, ukabzala nyemba, udzakolola nyemba.