Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Baibulo Imakamba Ciani?

Kodi Baibulo Imakamba Ciani?

Kodi anayambitsa cipembedzo ni anthu?

ANTHU ENA AMAKHULUPILILA kuti cipembedzo ni nkhani cabe ya anthu. Koma ena amaganiza kuti Mulungu amaseŵenzetsa cipembedzo kuti athandize anthu kukhala naye pa ubwenzi. Nanga inu muganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

Pali “kupembedza koyela ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu.” (Yakobo 1:27) Mulungu ni amene anayambitsa kulambila koyela kapena kuti koona.

ZINTHU ZINA ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

  • Mulungu amakondwela ndi cipembedzo cimene cimatsatila mfundo zoona za m’Baibulo.—Yohane 4:23, 24.

  • Zipembedzo zimene zimatsatila maganizo a anthu n’zopanda phindu.—Maliko 7:7, 8.

Kodi kukhala m’cipembedzo kuli ndi phindu?

MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Inde

  • Iyai

  • Nthawi zina

ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

“Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi.” (Aheberi 10:24, 25) Mulungu amafuna kuti anthu amene amamulambila azisonkhana monga gulu.

ZINTHU ZINA ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

  • Amene amalambila Mulungu afunika kukhulupilila zinthu zofanana.—1 Akorinto 1:10, 11.

  • Amene ali m’cipembedzo ca zoona amakhala okondana ndi ogwilizana monga gulu la abale la padziko lonse.—1 Petulo 2:17

Nditumizileni buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse