NSANJA YA MLONDA Na. 6 2016 | Masomphenya a Zinthu za Kumwamba

Dziŵani zinthu za kumwamba mwa kuŵelenga Baibo.

NKHANI YA PACIKUTO

N’ndani Amene Akhala Kumwamba

N’zotheka kupeza mayankho okhutilitsa.

NKHANI YA PACIKUTO

Masomphenya Oonetsa Amene Ali Kumwamba

Kodi Malemba amatiuza ciani za Yehova Mulungu, Yesu Khiristu, ndi angelo okhulupilika?

Phunzilani ku Mbalame za M’mlenga-lenga

Mbalame zimaonetsa luso limene Mulungu ali nalo polenga zinthu ndiponso zimatilimbikitsa kuika maganizo athu pa zinthu zofunika kwambili.

Lefèvre d’Étaples—Anafuna Kuti Anthu Wamba Adziŵe Mau a Mulungu

Anakwanilitsa bwanji colinga cake ngakhale kuti anali kutsutsidwa?

MBILI YANGA

N’nalandila Coonadi Olo Kuti Nilibe Manja

Mwamuna wacita ngozi yoopsa, komabe wadziŵa cifukwa cake afunika kukhulupilila Mlengi.

Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Kodi Mulungu amamvela na kuyankha mapemphelo anu?