Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi apolisi aciyuda a pa kacisi anali ndani? Nanga anali kugwila nchito yanji?

Alevi amene sanali ansembe anali kugwila nchito zina zosiyana-siyana. Imodzi mwa nchito zawo inali yotumikila monga apolisi. Iwo anali kuyang’anilidwa na woyang’anila kacisi. Pofotokoza nchito zina zimene apolisiwa anali kucita, wolemba nkhani wina waciyunda, dzina lake Philo anati: “Ena mwa [Alevi] amenewa, amatumikila monga alonda a pageti. Amaimilila pageti peni-peni poloŵela. Enanso amaimilila mkati [m’bwalo la kacisi] kutsogolo kwa malo opatulika, kuti aziletsa anthu osayenelela kulowa m’malo opatulikawo, kaya mwadala kapena mosadziŵa. Ena amayenda-yenda kuzungulila kacisi kuti aziulondela mosinthana-sinthana, usana na usiku.”

Nthawi zina, Khoti Lalikulu la Ayuda linali kupempha gulu limeneli la apolisi kuti liwacitile zimene afuna. Ndipo apolisi amenewa ndiwo okha cabe amene anali ovomelezedwa na boma la Aroma kunyamula zida.

Malinga na zimene katswili wina wa Baibo, dzina lake Joachim Jeremias anakamba, ‘Mawu odzudzula amene Yesu anakamba pa nthawi imene anagwidwa, akuti n’cifukwa ciani sanamugwile ngakhale kuti tsiku na tsiku anali kuphunzitsa mu Kacisi (Mat. 26:55), aonetselatu kuti amene anabwela kudzamugwila anali apolisi a pa Kacisi.’ Katswiliyo anali kukhulupilila kuti alonda amene anatumidwa kuti akagwile Yesu pa nthawi ina m’mbuyomo, analinso apolisi a pa kacisi. (Yoh. 7:32, 45, 46) Patapita nthawi, apolisi a pa kacisi pamodzi na woyang’anila wawo anatumidwa kuti akagwile ophunzila a Yesu na kuwatengela ku Khoti Lalikulu la Ayuda. Komanso n’zoonekelatu kuti apolisi amenewa ni amenenso anagwila mtumwi Paulo na kum’kokela kunja kwa kacisi.—Mac. 4:1-3; 5:17-27; 21:27-30.