Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZA M’NKHOKWE YATHU

Nchito Inali Kuyenda Bwino M’kafiteliya Cifukwa ca Cikondi

Nchito Inali Kuyenda Bwino M’kafiteliya Cifukwa ca Cikondi

NTHAWI zonse timasangalala kukhala pamodzi pamisonkhano ndi kuphunzitsidwa ndi Yehova. Anthu a Mulungu akakumana pamodzi kuti aphunzitsidwe amasangalalanso kwambili kudya cakudya cakuthupi pamodzi.

Mu September 1919, Ophunzila Baibulo anacita msonkhano wa masiku 8 ku Cedar Point, Ohio, m’dziko la U.S.A. Alendo anafunika kudya ndi kugona ku mahotela, koma kunafika alendo ambili kuposa amene anali kuyembekezela. Poona kuculuka kwa anthu amene anabwela, opeleka cakudya mu hotela ina onse anasiya nchito nthawi imodzi. Woyang’anila hotela atasowa cocita anapempha alendowo ngati acinyamata angazipeleke kugwila nchito mu hotelayo, ndipo acinyamata ambili anadzipeleka mofunitsitsa. Sadie Green anali mmodzi wa odzipelekawo. Iye anati: “Inali nthawi yanga yoyamba kugwila nchito yopelekela cakudya, koma tinasangalala.”

Ku Sierra Leone, mu 1982

Zaka zotsatilapo, panapangidwa makonzedwe akuti pamisonkhano yacigawo pazikhala kafiteliya. Makonzedwe amenewo anacititsa kuti anchito odzifunila azisangalala kutumikila abale ndi alongo ao. Kugwila nchito pamodzi monga Akristu kunathandiza acicepele ambili kukhala ndi zolinga za kuuzimu. Gladys Bolton, amene anatumikila mu kafiteliya pa msonkhano wa mu 1937, anati: “Ndinakumana ndi anthu ocokela m’madela osiyanasiyana ndi kumva mmene anali kulimbanilana ndi mavuto. Zimenezi zinandithandiza kuti ndikhale ndi maganizo oyamba upainiya wa nthawi zonse”.

M’modzi wa opezeka pa msonkhano dzina lake Beulah Covey anati: “Anchito odzifunila amene amagwila nchito modzipeleka amathandiza kuti zinthu ziyende bwino.” Ngakhale n’conco panali zina zovuta. Mu 1969, M’bale wina dzina lake Angelo Manera atafika ku msonkhano ku Dodger Stadium mumzinda wa Los Angeles, ku California, anauzidwa kuti waikidwa kukhala mtumiki wa kafiteliya. Iye anati: “Zimenezo zinandidzidzimutsa kwambili.” Pokonzekela msonkhanowo, panafunika kukumbidwa mfolo wa mamita 400 kuti mupite mapaipi a gasi opita ku khicheni.

Ku Frankfurt, m’dziko la Germany, mu 1951

Mu 1982, m’dziko la Sierra Leone, abale odzipeleka anagwila nchito mwakhama. Iwo anakonza malo ndi kumangapo kafiteliya pogwilitsila nchito zipangizo zimene anali nazo. Ku Frankfurt, m’dziko la Germany m’caka ca 1951, abale akhama anacita lendi makina ena ake ndi kuwagwilitsa nchito kutenthetsa maketulo 40 ophikila. Zimenezi zinathandiza kuti abale azitha kuphika zakudya zokwanila anthu 30,000 pa ola limodzi. Pofuna kucepetsa nchito ya anthu okwana 576 amene anali kutsuka mbale, anthu obwela ku msonkhano anali kunyamula mipeni ndi mafoloko ao. Ku Yangon m’dziko la Myanmar, ophika anali kucita zinthu moganizila ena. Iwo anali kuika mphilipili yocepa m’zakudya za alendo ocoka m’maiko ena.

“AKUDYA COIMILILA”

Pamsonkhano wina mu 1950 m’dziko la United States, mlongo Annie Poggensee anapindula kwambili pamene anaimilila pa mzele kwa nthawi yaitali ngakhale kuti kunali kotentha. Iye anati: “Ndinasangalala kumvetsela makambilano olimbikitsa a alongo aŵili amene anayenda ulendo wa pa boti kucokela ku Europe.” Iwo anali kukambilana mmene Yehova anawathandizila kuti afike pamsonkhanowo. Annie anapitiliza kuti: “Alongowo anali osangalala kwambili pamsonkhanopo. Kutalika kwa nthawi imene tinakhala pamzele ndi kutentha kwa dzuŵa zinalibe kanthu kwa io.”

Ku Seoul, m’dziko la Korea, mu 1963

Pamisonkhano yacigawo, m’matenti a kafiteliya anali kuikamo mathebulo akuluakulu aatali. Anthu anali kuimilila pamenepo ndi kudya msangamsanga kuti asiyile ena malo. Zimenezo zinathandiza kuti anthu masauzande ambili athe kudya cakudya pa nthawi yopuma. Munthu wina yemwe sanali Mboni anati: “Ha! Koma ici ndi cipembedzo cacilendo. Anthu akudya coimilila.”

Akuluakulu a asilikali ndi a boma anadabwa ndi mgwilizano umene anaona pamsonkhano. Mmodzi wa akuluakulu a asilikali ku United States atayendela kafiteliya yathu ku Yankee Stadium mumzinda wa New York, analimbikitsa Faulkner, mkulu wa Dipatimenti ya nkhondo ya dziko la Britain kuti nayenso akayendele kafiteliya yathu. Conco, Faulkner ndi mkazi wake anapita ku msonkhano umene unacitikila ku Twickenham, m’dziko la England m’caka ca 1955. Msonkhano umenewo unali wa mutu wakuti “Ufumu Wolakika.” Iye ananena kuti nchito inali kuyenda bwino m’kafiteliya cifukwa ca cikondi.

Kwa zaka zambili, anchito odzifunila anali kuphikila anthu obwela ku misonkhano yacigawo cakudya copatsa thanzi koma osati capamwamba kwambili. Komabe, cifukwa ca kukula kwa nchito panali kufunika anchito ambili ndiponso anafunika kugwila nchitoyi maola ambili. Izi zinacititsa kuti iwo asamamvetsele mapulogilamu pamisonkhano. Pofika kumapeto kwa zaka za m’ma 1970, m’madela ambili, nchito yophika cakudya pamisonkhano inapeputsidwa. Ndipo mu 1995, anthu obwela ku msonkhano anauzidwa kuti azinyamula zakudya zao. Zimenezi zinathandiza kuti anthu amene anali kuphika ndi kupelekela cakudya azimvetsela mapulogilamu ndi kusangalala ndi maceza olimbikitsa. *

Yehova amayamikila kwambili onse amene anadzipeleka kutumikila okhulupilila anzao. Ena amakumbukila ndi kulakalaka nthawi imene anali kugwila nchito mu kafiteliya. Koma cokondweletsa n’cakuti: Cikondi cikali kuonekela kwambili pamisonkhano yathu.—Yoh. 13:34, 35.

^ par. 12 Ngakhale n’conco, mwai ukalipo wakuti anthu azidzipeleka kugwila nchito m’madipatimenti ena pamisonkhano.