Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NHANI YA PACIKUTO

Anthu Kulikonse Ali Ndi Nkhawa

Anthu Kulikonse Ali Ndi Nkhawa

“Ndinapita kukagula zakudya koma ndinangopeza mabisiketi. Komabe, anali odula kuwilikiza ka 10,000 pamtengo wake weniweni. Tsiku lotsatila m’masitolo onse munalibe cakudya ciliconse.”—Paul, wa ku Zimbabwe.

“Mwamuna wanga anandiuza kuti akucoka panyumba. Zimenezi zinandidetsa nkhawa. Ndinali kudzifunsa kuti, ndidzasunga bwanji ana anga aŵili?”—Janet, wa ku United States.

“Nditamva mabelu ocenjeza, ndinapita kukabisala ndipo ndinagona pansi apo n’kuti mabomba akuphulika. Komabe, patapita maola angapo, ndinayamba kunjenjemela ndi mantha.”—Alona, wa ku Israel.

Tikukhala m’nthawi “yapadela komanso yovuta,” pamene anthu ambili ali ndi nkhawa zoculuka. (2 Timoteyo 3:1) Ambili akukumana ndi mavuto a zacuma, kutha kwa mabanja, nkhondo, matenda oopsa amene afala, ndi ngozi zacilengedwe kapena zimene zimacitika cifukwa ca zocita za anthu. Kuonjezela apo, anthu ena amakhala ndi nkhawa zaumwini ndipo amadzifunsa kuti, ‘Kodi ndidzakhala ndi khansa ya pakhungu?’ ‘Nanga zinthu zidzakhala bwanji adzukulu anga akakula?’

N’zoona kuti nkhawa zonse si zoipa. Mwacibadwa, timada nkhawa tikafuna kucita zinthu zina monga poyamba kulemba mayeso, pofunsidwa mafunso oloŵela nchito, ndi poyembekeza zotulukapo zake. Komanso kuopa zinthu zina kumatithandiza kupewa ngozi. Komabe, kukhala ndi nkhawa zopitilila muyeso kungatibweletsele mavuto. Kafukufuku wina wa posacedwapa amene anacitika pakati pa anthu oposa 68,000, anaonetsa kuti ngakhale nkhawa yaing’ono ingacititse munthu kufa msanga. Pofuna kutithandiza, Yesu anafunsa kuti: “Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?” Kukamba zoona, nkhawa sizingatalikitse moyo wa munthu. Conco, Yesu anatilangiza kuti: “Lekani kudela nkhawa.” (Mateyu 6:25, 27) Koma, kodi tingacite ciani kuti tileke kuda nkhawa?

Kuti zimenezi zitheke, tifunika kugwilitsila nchito nzelu zothandiza, kukhulupilila Mulungu, ndi kukhala ndi ciyembekezo ceniceni ca mtsogolo. Ngakhale tilibe mavuto palipano, tidzakumanabe nao mtsogolo. Conco, tiyeni tione mmene njila zimenezi zathandizila Paul, Janet, ndi Alona kulimbana ndi nkhawa.