Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Kodi zidzatheka kuti padziko lapansi pakhale cilungamo ceni-ceni?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Iyai

  • Kapena

Zimene Baibo imakamba

“Ndikudziŵa bwino kwambili kuti Yehova adzazengela mlandu anthu osautsika. Iye adzacitila cilungamo anthu osauka.” (Salimo 140:12) Ufumu wa Mulungu udzabweletsadi cilungamo ceni-ceni padziko lapansi.

Mfundo zina zimene Baibo imakamba

  • Mulungu amaona zinthu zopanda cilungamo zimene zikucitika, ndipo adzazithetsa.—Mlaliki 5:8.

  • Cilungamo ca Mulungu cidzabweletsa mtendele na citetezo padziko lapansi.—Yesaya 32:16-18.

Kodi Mulungu amakondela?

Ena amakhulupilila kuti Mulungu amadalitsa na kutembelela anthu ena. Ena amakhulupilila kuti Mulungu amaona anthu onse cimodzi-modzi. Nanga imwe muganiza bwanji?

Zimene Baibo imakamba

“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Mulungu amaona anthu onse cimodzi-modzi.

Mfundo zina zimene Baibo imakamba

  • Baibo ili na “uthenga wabwino” wopita “kudziko lililonse, fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse.”—Chivumbulutso 14:6.