Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 69

Patsogolo na Ulaliki wa Ufumu!

Patsogolo na Ulaliki wa Ufumu!

(2 Timoteyo 4:5)

  1. 1. Pitani, kalalikileni

    Kwa amitundu yonse.

    Na mtima wokonda anansi,

    Thandizani ofatsa.

    Ni mwayi wathu kulengeza

    Za Ufumu wa Yehova.

    Mokondwa tiphunzitsa ena,

    Za dzina lake loyela.

    (KOLASI)

    Lalikani uthenga wa Ufumu

    konse konse.

    Khalanibe okhulupilika

    kwa M’lungu wathu.

  2. 2. Capamodzi titumikile

    Yehova, ‘tate wathu.

    Odzozedwa na nkhosa zina,

    Tiphunzitse co’nadi.

    Onse tiŵauze uthenga,

    Wa Ufumu wa Yehova.

    Tilengeza molimba mtima

    Timadalila Yehova.

    (KOLASI)

    Lalikani uthenga wa Ufumu

    konse konse.

    Khalanibe okhulupilika

    kwa M’lungu wathu.

(Onaninso Sal. 23:4; Mac. 4:29, 31; 1 Pet. 2:21.)