Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 78

Phunzitsani Mau a Mulungu

Phunzitsani Mau a Mulungu

(Machitidwe 18:11)

  1. 1. Timakonda kuphunzitsa

    Anthu za Yehova.

    Madalitso timapeza

    Ni osaneneka.

    Tiphunzitse mwa cikondi

    Monga Yesu Khristu

    Kuti anthu onse

    Ayandikile kwa Yehova.

  2. 2. Tiziyesetsa mwakhama

    Kucita zabwino,

    Kuti onse otiona

    Amvele uthenga.

    Zimene taphunzitsidwa

    Tiphunzitse ena.

    Tidzakhala acimwemwe

    Tikaphunzitsa ena.

  3. 3. M’lungu adzatithandiza

    Pophunzitsa anthu.

    Tikapemphela kwa iye,

    Adzatithandiza.

    Tikonde onse amene

    Tiphunzila nawo.

    Posacedwa nawonso

    Adzapita patsogolo.

(Onaninso Sal. 119:97; 2 Tim. 4:2; Tito 2:7; 1 Yoh. 5:14.)