Onani zimene zilipo

Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupilila Kuti Cipembedzo Cao Ndico Cokha Coona?

Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupilila Kuti Cipembedzo Cao Ndico Cokha Coona?

Normal;Anthu amene amakonda kwambili zacipembedzo ayenela kukhulupilila kuti Mulungu ndi Yesu amavomeleza cipembedzo cao. Ngati sakhulupilila zimenezo, kungakhale kungotaya nthawi kukhala m’cipembedzo cimeneco.

Yesu sanavomeleze zimene anthu amakamba kuti pali zipembedzo zambili kapena miseu yambili imene imatsogolela ku cipulumutso. M’malo mwake, iye anati: “Cipata coloŵela ku moyo n’copapatiza komanso mseu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi oŵelengeka.” (Mateyu 7:14) A Mboni za Yehova amakhulupilila kuti anapeza mseu wakumoyo umenewu. Iwo akanapanda kukhulupilila, akanaloŵa cipembedzo cina.