Onani zimene zilipo

Kodi Mboni za Yehova ndi Gulu Lampatuko la ku America?

Kodi Mboni za Yehova ndi Gulu Lampatuko la ku America?

N’zoona kuti likulu lathu la padziko lonse lili ku America. Koma sindife gulu lampatuko la ku America pa zifukwa zotsatilazi:

  • Mau akuti mpatuko angatanthauze kupatuka kucoka m’gulu lina. Koma Mboni za Yehova sizinacoke m’cipembedzo cina. M’malo mwake timakhulupilila kuti tikutsatila njila ya kalambilidwe imene Akristu a m’nthawi ya atumwi anali kutsatila.

  • Mboni za Yehova ndi zacangu pa nchito yao yolalikila ndipo zili m’maiko oposa 230. M’dziko lililonse limene timakhala timaona kuti cofunika kwambili ndi kumvela Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu osati boma la America kapena boma lina lililonse la anthu.—Yohane 15:19; 17:15, 16.

  • Ziphunzitso zathu zonse ndi zocokela m’Baibulo osati m’mabuku olembedwa ndi mtsogoleli winawake wa ku America.?—1 Atesalonika 2:13.

  • Timatsatila Yesu Kristu osati mtsogoleli wina aliyense pano padziko lapansi.?—Mateyu 23:8-10.