Onani zimene zilipo

Kukaona Malo pa Beteli

Tikuitanani kuti mudzaone maofesi athu a nthambi, amene timayacha kuti Beteli. Maofesi ena a nthambi ali na ma miziyamu yakuti munthu akhoza kudzionela yekha zinthu popanda wina kumutsogolela.

Kuyambilanso Kukayendela Maofesi a Nthambi: Pa June 1, 2023, m'maiko ambili tinayambilanso kulola anthu kukayendela maofesi athu a nthambi. Kuti mumve zambili, funsilani ku ofesi ya nthambi imene mufuna kukayendela. Koma conde, osapitako ngati munapezeka na COVID-19, ngati muli na cimfine, kapena ngati caposacedwa munakhalako pafupi na munthu wodwala COVID-19.

Germany

Jehovas Zeugen

Am Steinfels 1

65618 SELTERS

GERMANY

+49 6483-41-0

Kuona Malo

Pa Mande mpaka pa Cisanu

8:00hrs mpaka 11:00hrs ndi 13:00hrs mpaka 16:00hrs.

Nthawi yoona malo: Maola aŵili

Zimene Timacita

Ofesi ya nthambi ku Selters, m’dziko la Germany imayang’anila nchito yolalikila m’dzikoli ndi m’maiko a Austria, Liechtenstein, Luxembourg, ndi Switzerland amene ali m’cigawo ca pakati ku Ulaya. Poona malo mudzaonanso zinthu zina zokhudza mbili ya Mboni za Yehova m’maiko amenewa. Ndiponso timasindikiza ndi kutumiza mabuku ku mipingo yoposa 16,000 m’maiko 51.

Tengani kapepala koonetsa malo.