Onani zimene zilipo

Kodi Chimo N’ciyani?

Kodi Chimo N’ciyani?

Yankho la m’Baibo

 Chimo ni kucita cinthu ciliconse cimene Mulungu amadana naco, kapena kuciganizila. Liphatikizapo kuphwanya mfundo kapena malamulo a Mulungu. (1 Yohane 3:4; 5:17) Koma Baibo imakambanso kuti munthu amacimwa akalephela kucita zinthu zoyenela.—Yakobo 4:17.

 M’zinenelo zoyambilila zimene anaseŵenzetsa polemba Baibo, mawu akuti chimo amatanthauza “kuphonya.” Mwacitsanzo, ku Isiraeli wakale kunali asilikali amene anali kuti akaponya mwala na gulaye, “sanali kuphonya.” Ngati mawuwa atamasulidwa mmene analili m’cinenelo coyamba, angalembedwe kuti “sanali kucimwa.” (Oweruza 20:16) Conco, chimo limatanthauza kulakwitsa kapena kuti kulephela kucita zimene Mulungu amafuna.

 Popeza Mulungu ndiye anatilenga, ni woyenela kutipatsa mfundo zoyenela kutsatila. (Chivumbulutso 4:11) Conco, ngati timacita zinthu zolakwika, tidzayankha mlandu kwa Mulungu.—Aroma 14:12.

Kodi n’zotheka kupewelatu kucita macimo?

 Ayi. Baibo imati: “Onse ndi ocimwa ndipo ndi opelewela pa ulemelelo wa Mulungu.” (Aroma 3:23; 1 Mafumu 8:46; Mlaliki 7:20; 1 Yohane 1:8) N’cifukwa ciyani zili conco?

 Anthu oyamba, , Adamu na Hava, anali angwilo. Sanali kucimwa cifukwa analengedwa m’cifanizilo ca Mulungu. (Genesis 1:27) Koma kenako, iwo anakhala opanda ungwilo cifukwa sanamvele Mulungu. (Genesis 3:5, 6, 17-19) Conco, atayamba kubeleka ana, anawapatsilako ucimowo na kupanda ungwilo. (Aroma 5:12) N’cifukwa cake Mfumu Davide ya Isiraeli inati: “[Ndinabadwa] ndili wocimwa.”—Salimo 51:5.

Kodi macimo ena ni aakulu kuposa ena?

 Inde. Mwacitsanzo, Baibo imati anthu a ku Sodomu anali “oipa, ndipo anali ocimwa kwambili” komanso ‘chimo lawo linali lalikulu kwambili.’ (Genesis 13:13; 18:20) Tiyeni tione mfundo zitatu zimene zingatithandize kudziŵa kuti chimo ili ni lalikulu.

  1.   Mtundu wake. Baibo imaticenjeza kuti tipewe macimo aakulu monga ciwelewele, kulambila mafano, kuba, kuledzela, kupha munthu, komanso kukhulupilila mizimu. (1 Akorinto 6:9-11; Chivumbulutso 21:8) Baibo imasiyanitsa macimowa na machimo ena amene munthu amacita mosazindikila monga kulankhula kapena kucita zinthu zokhumudwitsa ena. (Miyambo 12:18; Aefeso 4:31, 32) Koma Baibo imatilimbikitsa kuti tisamaone chimo lililonse kukhala laling’ono, cifukwa zingapangitse kuti tiyambe kucita macimo aakulu.—Mateyu 5:27, 28.

  2.   Colinga. Anthu ena amacita macimo cifukwa sadziŵa zimene Mulungu amafuna. (Machitidwe 17:30; 1 Timoteyo 1:13) Baibo silicepetsa macimo amenewa, koma limangowasiyanitsa na macimo amene anthu ena amacita mwadala mwa kuphwanya malamulo a Mulungu. (Numeri 15:30, 31) Macimo a mwadala amacokela mu ‘mtima woipa.’—Yeremiya 16:12.

  3.   Kucita mobweleza-bweleza. Baibo imasiyanitsanso munthu amene wacita chimo kamodzi kokha, na munthu amene amacita mobweleza-bweleza. (1 Yohane 3:4-8) Mulungu adzaweluza anthu amene amacita “macimo mwadala” ngakhale pambuyo podziŵa zolondola.—Aheberi 10:26, 27.

 Anthu amene anacita macimo aakulu akhoza kumva cisoni kwambili na zimene anacitazo. Mwacitsanzo, Mfumu Davide anati: “Zolakwa zanga zakwela kupitilila mutu wanga. Zandilemela kwambili ngati katundu wolemela.” (Salimo 38:4) Komabe, Baibo imati: “Munthu woipa asiye njila yake ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake. Iye abwelele kwa Yehova ndipo adzamucitila cifundo. Abwelele kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.”—Yesaya 55:7.