Onani zimene zilipo

Kodi Sayansi Imagwilizana na Baibo?

Kodi Sayansi Imagwilizana na Baibo?

Yankho la m’Baibo

 Inde. Ngakhale kuti Baibo si buku la sayansi, ikachula nkhani zokhudza sayansi imakamba zoona. Onani zitsanzo zoonetsa kuti Baibo igwilizana na sayansi, komanso kuti ili na mfundo zolondola zokhudza sayansi ngakhale kuti anthu ambili pa nthawi imene inali inalembedwa anali kukhulupilila zosiyana kwambili.

  •   Cilengedwe conse cili na ciyambi. (Genesis 1:1) Mosiyana na zimenezi, anthu kale anali kukhulupilila kuti cilengedwe sicinacite kulengedwa koma cinangokhalako kucokela ku msokonezo winawake. Ababulo anali kukhulupilila kuti milungu imene inabeleka cilengedwe inacokela ku nyanja ziŵili za mcele. Nthano zina zakale zimaonetsa kuti cilengedwe cinacokela ku dzila lina lalikulu.

  •   Cilengedwe conse cimatsatila malamulo a m’cilengedwe, osati motsatila malamulo a milungu ina. (Yobu 38:33; Yeremiya 33:25) Anthu m’dzikoli amaphunzitsa mabodza akuti anthu sangadziteteze kuzocita zoipa za milungu ya bodza.

  •   Dziko lapansi ili m’malele. (Yobu 26:7) Anthu kale anali kukhulupilila kuti dziko niyobwatalala, ndipo imacilikizidwa na nyama yaikulu monga njati, kapena fulu.

  •   Madzi amene ali m’mtsinje amacokela ku madzi a m’nyanja amene akacita nthunzi n’kukwela kumwamba, amagwa monga mvula, sinoo, kapena matalala. (Yobu 36:27, 28; Mlaliki 1:7; Yesaya 55:10; Amosi 9:6) Agiliki akale anali kukhulupilila kuti madzi amene ali m’mtsinje amacokela pansi panyanja zina, ndipo anali kukhulupilila zimenezi mpaka zaka za m’ma 1700.

  •   Mapili amatha kuphulika kucokela pansi pa nthaka. Ndipo mapili amene alipo panopa anali pansi panyanja. (Salimo 104:6, 8) Mosiyana na zimenezi, nthano zambili zimati mapili anacita kupangidwa na milungu kukhala mmene alilimo.

  •   Kukhala aukhondo kumatiteteza. Malamulo amene Aisiraeli anapatsidwa anaphatikizapo kusamba m’manja pambuyo pogwila mtembo, kupatula anthu odwala matenda oyambukila, komanso kutaya zonyansa za munthu moyenelela. (Levitiko 11:28; 13:1-5; Deuteronomo 23:13) Mosiyana na zimenezi, Aiguputo anali kusakaniza zinthu zina na zonyansa za munthu kupanga mankhwala ophaka munthu pa cilonda.

Kodi Baibo ili na mfundo zolakwika zokhudza sayansi?

 Tikafufuza bwino m’Baibo tizapeza kuti yankho yake ni ayi. Pansipa pali maganizo olakwika amene anthu ali nawo okhudza kulondola kwa Baibo pankhani ya sayansi:

 Maganizo olakwika: Baibo imakamba kuti cilengedwe conse cinalengedwe m’masiku 6 cabe.

 Mfundo yazoona: Malinga na zimene Baibo imanena, Mulungu analenga cilengedwe conse kale kwambili. (Genesis 1:1) Komanso kutalika kwa nthawi imene Mulungu analenga zinthu zonse, imene ikuchulidwa kuti masiku mu Genesis caputa 1, Baibo siinafotokoze. Ndipo kutalika kwa nthawi pamene dziko lapansi na kumwamba kunalengedwa imachulidwa kuti ‘tsiku.’—Genesis 2:4.

 Maganizo olakwika: Baibo imakamba kuti zomela zinalengedwa coyamba dzuŵa isanalengedwa kuti ithandize zomelazo.—Genesis 1:11, 16.

 Mfundo yazoona: Baibo imaonetsa kuti dzuŵa, imene ni imodzi mwa nyenyezi zimene zimapanga kuthambo, inalengedwa coyamba zomela zikalibe kulengedwa. (Genesis 1:1) Kuwala kwa dzuŵa kunafika padziko lapansi mkati mwa “tsiku” loyamba ya kulenga. Pa “tsiku” lacitatu la kulenga, kuwala kwamphamvu kwa dzuŵa kunali kokwanila kuti kucilikize zomela. (Genesis 1:3-5, 12, 13) Ndipo patapita nthawi m’pamene dzuŵa linayamba kuonekela bwino-bwino padziko lapansi.—Genesis 1:16.

 Maganizo olakwika: Baibo imakamba kuti dzuŵa imazungulila dziko lapansi.

 Mfundo yazoona: Mlaliki 1:5 imati: “Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa, kenako limathamanga mwawefuwefu kupita kumalo ake kuti likatulukenso.” Komabe, lembali limafotokoza kwenikweni mmene dzuŵa limayendela tikamaiona pano padziko lapansi. Anthu akonda kukamba kuti ‘dzuŵa latuluka,’ kapena ‘dzuŵa yalowa’ pamene adziŵa kuti dziko lapansi ndiyo imazungulila dzuŵa.

 Maganizo olakwika: Baibo imati dziko niyotambalala.

 Mfundo yazoona: Baibo imaseŵenzetsa mawu akuti “kumalekezelo a dziko lapansi”; koma zimenezi sizitanthauza kuti dziko lapansi niyafulati, kapena ili na polekezela. (Machitidwe 1:8) Mofananamo, mawu akuti “kumalekezelo anayi a dziko lapansi” ni mawu okuluŵika amene amangotanthauza dziko lonse lapansi. Masiku anonso, munthu angakambe mawu akuti mbali zinayi za kampasi mophiphilitsila pokamba za dziko lonse lapansi.—Yesaya 11:12; Luka 13:29.

 Maganizo olakwika: Baibo imakamba kuti utali wa kuzungulila kwa cinthu ni wolingana ndendende na utali wodutsa pakati pa cinthu cozungulilaco tikawilikiza katatu. Koma nambala yake ya zoona ni 3.1416 pi (π).

 Mfundo yazoona: Pa lemba la 1 Mafumu 7:23; 2, komanso 2 Mbiri 4:2 paonetsa kuti pamwamba pa “thanki yamkuwa” panali papakulu mikono 10 ndipo “pankafunika cingwe cotalika mikono 30 kuti ayeze kuzungulila thankiyo.” Ziŵelengelo zimenezi ziyenela kuti zinalembedwa m’manambala athunthu (round off numbers). Nkuthekanso kuti kutalika kwa cingwe coyezela kuzungulila thanki cinali copimila mkati, pamene ciŵelengelo ca kutalika kwa pakamwa pa thankiyo sicinali ca mkati.