Yobu 35:1-16

  • Elihu anasonyeza kuti maganizo a Yobu anali olakwika (1-16)

    • Yobu ananena kuti anali wolungama kuposa Mulungu (2)

    • Mulungu ali pamwamba kwambiri, ndipo sakhudzidwa ndi tchimo (5, 6)

    • Yobu ankayenera kuyembekezera Mulungu (14)

35  Elihu anapitiriza kulankhula kuti:   “Kodi mukutsimikiza kuti zimene mukunena nʼzoona moti munganene kuti,‘Ndine wolungama kuposa Mulunguʼ?+   Inu mwanena kuti, ‘Kodi ndikachita zabwino, inu* muli nazo ntchito yanji? Kodi ndikapanda kuchimwa ndimapindula chiyani?’+   Ine ndikuyankhani inuyoLimodzi ndi anzanu+ amene muli nawowo.   Yangʼanani kumwamba muone,Muonetsetse mitambo+ imene ili kutali ndi inu.   Mukachimwa, kodi Mulungu zimamupweteka bwanji?+ Zolakwa zanu zikachuluka, kodi zimamukhudza bwanji Mulungu?+   Ngati muli wolungama, kodi mumamʼpatsa chiyani?Kodi amalandira chiyani kuchokera kwa inu?+   Zoipa zimene mumachita zimangopweteka munthu ngati inu nomwe,Ndipo chilungamo chanu chimangothandiza mwana wa munthu.   Ngati anthu akuponderezedwa kwambiri, amalira kuti athandizidwe.Amalira kuti apulumutsidwe mʼmanja mwa anthu amphamvu amene akuwapondereza.+ 10  Koma palibe amene amanena kuti, ‘Kodi Mulungu Wamkulu amene anandipanga+ ali kuti,Amene amachititsa kuti tiziimba nyimbo usiku?’+ 11  Iye amatiphunzitsa+ zinthu zambiri kuposa nyama zakutchire,+Ndipo amatipatsa nzeru kuposa mbalame zamumlengalenga. 12  Iwo amalira kuti athandizidwe, koma iye sawayankha,+Chifukwa cha kunyada kwa anthu oipa.+ 13  Ndithudi Mulungu samvetsera kulira kwachinyengo,*+Wamphamvuyonse samvetsera zinthu zabodza. 14  Ndiye kodi iye angamvetsere mukamadandaula kuti simukumuona?+ Iye ndi amene angaweruze mlandu wanu, choncho muzimuyembekezera.+ 15  Pajatu iye sanakukwiyireni nʼkukupatsani chilango,Komanso sanaone kudzitukumula kwanu.+ 16  Choncho Yobu watsegula pakamwa pake mopanda phindu.Ngakhale kuti sakudziwa zoona, iye akulankhula zambirimbiri.”+

Mawu a M'munsi

Nʼkutheka kuti akunena Mulungu.
Kapena kuti, “samvetsera bodza.”