Yobu 38:1-41

  • Yehova anasonyeza kuti munthu ndi wamngʼono (1-41)

    • ‘Unali kuti pamene dziko lapansi linkalengedwa?’ (4-6)

    • Ana a Mulungu anafuula mosangalala (7)

    • Mafunso okhudza zinthu zodabwitsa zamʼchilengedwe (8-32)

    • “Malamulo amene zinthu zakuthambo zimatsatira” (33)

38  Kenako Yehova anayankha Yobu kudzera mumphepo yamkuntho kuti:+   “Kodi uyu ndi ndani amene akuphimba malangizo angayuNʼkumalankhula mopanda nzeru?+   Konzeka ngati mwamuna wamphamvu.Ndikufunsa mafunso ndipo iweyo undiyankhe.   Kodi unali kuti pamene ndinkaika maziko a dziko lapansi?+ Ndiuze ngati ukudziwa mmene zinakhalira.   Ndi ndani amene anaika miyezo yake, ngati ukudziwa,Kapena ndi ndani analiyeza ndi chingwe choyezera?   Kodi zipilala zake zinazikidwa pachiyani?Kapena ndi ndani amene anaika mwala wake wapakona,+   Pamene nyenyezi zamʼmawa+ zinafuula pamodzi mosangalala,Ndiponso pamene ana onse a Mulungu*+ anayamba kufuula mosangalala?   Ndi ndani anatseka nyanja ndi zitseko,+Pamene inaphulika kuchokera mʼmimba,   Pamene ndinaiveka mitamboNʼkuikulunga mumdima wandiweyani, 10  Pamene ndinaiikira malire,Nʼkuiikiranso mpiringidzo ndi zitseko zake,+ 11  Ndiye ndinati, ‘Ukhoza kufika apa, koma usapitirirepo,Ndipo mafunde ako aatali azilekezera pamenepaʼ?+ 12  Kodi unayamba* walamulapo mʼmawaKapena kuchititsa kuti mʼbandakucha udziwe malo ake,+ 13  Kuti kuwala kwake kufike mpaka kumalekezero a dziko lapansi,Nʼkuthamangitsa anthu oipa kuti achokemo?+ 14  Dzikolo limasintha ngati dongo limene ladindidwa ndi chodindira,Ndipo limaoneka ngati chovala chokongola cha mitundu yosiyanasiyana. 15  Koma kuwala kwa oipa kwachotsedwa,Ndipo dzanja lawo limene analikweza mʼmwamba lathyoledwa. 16  Kodi unayamba wafika kumene kuli akasupe a nyanjaKapena kodi unayamba wafufuzapo zimene zili pansi pa nyanja zakuya?+ 17  Kodi anayamba akuululira kumene kuli mageti a imfa,+Kapena kodi unaonapo mageti a mdima wandiweyani?*+ 18  Kodi ukudziwa bwino kukula kwa dziko lapansi?+ Ndiuze ngati ukudziwa zonsezi. 19  Kodi kuwala kumakhala kuti kwenikweni,+ Nanga mdima umakhala kuti? 20  Kodi ungazipititse kumalo awo,Komanso kodi ukudziwa njira zopita kunyumba kwawo? 21  Kodi ukudziwa zimenezi chifukwa choti pa nthawiyo unali utabadwa,Komanso chifukwa chakuti uli ndi zaka zambiri?* 22  Kodi unalowapo mʼnyumba zosungira madzi oundana,+Kapena unaonapo nyumba zosungira matalala,+ 23  Zimene ndazisunga kuti ndidzazigwiritse ntchito pa nthawi ya mavuto aakulu,Pa tsiku lomenyana komanso lankhondo?+ 24  Kodi kuwala kumamwazikana* kuchokera kuti,Ndipo kodi mphepo yakumʼmawa imawomba padziko lapansi kuchokera kuti?+ 25  Ndi ndani anatsegula ngalande za madzi a mvula kuthambo,Nʼkupanga njira ya mtambo wa mvula yamabingu,+ 26  Kuti achititse mvula kugwa kumalo amene sikukhala munthu,Kuchipululu kumene kulibe anthu,+ 27  Kuti inyowetse chipululu chouma chomwe ndi chowonongeka,Nʼkuchititsa kuti udzu umere?+ 28  Kodi mvula ili ndi bambo,+Kapena ndi ndani anabereka mame?+ 29  Kodi madzi oundana amachokera mʼmimba mwa ndani,Ndipo ndi ndani amene anabereka nkhungu yamumlengalenga?+ 30  Kodi ndi ndani amene amachititsa chivundikiro cha madzi kuti chikhale cholimba ngati mwala,Komanso kuti madzi amene ali pamwamba pa madzi akuya aundane chifukwa chozizira?+ 31  Kodi ungamange zingwe za gulu la nyenyezi la KimaKapena kumasula zingwe za gulu la nyenyezi la Kesili?+ 32  Kodi ungatulutse gulu la nyenyezi* pa nyengo yakeKapena kutsogolera gulu la nyenyezi la Asi* pamodzi ndi ana ake? 33  Kodi ukudziwa malamulo amene zinthu zakuthambo zimatsatira,+Kapena kodi ungaike ulamuliro wake padziko lapansi? 34  Kodi ungafuulire mitamboKuti igwetse mvula yamphamvu nʼkukunyowetsa?+ 35  Kodi ungatumize mphezi kuti zikagwire ntchito yake? Kodi zingabwere kwa iwe nʼkudzakuuza kuti, ‘Ife tabwerakoʼ? 36  Ndi ndani anaika nzeru mʼmitambo,*+Kapena ndi ndani anachititsa kuti zinthu zakuthambo zikhale zozindikira?*+ 37  Ndi ndani amene ali wanzeru kwambiri moti angawerenge mitambo,Kapena ndi ndani amene angapendeketse zosungira madzi zakumwamba?+ 38  Ndi ndani amene amachititsa kuti fumbi lisanduke matope,Komanso kuti zibuma zadothi zimatane? 39  Kodi mkango ungausakire nyama,Kapena kuthetsa njala ya mikango yamphamvu?+ 40  Kodi ungaipatse chakudya pamene yamyata mʼmalo amene imabisala,Kapena pamene yabisalira nyama mʼnyumba zawo? 41  Ndi ndani amakonzera khwangwala chakudya,+Ana ake akamalirira Mulungu kuti awathandize,Komanso akamadzandira chifukwa chosowa chakudya?”

Mawu a M'munsi

Awa ndi mawu okuluwika a Chiheberi onena za angelo omwe ndi ana a Mulungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Kodi mʼmasiku ako unayamba.”
Kapena kuti, “mageti a mthunzi wa imfa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku ambiri.”
Mabaibulo ena amati, “chingʼaningʼani chimamwazikana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mazaroti.” Pa 2Mf 23:5, mawu ofanana ndi amenewa, omwe akunena zinthu zambiri, akunena za gulu la nyenyezi la Zodiyaki.
Mabaibulo ena amati, “gulu la nyenyezi la Chimbalangondo Chachikulu.”
Mabaibulo ena amati, “mumtima.”
Mabaibulo ena amati, “Kapena ndi ndani anaika nzeru mʼmaganizo.”