Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 4

Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama

Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama

“Zolinga zimakhazikika anthu akakambirana.”—Miyambo 20:18

Tonsefe timafuna ndalama zogulira zinthu zofunika m’banja lathu. (Miyambo 30:8) Paja “ndalama zimatetezera.” (Mlaliki 7:12) Mabanja ambiri amavutika kuti akambirane nkhani za ndalama. Koma musalole kuti ndalama zisokoneze banja lanu. (Aefeso 4:32) Mwamuna ndi mkazi ayenera kukhulupirirana ndiponso kukambirana mmene angagwiritsire ntchito ndalama zawo.

1 MUZIKHALA NDI BAJETI

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo?” (Luka 14:28) N’zofunika kwambiri kuti muzigwirizana mmene mudzagwiritsira ntchito ndalama zanu. (Amosi 3:3) Muyenera kusankha zinthu zofunika kugula komanso kuchuluka kwa ndalama zimene mungawononge. (Miyambo 31:16) Komanso ngati muli ndi ndalama zokwanira kuti mugule chinachake sikuti muyenera kuchigula basi. Yesetsani kupewa ngongole. Muzingogwiritsa ntchito ndalama zimene muli nazo.—Miyambo 21:5; 22:7.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Mukatsala ndi ndalama pa mapeto pa mwezi, muzikambirana zimene mungachite nazo

  • Ngati ndalama zanu zimakhala zoperewera, kambiranani zimene mungachite kuti musamawononge zambiri. Mwachitsanzo, m’malo mophika chakudya chambiri n’kutaya chotsala, muzingophika chokwanira bwinobwino banja lanulo

2 MUZIKAMBIRANA MOMASUKA

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Timasamalira zinthu zonse moona mtima, osati pamaso pa Yehova pokha ayi, komanso pamaso pa anthu.” (2 Akorinto 8:21) Muziuza mwamuna kapena mkazi wanu ndalama zonse zimene mumalandira komanso mmene mumazigwiritsira ntchito.

Muzikambirana kaye musanagwiritse ntchito ndalama zambiri. (Miyambo 13:10) Kukambirana bwinobwino nkhani za ndalama kungathandize kuti muzikhala mwamtendere. Muzionanso kuti ndalama zimene mumapeza ndi za banja lonse osati zanokha.—1 Timoteyo 5:8.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzikambirana n’kuona kuchuluka kwa ndalama zimene aliyense angagwiritse ntchito popanda kuuza mnzake

  • Musamadikire kuti pakhale vuto kaye kuti mukambirane za ndalama