Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 66

Zimene Zinachitika Yesu Atapita ku Chikondwerero cha Misasa ku Yerusalemu

Zimene Zinachitika Yesu Atapita ku Chikondwerero cha Misasa ku Yerusalemu

YOHANE 7:11-32

  • YESU ANAPHUNZITSA ANTHU M’KACHISI

Anthu ambiri anadziwa za Yesu kuchokera pa nthawi imene anabatizidwa. Ayuda ambiri anaona Yesu akuchita zozizwitsa ndiponso anthu ambiri akumadera akutali anamva zimene ankachita. Ndiye pa nthawi ya Chikondwerero cha Misasayi (kapena kuti Chikondwerero cha Zokolola) anthu ambiri ankafunitsitsa kumuona.

Anthuwo anali ndi maganizo osiyanasiyana ponena za Yesu. Ena ankati: “Amene uja ndi munthu wabwino” pomwe ena ankati: “Ayi si munthu wabwino amene uja, iye akusocheretsa anthu ambiri.” (Yohane 7:12) Manong’onong’o ambiri anayamba kumveka pa tsiku loyamba la chikondwererochi. Koma pa nthawiyi panalibe amene analimba mtima n’kulankhula zoikira kumbuyo Yesu chifukwa ankaopa atsogoleri achiyuda.

Patangodutsa masiku angapo chikondwererochi chitayamba, Yesu anapita kukachisi. Anthu ambiri anadabwa chifukwa Yesu ankaphunzitsa mwaluso kwambiri. Anthuwo ankadabwa chifukwa chakuti Yesu sanaphunzitsidwe ku sukulu za arabi ndipo ankafunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu zolembazi anazidziwa bwanji, popeza sanapite kusukulu?”—Yohane 7:15.

Koma Yesu anawayankha kuti: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma. Ngati munthu akufuna kuchita chifuniro cha amene ananditumayo, adzadziwa za chiphunzitsochi ngati chili chochokera kwa Mulungu, kapena ngati ndimalankhula za m’maganizo mwanga.” (Yohane 7:16, 17) Zimene Yesu ankaphunzitsa zinali zogwirizana ndi Chilamulo cha Mulungu, choncho zinali zoonekeratu kuti sankafuna kuti anthu azilemekeza iyeyo koma azilemekeza Mulungu.

Kenako Yesu anawauza kuti: “Mose anakupatsani Chilamulo, si choncho kodi? Komatu palibe ngakhale mmodzi wa inu amene amamvera Chilamulocho. Nanga n’chifukwa chiyani inu mukufuna kundipha?” Anthu ena omwe anali pagulupo, amene mwina anali alendo ochokera m’mizinda ina, sanamvetse kuti Yesu ankatanthauza chiyani ponena mawu amenewa. Iwo ankaganiza kuti zingatheke bwanji kuti munthu wina akonze chiwembu chofuna kupha mphunzitsi wabwino ngati Yesu. Choncho anayamba kumukayikira ngati ankaganiza bwinobwino ponena kuti anthu ena ankafuna kumupha. Anthuwo anati: “Uli ndi chiwanda iwe. Akufuna kukupha ndani?”—Yohane 7:19, 20.

Kukadali chaka ndi hafu zimenezi zisanachitike, atsogoleri achiyuda ankafuna kupha Yesu atachiritsa munthu pa tsiku la Sabata. Pokumbukira zimenezo Yesu anafotokoza mfundo ina pofuna kusonyeza kuti atsogoleriwo anali ndi maganizo olakwika. Anafotokoza zimene zinalembedwa mu Chilamulo kuti mwana wamwamuna akabadwa, azidulidwa pakatha masiku 8 ngakhale tsikulo litakhala la Sabata. Ndiyeno anawafunsa kuti: “Ngati munthu amadulidwa tsiku la sabata posafuna kuphwanya chilamulo cha Mose, kodi mukundipsera mtima ine chifukwa ndinachiritsa munthu tsiku la sabata? Lekani kuweruza poona maonekedwe akunja, koma muziweruza ndi chiweruzo cholungama.”—Yohane 7:23, 24.

Anthu amene ankakhala ku Yerusalemu, omwenso ankadziwa kuti Ayuda ankafuna kupha Yesu, ananena kuti: “Si ameneyu kodi akufuna kumupha uja? Koma taonani! Si uyu akulankhula poyera apa, ndipo palibe akunenapo kanthu kwa iye. Olamulirawo sakutsimikiza ngati iyeyo alidi Khristu eti?” Koma n’chifukwa chiyani anthuwo sankakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu? Chifukwa ankanena kuti: “Koma ife tikudziwa kumene munthu ameneyu akuchokera. Komano Khristuyo akadzabwera, palibe amene adzadziwe kumene wachokera.”—Yohane 7:25-27.

Akadali m’kachisi momwemo Yesu anawayankha kuti: “Inu mukundidziwa ine komanso mukudziwa kumene ndikuchokera. Ndipo ine sindinabwere mwa kufuna kwanga, alipo ndithu amene anandituma, koma inu simukumudziwa. Ine ndikumudziwa, chifukwa ndine nthumwi. Iyeyu anandituma ine.” (Yohane 7:28, 29) Chifukwa cha zimene analankhulazo, anthuwo anaganiza zoti amugwire kuti mwina akamutsekere kundende kapena angomupha. Koma zimene ankaganizazo sizinatheke chifukwa nthawi yoti Yesu aphedwe inali isanafike.

Komabe anthu ambiri anakhulupirira Yesu. Ndipo mpake kuti anachita zimenezi chifukwa nthawi ina Yesu anayenda pamadzi, analetsa mphepo yamphamvu, anadyetsa anthu ambiri pochulukitsa mikate yochepa ndiponso nsomba, anachiritsa odwala, anathandiza osayenda kuti ayambe kuyenda, anatsegula maso a osaona, anachiritsa akhate komanso anaukitsa akufa. N’chifukwa chake zinali zomveka kuti anthuwo afunse kuti: “Akadzafika Khristu, kodi adzachita zizindikiro zochuluka kuposa zimene munthu uyu wachita?”—Yohane 7:31.

Afarisi atamva kuti anthu akulankhula zimenezi, iwowo pamodzi ndi ansembe aakulu anatumiza alonda kuti akamugwire Yesu.