Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 114

Khristu Akadzayamba Kulamulira Adzaweruza Nkhosa ndi Mbuzi

Khristu Akadzayamba Kulamulira Adzaweruza Nkhosa ndi Mbuzi

MATEYU 25:31-46

  • YESU ANANENA FANIZO LA NKHOSA NDI MBUZI

Yesu ali paphiri la Maolivi ananena fanizo la anamwali 10 komanso la ndalama za matalente. Pomaliza kuyankha funso la atumwi ake lokhudza chizindikiro cha kukhalapo kwake komanso chizindikiro chakuti dziko la Satanali latsala pang’ono kutha, Yesu ananenanso fanizo lina. Fanizoli limanena za nkhosa ndi mbuzi.

Yesu anayamba kufotokoza zimene zinachitika m’fanizoli kuti: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero.” (Mateyu 25:31) Pamene ankanena fanizoli, Yesu anasonyezeratu kuti ankanena za iyeyo chifukwa nthawi zambiri ankadzitchula kuti “Mwana wa munthu.”—Mateyu 8:20; 9:6; 20:18, 28.

Kodi fanizo limeneli lidzakwaniritsidwa liti? Lidzakwaniritsidwa Yesu “akadzafika mu ulemerero wake” limodzi ndi angelo n’kukhala “pampando wake wachifumu waulemerero.” M’mbuyomo Yesu anali atanenapo kale kuti “Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu” pamodzi ndi angelo ake. Kodi zimenezi zidzachitika liti? Zidzachitika “chisautso chikadzangotha.” (Mateyu 24:29-31; Maliko 13:26, 27; Luka 21:27) Choncho fanizoli lidzakwaniritsidwa Yesu akadzabwera mu ulemerero wake m’tsogolo. Kodi adzachita chiyani pa nthawi imeneyo?

Yesu ananena kuti: “Mwana wa munthu akadzafika. . . , mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye ndipo adzalekanitsa anthu, mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Adzaika nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi adzaziika kumanzere kwake.”—Mateyu 25:31-33.

Ponena za nkhosa zomwe zidzakhale kudzanja lake lamanja Yesu ananena kuti: “Pamenepo mfumu idzauza a kudzanja lake lamanja kuti, ‘Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga. Lowani mu ufumu umene anakonzera inu kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.” (Mateyu 25:34) N’chifukwa chiyani Mfumuyi inakonda nkhosa?

Mfumuyo inanena kuti: “Ine ndinamva njala koma inu munandipatsa chakudya. Ndinamva ludzu koma inu munandipatsa chakumwa. Ndinali mlendo koma inu munandilandira bwino. Ndinali wamaliseche koma inu munandiveka. Ndinadwala koma inu munandisamalira. Ndinali m’ndende koma inu munabwera kudzandiona.” Ndiyeno anthu ‘olungama’ omwe ndi nkhosazo anafunsa mmene anachitira zinthu zimenezo. Mfumu inayankha kuti: “Pa mlingo umene munachitira zimenezo mmodzi wa abale anga aang’ono awa, munachitira ine amene.” (Mateyu 25:35, 36, 40, 46) Mosakayikira anthuwa sanachite zinthu zabwino zimenezi ali kumwamba chifukwa kumwamba kulibe anthu odwala kapena anjala. Choncho zimenezi ziyenera kukhala zinthu zimene anachitira abale ake a Khristu padziko lapansi.

Nanga n’chiyani chimene chinachitikira mbuzi zomwe zinaikidwa ku dzanja lake la manzere? Yesu anafotokoza kuti: “Kenako [Mfumu] adzauza a kumanzere kwake kuti, ‘Chokani pamaso panga inu otembereredwa. Pitani kumoto wosatha wokolezedwera Mdyerekezi ndi angelo ake. Pakuti ndinamva njala koma inu simunandipatse chakudya. Ndinamva ludzu koma inu simunandipatse chakumwa. Ndinali mlendo koma inu simunandilandire bwino. Ndinali wamaliseche koma inu simunandiveke. Ndinadwala komanso ndinali m’ndende, koma inu simunandisamalire.’” (Mateyu 25:41-43) Mpake kuti mbuzi zidzalandira chiweruzo chimenechi chifukwa cholephera kusonyeza chifundo kwa abale ake a Khristu pa nthawi imene anali padziko lapansi.

Atumwi anazindikira kuti chiweruzo chimene chidzaperekedwe m’tsogolo sichidzasintha mpaka kalekale. Yesu anawauza kuti: “Pamenepo [Mfumu] adzawayankha kuti, ‘Ndithu ndikukuuzani, Popeza simunachitire zimenezo mmodzi wa aang’ono awa, simunachitirenso ine.’ Ndipo iwowa adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu, koma olungama ku moyo wosatha.”—Mateyu 25:45, 46.

Zimene Yesu ananena poyankha funso la atumwi, zimathandiza kwambiri otsatira ake kuganizira za khalidwe lawo komanso zochita zawo.