Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mtendere Udzabweradi Padziko Lapansi!

Mtendere Udzabweradi Padziko Lapansi!

Mtendere Udzabweradi Padziko Lapansi!

ANTHU ena amaganiza kuti palibenso njira ina kupatulapo chiwawa imene angapezere ufulu wandale ndi kuyeretsa chipembedzo, ndiponso kuti mphamvu zowononga zokha n’zimene zingachotse atsogoleri osafunidwa. Ndiponso, maboma ena amagwiritsa ntchito chiwawa kuti akhazikitse bata ndi kuchititsa anthu awo kuwamvera. Koma ngati n’zoona kuti uchigawenga ndi njira yabwino yolamulira ndi kusinthira zinthu, uyenera kubweretsa mtendere, chitukuko, ndi bata. Pakapita nthawi, chiwawa ndi mantha ziyenera kutha. Kodi taona zimenezi zikuchitika?

Zoona zake n’zoti uchigawenga umachititsa anthu kusiya kulemekeza moyo ndipo umayambitsa kuphana ndi nkhanza. Chifukwa chopwetekedwa mtima, anthu amene achitidwa zauchigawenga nthawi zambiri amabwezera. Akabwezera choncho, amawaponderezanso kwambiri, ndipo zimawapangitsa kuti abwezerenso.

Chiwawa Sichithetsa Mavuto

Anthu akhala akuyesera kuthetsa mavuto awo a ndale, a chipembedzo, ndi okhudza umoyo wawo paokha kwa zaka zambiri. Koma zoyesayesa zawo zonse zalephera. N’zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, kuti: “Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Yesu anati: “Nzeru imadziwika ndi zotsatirapo zake.” (Mateyu 11:19, The New Testament in Modern English, lolembedwa ndi J. B. Phillips) Tikatengera pa mfundo za m’Baibulo zimenezi, tingaone kuti uchigawenga umapereka chiyembekezo chabodza. Uchigawenga sunabweretse ufulu ndi chimwemwe, koma m’malo mwake, wabweretsa imfa, kuzunzika, ndi kuwonongeka kwa zinthu. Zotsatirapo zoipa zimenezi zinali paliponse m’zaka za m’ma 1900 ndipo zikuyamba kufalikiranso m’zaka za m’ma 2000 zino. Anthu ambiri anganene kuti uchigawenga umangobweretsa mavuto ena m’malo mowathetsa.

“Tsiku lililonse ndimalakalaka kuti munthu wa m’banja mwathu kapena mnzanga aliyense asafe . . . Mwina tikufunikira chozizwitsa.” Analemba choncho mtsikana wina wamng’ono amene m’dziko mwawo munali mutadzaza chiwawa cha zigawenga. Mawu akewo akufanana ndi zimene anthu ambiri azindikira: Kuti anthu paokha sangathe kuthetsa mavuto awo. Ndi Mlengi wa anthu yekha amene angathetse mavuto amene alipowa, kuphatikizapo uchigawenga. Koma kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Mulungu?

Zifukwa Zimene Tingakhulupirire Mulungu

Chifukwa chimodzi n’choti pokhala Mlengi, Yehova anatipatsa moyo ndipo amafuna kuti tisangalale nawo ndipo tikhale pamtendere, komanso tisamasowe kalikonse. Mneneri wa Mulungu Yesaya analemba kuti: “Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu.” (Yesaya 64:8) Yehova ndiye Tate wa mtundu wonse wa anthu, ndipo anthu a mitundu yonse ndi amtengo wapatali kwa iye. Iye sindiye wachititsa kupanda chilungamo ndi chidani zimene zimayambitsa uchigawenga. Mfumu yanzeru Solomo inanenapo kuti: “Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu.” (Mlaliki 7:29) Zimene zimayambitsa uchigawenga ndizo kuipa kwa anthu ndi mphamvu ya ziwanda, osati kulephera kwa Mulungu.—Aefeso 6:11, 12.

Chifukwa china chomwe tingakhulupirire Yehova n’choti, amadziwa bwino kuposa wina aliyense chimene chimayambitsa mavuto a anthu ndi momwe angawathetsere popeza iye ndi amene anawalenga. Baibulo limanena mfundo yoona iyi pa Miyambo 3:19. Limati: “Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zam’mwamba ndi luntha.” Ndi chikhulupiriro chonse mwa Mulungu, munthu wina wakale analemba kuti: “Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova. Wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.”—Salmo 121:1, 2.

Palinso chifukwa chachitatu chomwe tiyenera kukhulupirira Mulungu: Iye ali ndi mphamvu zotha kuletsa kuphana mwachiwawa komwe kukuchitikaku. Mu nthawi ya Nowa, “dziko lapansi . . . linadzala ndi chiwawa.” (Genesis 6:11) Chiweruzo cha Mulungu chinali chadzidzidzi ndiponso chotheratu. Iye “sanalekerera dziko lapansi lakale, . . . pakulitengera dziko la osapembedza chigumula.”—2 Petro 2:5.

Baibulo limatchula phunziro limene tiyenera kutengapo pa Chigumula cha m’tsiku la Nowa, lakuti: “Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe.” (2 Petro 2:9) Mulungu amatha kusiyanitsa pakati pa anthu amene akufunadi moyo wabwinopo ndi amene amachititsa moyo wa ena kukhala wovuta. Iye wasungira anthu oterowo “chiwonongeko cha anthu osapembedza.” Koma pofuna kuthandiza anthu amene amafuna mtendere, iye akukonza dziko lapansi limene mudzakhalitsa chilungamo.—2 Petro 3:7, 13.

Padziko Lapansi Padzakhala Mtendere Wosatha!

Olemba Baibulo nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito mawu oti “dziko” kutanthauza anthu. Mwachitsanzo, lemba la Genesis 11:1 limati “dziko lapansi,” kutanthauza anthu onse amene anali ndi moyo panthawi imeneyo, linalankhula chinenero chimodzi. Mtumwi Petro anali ndi tanthauzo limenelo m’maganizo pamene analemba za “dziko latsopano.” Yehova Mulungu adzasintha anthu m’njira yakuti chilungamo chidzalowa m’malo mwa chiwawa ndi chidani monga zinthu ‘zokhalitsa’ padziko. Pa ulosi umene unalembedwa pa Mika 4:3, Baibulo limatiuza kuti: “Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale makasu, ndi mikondo yawo ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.”

Kodi anthu azidzakhala bwanji ulosi umenewo ukadzakwaniritsidwa? Lemba la Mika 4:4 limati: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.” M’Paradaiso wapadziko lapansi ameneyo, palibe amene azidzakhala mwamantha poopa kuti zigawenga zichita zachiwawa. Kodi mungakhulupirire lonjezo limenelo? Inde, “pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.”—Mika 4:4.

Choncho, pamene zigawenga zikupitiriza kuopseza anthu paliponse ndipo mayiko akuchita mantha chifukwa cha chiwawa, kwa anthu okonda mtendere, njira yothetsera zonsezi ndiyo kukhulupirira Yehova. Palibe vuto limene Yehova sangathe kuthetsa. Adzathetsa kuvulala, kuvutika, ngakhalenso imfa. Baibulo limati: “Iye wameza imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.” (Yesaya 25:8) Mayiko okondedwa a anthu ambiri, amene panopa ndi odzaza ndi kupweteka ndi mantha chifukwa cha uchigawenga, posachedwapa adzadzaza ndi zipatso za mtendere. Mtendere umenewo, umene unalonjezedwa ndi Mulungu “wosanamayo,” ndi umene anthu akufunikira kwambiri.—Tito 1:2; Ahebri 6:17, 18.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 9]

NJIRA YABWINO KUPOSA ZIPOLOPOLO NDI MABOMBA

Mawu ali m’munsiwa ananenedwa ndi anthu amene ankakhulupirira kuti chiwawa ndiyo njira yobweretsera kusintha pa ndale.

▪ “Pamene ndinali kuwerenga mabuku a mbiri yakale, ndinazindikira kuti mafumu ndi akuluakulu a boma nthawi zonse akhala akupondereza anthu osauka. Ndinatha kuona mmene anthu otsika anali kuvutikira. Pamene ndinali kuganizira za mmene kuipa kumeneku kudzathere, ndinaona kuti tiyenera kumenyana ndi mfuti.”Anatero Ramon. *

▪ “Ndinachita nawo ziwawa zamfuti. Cholinga changa chinali kutsutsana ndi ulamuliro wakale ndi kubweretsa dongosolo loti lichotse kusiyana pakati pa anthu.”—Anatero Lucian.

▪ “Kuyambira ndili mwana, zinthu zopanda chilungamo sizinkandisangalatsa. Zimenezi zinali zinthu monga umphawi, umbanda, maphunziro operewera, ndi kusowa kwa thandizo la mankhwala. Ndinkakhulupirira kuti pogwiritsira ntchito zida za nkhondo, anthu onse akanatha kupeza maphunziro abwino, thandizo la mankhwala, nyumba, ndi ntchito. Ndinkakhulupiriranso kuti aliyense wosafuna kumvera malamulo ndi kulemekeza munthu mnzake ayenera kulangidwa.”—Anatero Peter.

▪ “Ine ndi mwamuna wanga tinali m’gulu lachinsinsi limene linkalimbikitsa ziwawa zotsutsa boma. Tinkafuna kubweretsa boma limene likanatukula moyo wa anthu ndi kusungitsa bwino bata m’dziko komanso limene likanathetsa kusiyana pakati pa anthu. Tinkaona kuti kuchita zinthu zotsutsana ndi boma ndi njira yokhayo yomwe tingabweretsere chilungamo m’dziko lathu.”—Anatero Lourdes.

Anthu amenewa anayesera kuthandiza anthu ovutika pogwiritsa ntchito chiwawa. Koma chifukwa chophunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anazindikira kuti Mawu a Mulungu ali ndi njira yabwino yochitira zinthu. Baibulo limafotokoza pa Yakobo 1:20 kuti: “Mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.” Baibulo la Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono limati: “Munthu wokwiya sangathe kuchita zolungama pamaso pa Mulungu.”

Ndi ulamuliro wa Mulungu wokha umene ungasinthe moyo wa anthu. Maulosi a m’Baibulo monga Mateyu chaputala 24 ndi 2 Timoteo 3:1-5 amasonyeza kuti boma la Mulungu latsala pang’ono kuchita zimenezo. Tikukulimbikitsani kuti muphunzire mfundo zoona zimenezi pophunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Tasintha mayina.