Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Akuopa Zam’tsogolo?

N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Akuopa Zam’tsogolo?

N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Akuopa Zam’tsogolo?

Padziko lonse anthu akaona zinthu zochititsa mantha zimene zikuchitikazi, amaopa mmene zinthu zidzakhalire m’tsogolo. Motero, pofuna kukhala otetezeka, m’mizinda yambiri anaikamo makamera oonera zinthu zosiyanasiyana zimene zikuchitika. Chifukwa choopa uchigawenga, m’mabwalo andege osiyanasiyana muli asilikali ochuluka zedi moti mukungooneka ngati malo a asilikali. Mbava ndi anthu ena okonda kugwirira ana amagwiritsa ntchito Intaneti pofuna kubera ndiponso kupezerera anthu amene sakudziwa maganizo awo oipawo. Komanso zinthu monga kuwonongeka kwa chilengedwe, kusakazika kwa mitengo, kutha kwa nyama zambiri ndiponso kutentha kwa dziko, zikuchititsa anthu kukayikira za mmene moyo udzakhalire m’tsogolomu.

M’MIBADWO iwiri yapitayo palibe aliyense akanaganizako za mavuto amenewa, koma pano afala padziko lonse. Mpake kuti anthu ambiri amadzifunsa kuti kodi dzikoli likupita kuti? Ndipo kodi iwo ndi ana awo adzakhala ndi tsogolo lotani? Kodi anthu adzachita kufika poopa kukwera basi, sitima kapena ndege? Malingana ndi kukwera kwa mitengo ya zinthu ndiponso kuchuluka kwa anthu padzikoli, kodi anthu m’tsogolomu adzakwanitsa kupeza thandizo lamankhwala, chakudya chabwino ndiponso mafuta oyendetsera zinthu zosiyanasiyana?

Ponena za kukwera kwa mitengo ya thandizo la mankhwala, nduna ina ya zaumoyo ku Canada, inati: “Zikuoneka kuti zinthu zifika poipa kwambiri m’tsogolo muno.” Anthu ambiri akuda nkhawa akaganizira za chakudya komanso mafuta oyendetsera zinthu zosiyanasiyana. Chifukwa chiyani akuda nkhawa? Pofuna kuti asamadalire kwambiri mafuta ochokera pansi panthaka, mayiko ena akuthera ndalama zambiri kupanga mafuta pogwiritsa ntchito zomera. Kwanthawi yoyamba, malo olima amene anthu ali nawo afunika kutulutsa chakudya cha anthu komanso mafuta a galimoto. Motero mitengo ya chakudya yayamba kale kukwera.

Masiku ano kusiyana kwa anthu olemera ndi osauka kukukulirakulira ndipo zikuchititsa moyo kukhala wovuta. Lipoti la Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linati: “M’zaka khumi zoyambirira za m’ma 2000 anthu ena akhala ndi moyo wapamwamba pomwe ena ndi osauka kwambiri. Zaka zimene anthu a m’mayiko osaukitsitsa amakhala ndi moyo zimangokhala theka la zaka zimene anthu a m’mayiko olemera kwambiri amakhala ndi moyo.” Kwenikweni zimenezi zimachitika chifukwa cha matenda, umphawi ndiponso mavuto ena a zandale.

Taganiziraninso za kutentha kwa dziko kumene kukuchititsa malo ambiri kukhala zipululu komanso mavuto ena a zanyengo. M’posadabwitsa kuti anthu ambiri ozindikira amaopa akaganizira za m’tsogolo. Gulu lina limene linakhazikitsa wotchi yosonyeza nthawi ya chiwonongeko, linanena kuti zinthu zifika poipa kwambiri m’tsogolomu popeza “asayansi akuonabe mavuto amene kutentha kwa dziko kwabweretsa pa zinthu za chilengedwe.”—Bulletin of the Atomic Scientists.

Mmene zinthu zililimu, kodi tinganene kuti kutsogoloku kulibiretu chabwino? Kodi kuti tikhale ndi tsogolo labwino zikungodalira anthu ochita bwino pankhani za malonda, ndale, chipembedzo ndiponso sayansi? Ena angafunse kuti, ‘Kodi pali njira ina iliyonse yokonzera zinthu?’ Iwo amati: ‘Mavutowa tadzibweretsera tokha motero tiyenera kuwakonzanso tokha.’ Ena amanena kuti anthufe sitingathe kukonza zinthu. Ndipo amati Mulungu yekha ndi amene angasinthe zinthu kuti tikhale ndi tsogolo labwino. Ngati ndi choncho, kodi pali umboni wakuti Mulungu amatiganizira ndipo adzatipulumutsa? Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso amenewa.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Kuti tikhale ndi tsogolo labwino, kodi zikungodalira anthu ochita bwino pankhani za malonda, ndale, chipembedzo ndiponso sayansi?