Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Dzikoli Lidzakhala Paradaiso?

Kodi Dzikoli Lidzakhala Paradaiso?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Dzikoli Lidzakhala Paradaiso?

NTHANO za mitundu yambiri ya anthu, monga ya ku Egypt, Mexico, Peruvia, ndi Tibet zimatchula nthawi inayake yakale. Zimati panthawiyo dziko lonse linali mumtendere ndipo anthu analibe uchimo koma anali ndi ubwenzi wabwino kwambiri ndi Mulungu, ndipo sankadwala kapena kufa. Nthano zimenezi zimasimbanso zimene zinachitika kuti anthu akhale ochimwa.

Ngakhale kuti m’nthanozi anawonjezeramo mfundo zina ndi zina, n’zoonekeratu kuti nthano zonsezi zinayambira pa nkhani imodzi. Motero anthu ambiri amaona kuti nthanozi zinachokera pa nkhani imene inachitikadi. Zimenezi n’zoona chifukwa nkhani za m’nthanozo zikufanana kwambiri ndi nkhani imene inafotokozedwa m’machaputala oyambirira a buku la m’Baibulo la Genesis. Koma tikawerenga nkhaniyi timaona kuti si nthano ayi, koma ndi nkhani yoti inachitikadi ndipo imafotokoza zinthu bwinobwino m’njira yolondola.—2 Timoteyo 3:16.

Poyamba Anali Angwiro

Buku la Genesis limatiuza kuti Mulungu atalenga anthu oyamba, Adamu ndi Hava, anawaika m’munda wokongola, wotchedwa Edene. Iwowa anali ndi thanzi labwino ndiponso akanatha kukhala ndi moyo wosatha, koma Mulungu anawauza kuti akachimwa adzafa. (Genesis 2:8-17; Aroma 5:12) Anawauzanso kuti “mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:28) Zimenezi zikanachititsa kuti dziko lonse likhale paradaiso wokhala ndi anthu angwiro, osangalala ndiponso omvera Mulungu yemwe ndi Wolamulira wawo.

N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu, motero anataya mwayi wawo wokwaniritsa cholinga cha Mlengi komanso wokhala ndi moyo wosatha. Komabe, Yehova Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake cholengera dziko lapansi. Iye anati: “Mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe,” koma adzakwaniritsidwa. (Yesaya 55:11) Inde mfundo yaikulu m’Baibulo ndi yokhudza cholinga cha Yehova choti dziko lapansi likhale paradaiso woti anthu otsanzira makhalidwe ake azikhalamo.—Aroma 8:19-21.

“Udzakhala Nane M’Paradaiso”

Adamu ndi Hava atangochimwa, Mulungu analonjeza kuti padzakhala “mbewu,” imene idzawonongeretu “njoka yakale ija,” yemwe ndi Satana Mdyerekezi, n’kuchotseratu zoipa zonse zimene anachita. (Genesis 3:15; Chivumbulutso 12:9; 1 Yohane 3:8) Patsogolo pake zinaoneka kuti “mbewu” imeneyi ndi Yesu Khristu. (Agalatiya 3:16) Mulungu anamuika Yesu kuti akhale Mfumu ya Ufumu wakumwamba, kapena kuti boma limene lidzalamulire dziko lonse.—Danieli 7:13, 14; Chivumbulutso 11:15.

Khristu adzakwaniritsa zinthu zonse zimene Adamu analephera. Ndipotu Baibulo limanena kuti Yesu ndi “Adamu womalizira.” (1 Akorinto 15:45) M’pemphero lachitsanzo, Yesu anasonyeza kuti tsogolo la dzikoli likudalira pa Ufumu wa Mulungu. Pempherolo limati: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.”—Mateyo 6:10.

Monga Mfumu ya ufumu umenewu, Yesu ali padziko lapansi pano ananena mawu akuti, “udzakhala nane m’Paradaiso” kwa munthu wochimwa amene anapachikidwa pafupi naye. Panthawiyi munthuyo anali atalapa. (Luka 23:43) Mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu choyambirira, paradaiso amene Yesu ankanena adzakhala padziko lapansi pompano. Mfundo imeneyi imafotokozedwa momveka bwino m’Baibulo. Taonani Malemba awa.

“Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.” (Salmo 72:16) “Pakuti oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo.” (Miyambo 2:21) ‘Anthu angwirowo sadzaipitsa, sadzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’—Yesaya 11:9.

Mogwirizana ndi malemba amenewa, Yesu ananena izi pa Ulaliki wa pa Phiri: “Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.” (Mateyo 5:5) Patsogolo pake, mtumwi Yohane analemba kuti: “Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu . . . Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Pamenepo n’zoonekeratu kuti malemba a m’Baibulowa sakunena za “paradaiso” wakumwamba koma za paradaiso wa padziko lapansi pompano.

Zimene Akatswiri a Maphunziro a Baibulo Anena

Akatswiri ambiri a maphunziro a Baibulo amanena kuti muulamuliro wa Ufumu wa Khristu, dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Katswiri wina wotere, dzina lake Joseph A. Seiss, anati: ‘Muulamuliro wa Mesiya, dziko lonse lidzakhala mmene linalili Adamu asanachimwe.’ M’buku lake lina, Henry Alford analemba kuti: “Ufumu wa Mulunguwu udzapitiriza kulamulira mpaka kufika pokhazikika monga ufumu wa padziko lonse, ndipo anthu onse olamulidwa ndi Ufumuwo adzalandira dziko lapansi, lomwe lidzakhale litakonzedwa n’kubwerera mwakale ndipo adzakhala mmenemo kosatha.”—The New Testament for English Readers.

Mofanana ndi mfundo imeneyi, wasayansi wotchuka dzina lake Isaac Newton, yemwe ankawerenga kwambiri Baibulo, anati: “Anthu adzapitirira kukhala padziko lapansi pambuyo pa tsiku la chiweruzo ndipo sadzakhala kwa zaka 1000 zokha ayi, koma kosatha.”

Chifukwa choti dziko lapansi lidzayamba kulamuliridwa mwachindunji ndi Yesu Khristu, zoipa sizidzazikanso mizu. (Yesaya 11:1-5, 9) Inde, dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso, motero Mlengi wake adzatamandidwa kosatha.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi Mulungu anali ndi cholinga chotani polenga anthu komanso dziko lapansi?—Genesis 1:28.

▪ Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita chiyani?—Mateyo 6:10.

▪ N’chifukwa chiyani zoipa sizidzazikanso mizu?—Yesaya 11:1-5, 9.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

“Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.”—Mateyo 5:5