Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Liziyenda Bwino

Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Liziyenda Bwino

Zimene Baibulo Limanena

Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Liziyenda Bwino

“Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’? . . . Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Anatero Yesu Khristu, malinga ndi Mateyu 19:4-6.

MASIKU ano anthu ambiri amaona ukwati mopepuka. Anthu ambiri okwatirana akumati akangokumana ndi mavuto pang’ono kapena akangoona kuti mnzawoyo sakuonekanso bwino ngati mmene analili poyamba, akumapatukana kapena kusudzulana. Zoterezi zikachitika, ana ndi amene amavutika kwambiri.

Anthu amene amawerenga Baibulo, amadziwa chifukwa chake zimenezi zikuchitika. Baibulo linalosera kuti “masiku otsiriza,” omwe ndi nthawi yomwe tikukhalayi, anthu ambiri adzakhala osakhulupirika komanso opanda chikondi. (2 Timoteyo 3:1-5) Choncho n’zosadabwitsa kuti mabanja ambiri akutha. Kodi inuyo mukuda nkhawa ndi mmene banja lanu likuyendera? Kodi inuyo mumaona kuti banja lanu ndi lofunika?

Malangizo a m’Baibulo angathandize banja lanu kuti liziyenda bwino. Malangizo amenewa akhala akuthandiza mabanja kuyambira kale kwambiri ndipo ngakhale masiku ano, malangizo amenewa akugwirabe ntchito. Mwachitsanzo, taonani mfundo zisanu zotsatirazi zomwe zingathandize kuti banja lanu liziyenda bwino. *

Mfundo Zisanu Zimene Zingathandize Banja Lanu

(1) Muziona kuti ukwati ndi wopatulika. Mogwirizana ndi mawu omwe ali kumanzereku, Yesu komanso Mlengi wathu Yehova Mulungu, amaona kuti banja ndi lopatulika. Umboni wa zimenezi ndi malangizo amphamvu amene Mulungu anapereka kwa amuna ena kalelo, amene ankasiya akazi awo kuti akwatire atsikana. Mulungu anawauza kuti: “Aliyense wa inu wachitira zachinyengo mkazi amene anamukwatira ali mnyamata, ngakhale kuti iye anali mnzake komanso mkazi wa pangano lake. . . . Pakuti ine ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja.” (Malaki 2:14-16) Choncho, n’zoonekeratu kuti Mulungu saona ukwati mopepuka. Iye amakhumudwa kwambiri anthu okwatirana akamachitirana nkhanza.

(2) Mwamuna asamanyalanyaze udindo wake. Kuti zinthu ziyende bwino m’banja, pamafunika winawake wotsogolera. Baibulo limapereka udindo umenewu kwa mwamuna. Lemba la Aefeso 5:23 limati: “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake.” Koma zimenezi sizitanthauza kuti mwamuna azichitira nkhanza mkazi wake. Mwamuna ayenera kukumbukira kuti iye ndi mkazi wake ndi “thupi limodzi,” ndipo ayenera kumulemekeza komanso kumva maganizo ake pa nkhani zokhudza banja lawo. (1 Petulo 3:7) Chifukwatu Baibulo limati: “Amuna akonde akazi awo monga matupi awo.”—Aefeso 5:28.

(3) Mkazi azithandiza mwamuna wake. Baibulo limanena kuti mkazi ayenera ‘kuthandiza’ mwamuna wake. (Genesis 2:18) Choncho mkazi ayenera kuchita zinthu zothandiza kuti banja liziyenda bwino. Monga womuthandiza, mkazi sayenera kupikisana ndi mwamuna wake koma ayenera kumugonjera n’cholinga choti pabanjapo pakhale mtendere. Lemba la Aefeso 5:22 limati: “Akazi agonjere amuna awo.” Koma bwanji ngati sakugwirizana ndi mwamuna wake pa nkhani inayake? Ayenera kufotokoza maganizo ake mwaulemu, monganso mmene angafunire kuti mwamuna wake azimulankhulira.

(4) Muziyembekezera kukumana ndi mavuto. Zinthu monga kulankhulana mosaganizira, mavuto a zachuma, matenda kapena kulera ana zingachititse kuti banja lisamayende bwino. N’chifukwa chake Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti anthu “olowa m’banjawo adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.” (1 Akorinto 7:28) Koma simuyenera kulola mavuto amene mukukumana nawo kusokoneza banja lanu. Ndipotu ngati mwamuna ndi mkazi wake amakondana komanso amatsatira malangizo a m’Baibulo, akhoza kuthetsa mavuto aakulu mosavuta. Kodi inuyo muli ndi nzeru zothetsera mavuto amene mungakumane nawo? Baibulo limanena kuti: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.”—Yakobo 1:5.

(5) Muzikhulupirika. Chigololo chimasokoneza kwambiri banja kuposa chinthu china chilichonse, ndipo Baibulo limanena kuti ngati mwamuna kapena mkazi wachita chigololo, winayo ali ndi ufulu wothetsa banja. (Mateyu 19:9) Baibulo limanenanso kuti: “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa, pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.” (Aheberi 13:4) N’chiyani chingathandize anthu okwatirana kuti asayesedwe mpaka kuchita chigololo? Baibulo limati: “Mwamuna azipereka kwa mkazi wake mangawa ake, mkazinso achite chimodzimodzi kwa mwamuna wake.”—1 Akorinto 7:3, 4.

Ena angaone kuti mfundo zisanu zimene takambiranazi n’zachikale. Koma mfundo zimenezi n’zothandiza kwambiri. Ndipotu mofanana ndi kutsatira malangizo ena a m’Baibulo, munthu amene amatsatira mfundo zimenezi zinthu zimamuyendera bwino. Baibulo limati: “Munthu ameneyo adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa mitsinje ya madzi, umene umabala zipatso m’nyengo yake, umenenso masamba ake safota, ndipo zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.”Salimo 1:2, 3.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Ngati mukufuna kuwerenga mfundo zina zokhudza banja, onani Nsanja ya Olonda ya February 1, 2011.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi Mulungu amaona bwanji nkhani yosudzulana?—Malaki 2:14-16.

● Kodi mwamuna ayenera kuchitira mkazi wake chiyani?—Aefeso 5:23, 28.

● Kuti banja liziyenda bwino, kodi tiyenera kutsatira malangizo a ndani?—Salimo 1:2, 3.