Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Makhalidwe Abwino Angakuthandizeni Kuti Muzisangalala

Makhalidwe Abwino Angakuthandizeni Kuti Muzisangalala

Mtsikana wina, dzina lake Christina, anadabwa kwambiri atapeza chikwama muli ndalama zambiri. Ndalamazo zinali zofanana ndi malipiro amene akanalandira kwa zaka 20. Popeza ankadziwa mwini wake wa chikwamacho, kodi akanatani? Nanga mukanakhala inuyo mukanatani? Yankho limene mungapereke lingasonyeze ngati muli woona mtima komanso ngati mumaona kuti kuona mtima n’kofunika kapena ayi.

Mfundo za makhalidwe abwino ndi mfundo zimene munthu amatsatira pa moyo wake chifukwa choona kuti ndi zabwino komanso zofunika. Makhalidwe amenewa ndi monga kukhululuka, kukhulupirika, chikondi, kulemekeza moyo komanso kudziletsa. Makhalidwe amene timatsatira amakhudza mbali zosiyanasiyana za moyo wathu, monga mmene timachitira zinthu, zimene timaona kuti ndi zofunika, anthu amene timacheza nawo komanso malangizo amene timapereka kwa ana athu. Ngakhale kuti makhalidwe abwino ndi ofunika, n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri alibe makhalidwe amenewa.

ANTHU ASIYA KUKHALA NDI MAKHALIDWE ABWINO

Mu 2008, akatswiri ena anachita kafukufuku kwa achinyamata a ku United States kuti adziwe mmene amaonera makhalidwe abwino. Ponena za kafukufukuyu, nyuzipepala ya The New York Times inalemba zimene David Brooks ananena. Nyuzipepalayo inanena kuti: “N’zomvetsa chisoni kuona kuti zimene achinyamata amaganiza komanso kulankhula zimasonyeza kuti samaona makhalidwe abwino kukhala ofunika.” Achinyamata ambiri amaona kuti kugwiririra komanso kupha munthu n’koipa, koma “kupatula pa zinthu zoopsa kwambiri ngati zimenezo, iwo sasiyanitsa n’komwe pakati pa makhalidwe  abwino ndi oipa. Ngakhale atamva zoti wina amayendetsa galimoto ataledzera, amabera mayeso kapenanso kuti wina akumazembera mwamuna kapena mkazi wake n’kumakachita zibwenzi, saona kuti amenewa ndi makhalidwe oipa.” Mtsikana wina ananena kuti: “Nthawi zambiri sindimalimbana nazo zoti izi n’zabwino kapena zoipa.” Anthu ambiri amayendera mfundo yoti: ‘Palibe vuto ndi kuchita chilichonse chomwe mtima wako ukufuna, bola ngati iweyo ukuona kuti n’choyenera.’ Koma kodi ndi nzeru kutsatira mfundo imeneyi?

Ngakhale kuti mtima wa munthu ukhoza kumuchititsa kuti azikonda komanso kuchitira ena zinthu mwachifundo, mtima ndi ‘wonyenga kwambiri ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.’ (Yeremiya 17:9) Timadziwa kuti zimenezi n’zoona chifukwa cha mmene anthu asinthira makhalidwe masiku ano ndipo n’zimene Baibulo linalosera. Linanena kuti: ‘M’masiku otsiriza anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, osakonda achibale awo [komanso] osadziletsa.’ Adzakhalanso “okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.”—2 Timoteyo 3:1-5.

Kudziwa kuti mtima ndi wonyenga kuyenera kutikumbutsa kuti tisamangochita chilichonse chomwe mtima wathu wafuna. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: “Munthu wodalira mtima wake ndi wopusa.” (Miyambo 28:26) Koma kuti mtima wathu uzititsogolera bwino, tikufunika kuuphunzitsa mfundo zabwino zoti uzitsatira. Kodi mfundo zimenezi tingazipeze kuti? Anthu ambiri amatsatira mfundo zopezeka m’Baibulo chifukwa zimakhala zolondola komanso zothandiza.

MFUNDO ZOMWE TIYENERA KUTSATIRA

Mfundo za makhalidwe abwino zopezeka m’Baibulo zimasonyeza kuti zinalembedwa n’cholinga choti zithandize anthu kukhala ndi moyo wabwino. Mwachitsanzo, tiyeni tikambirane makhalidwe monga chikondi, chifundo, mtima wopatsa komanso kukhulupirika.

Chikondi.

Buku lina linanena kuti: “Chimwemwe chidzabwera pakhomo panu, ngati mwaphunzira kusonyeza ena chikondi.” Zimenezi zikusonyeza kuti mwachibadwa anthufe timafuna kukondedwa. Popanda kukondana, ndiye kuti sitingakhale osangalala.—Engineering Happiness—A New Approach for Building a Joyful Life.

Zimene Baibulo limanena: “Valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” (Akolose 3:14) Munthu amene anauziridwa kulemba buku la Akolose ananenanso kuti: “Ngati . . . ndilibe chikondi, sindili kanthu.”—1 Akorinto 13:2.

Chikondi chimenechi si chimene chimakhala pakati pa mwamuna ndi mkazi, koma ndi chikondi chimene chimatsogoleredwa ndi mfundo za m’Baibulo. Chikondi chimenechi ndi chimene chingatilimbikitse kuti tithandize munthu yemwe sitikumudziwa popanda kuganizira kuti tilandirapo kenakake. Lemba la 1 Akorinto 13:4-7 limati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. Sichisunga zifukwa. Sichikondwera ndi zosalungama, koma chimakondwera ndi choonadi. Chimakwirira zinthu zonse, . . . chimapirira zinthu zonse.”

Ngati m’banja mulibe chikondi chimenechi, aliyense amavutika makamaka ana. Mwachitsanzo, mayi wina, dzina lake Monica, analemba kuti ali mwana anachitidwapo nkhanza zosiyanasiyana monga kumenyedwa komanso kugwiriridwa. Iye ananena kuti: “Ndinkaona kuti palibe amene amandikonda komanso kuti ndilibe  tsogolo lililonse.” Koma ali ndi zaka 15, Monica anayamba kukhala ndi agogo ake omwe anali a Mboni za Yehova.

Monica ananena kuti: “Ndinakhala ndi agogo anga kwa zaka ziwiri koma pa zaka zimenezo, ngakhale kuti ndinali wamanyazi, anandiphunzitsa kukonda komanso kucheza momasuka ndi anthu ndiponso kuganizira ena. Anandithandizanso kukhala munthu wodzilemekeza.” Panopa Monica anakwatiwa ndipo iye, mwamuna wake komanso ana awo atatu amasonyeza chikondi kwa ena mwa kuwaphunzitsa uthenga wa m’Baibulo.

Koma pali khalidwe lina lomwe ndi losemphana ndi khalidwe la chikondi. Khalidwe limeneli ndi kukonda ndalama. Anthu ambiri amaona kuti kukhala ndi chuma komanso katundu wochuluka n’kofunika kwambiri poyerekeza ndi chikondi. Komabe, kafukufuku amasonyeza kuti anthu amangofunikira ndalama zochepa kuti akhale ndi moyo wosangalala. Ndipo anthu amene amakonda kwambiri ndalama komanso katundu amakhala akuitana mavuto. Zimenezi n’zimene Baibulo limanena pa Mlaliki 5:10 kuti: “Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza. Zimenezinso n’zachabechabe.” Baibulo limanenanso kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama.”—Aheberi 13:5.

Chifundo komanso mtima wopatsa.

Nkhani ina imene inalembedwa ndi bungwe lina la payunivesite ya California, ku Berkeley, m’dziko la United States linanena kuti: “Kodi sizingakhale zosangalatsa kukhala ndi shopu yogulitsa chimwemwe chenicheni? Ngakhale kuti zingamveke ngati n’zosatheka, koma ndi zimene zimachitika ukamagula chinthu n’cholinga choti ukapatse munthu wina.” Mfundo yake pamenepa ndi yakuti, munthu amene wapereka mphatso kwa munthu wina ndi amene amakhala wosangalala kwambiri kuposa amene wailandirayo.

Zimene Baibulo limanena: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.

Njira yabwino kwambiri yosonyezera mtima wopatsa ndi kugwiritsa ntchito nthawi yathu komanso mphamvu zathu pothandiza ena. Mwachitsanzo, mayi wina, dzina lake Karen, anaona mzimayi ndi ana ake awiri aakazi atangokhala m’galimoto, itawawonongekera. Mzimayiyo ndi mwana wake mmodzi ankapita kukakwera ndege koma galimoto yawoyo inkakanika kulira. Karen anawauza kuti akhoza kukawasiya kokwerera ndegeko, ngakhale kuti kunali kutali moti ankafunika kuyenda mphindi 45. Atakawasiya anapeza mwana wawo wina uja akudikirirabe m’galimoto ija, kenako anayamba kucheza.

Mtsikanayo ananena kuti: “Mwamuna wanga akubwera.”

Karen anayankha kuti: “Ndasangalala kuti mwamuna wanu akubwera kudzakuthandizani. Basi, ndikupita kukakonza maluwa ku Nyumba yathu ya ufumu, kapena kuti kutchalitchi.”

Mtsikanayo anamufunsa kuti: “Ndinu wa Mboni za Yehova?”

Karen anavomera ndipo anachezako pang’ono.

Patadutsa milungu ingapo, Karen analandira kalata. Kalatayo inanena kuti: “Ineyo ndi mayi anga sitidzaiwala zimene munatichitira tsiku lija. Kupanda kutithandiza ndege ikanatithawa. Tikufuna kukuthokozani kwambiri. Mbale wanga anandiuza kuti ndinu wa Mboni za Yehova. Ndamvetsano chifukwa chake munatithandiza. Mayi anga ndi a Mboni koma ineyo ndinasiya kusonkhana komanso kulalikira. Koma ndiyesetsa kuti ndiyambirenso mwamsanga.” Karen anasangalala kwambiri kuti anathandiza Akhristu  anzake moti ananena kuti: “Zinandikhudza kwambiri mpaka ndinalira.”

Wolemba mabuku wina, dzina lake Charles D. Warner, analemba kuti: “Chinthu chokhazikitsa mtima pansi komanso chosangalatsa kwambiri . . . pa moyo wa munthu ndi kuthandiza ena, chifukwa ukamachita zimenezo umakhala ukudzithandizanso wekha.” Zimenezi n’zomveka chifukwa Mulungu anatilenga m’njira yakuti tizisonyeza makhalidwe amene iye ali nawo, osati kuti tizichita zinthu zodzikonda. (Genesis 1:27) Limodzi mwa makhalidwe amenewa ndi mtima wopatsa.

Kukhulupirika.

Khalidwe limeneli ndi lofunika kwambiri kwina kulikonse. Kusakhulupirika kumapangitsa kuti anthu azikhala mwamantha, azikayikirana komanso asamagwirizane.

Zimene Baibulo limanena: “Ndani amene angakhale mlendo m’chihema [cha Mulungu]? . . . Ndi amene akuyenda mosalakwitsa zinthu . . . ndi kulankhula zoona mumtima mwake.” (Salimo 15:1, 2) Munthu wokhulupirika amasonyeza khalidwe limeneli nthawi zonse ngakhale kuchita zimenezi kutakhala kovuta.

Kumayambiriro kwa nkhani ino tinanena za Christina yemwe anapeza chikwama cha ndalama. Cholinga chachikulu pa moyo wake chinali kusangalatsa Mulungu osati kulemera. Choncho, mwiniwake wa ndalamazo, atabwera kudzayang’ana ndalamazo, Christina anamuuza kuti zapezeka. Munthuyo anadabwa kwambiri ndi kukhulupirika kumene Christina anasonyeza. Ngakhale bwana wake anakhudzidwa kwambiri ndi zimene Christina anachitazi, moti anamukweza n’kukhala woyang’anira chipinda chosungiramo katundu. Udindo umenewu umafuna munthu wokhulupirika kwambiri. Umenewu ndi umboni wakuti mawu a pa 1 Petulo 3:10 ndi oona, omwe amati: “Amene akufuna kusangalala ndi moyo ndi kuona masiku abwino, aletse . . . milomo yake kuti isalankhule chinyengo.”

“UZIYENDA M’NJIRA YA ANTHU ABWINO”

Mfundo za makhalidwe abwino zopezeka m’Baibulo zimasonyeza kuti Mlengi wathu amatikonda chifukwa zimatithandiza kuti ‘tiziyenda m’njira ya anthu abwino.’ (Miyambo 2:20; Yesaya 48:17, 18) Ngati titatsatira malangizo amenewa tingasonyeze kuti timakonda Mulungu ndipo tidzapeza madalitso ochuluka. Ndipotu m’Baibulo muli lonjezo lakuti: “Sunga njira [za Mulungu], ndipo adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi. Pamene oipa akuphedwa, iwe udzaona.”—Salimo 37:34.

Anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo ali ndi tsogolo labwino kwambiri. Iwo adzakhala padziko lapansi pa nthawi imene anthu onse a makhalidwe oipa adzakhala atachotsedwa. Choncho ndi bwino kutsatira mfundo za makhalidwe abwino zopezeka m’Baibulo.