Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Phunzitsani Ana Anu Kuti Azigwiritsa Ntchito Intaneti Moyenera

Phunzitsani Ana Anu Kuti Azigwiritsa Ntchito Intaneti Moyenera

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Mumamva nkhani zonena kuti Intaneti ndi yoipa chifukwa anthu amaigwiritsa ntchito poopsezera anzawo, pofuna kupeza ana oti azigona nawo komanso pofuna kubera ena. Mumada nkhawa kwambiri ndi zimenezi ndipo m’pomveka, chifukwa mwana wanu amakonda kugwiritsa ntchito Intaneti ndipo amaoneka kuti sadziwa kuopsa koigwiritsa ntchito mosasamala.

Komatu dziwani kuti mungathe kuphunzitsa mwana wanu kuti azigwiritsa ntchito Intaneti moyenera. Koma choyamba, makolonu muyenera kudziwa zambiri zokhudza Intaneti.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Achinyamata angathe kulowa pa Intaneti pogwiritsa ntchito zipangizo za m’manja monga foni. Malangizo oti mwana azigwiritsa ntchito kompyuta pamalo oonekera adakali othandiza. Koma masiku ano kuli matabuleti komanso mafoni amakono. Mwana angathe kulowa pa Intaneti pogwiritsa ntchito zinthu zimenezi ndipo inuyo simungathe kudziwa zimene akuchita pa Intanetipo.

Sitinganene kuti kuyendetsa galimoto n’koipa chifukwa choti ena anachitapo ngozi. Ambiri amachita ngozi chifukwa choyendetsa galimoto mosasamala. N’chimodzimodzinso ndi Intaneti. Mwana wanu ayenera kuphunzira kuigwiritsa ntchito moyenera

Achinyamata ena amathera nthawi yambiri ali pa Intaneti. Mtsikana wina wazaka 19 anati: “Ndimayatsa kompyuta n’cholinga chongoti ndiwerenge maimelo amene anthu anditumizira. Poyamba ndimaganiza kuti zimenezi zitenga mphindi 5 zokha. Koma kenako ndimayamba kuonera mafilimu mpaka maola angapo. Ndikuona kuti ndiyenera kumadziletsa.”

Achinyamata amalemba zinthu zilizonse pa Intaneti, ngakhale zachinsinsi. Anthu oipa angathe kugwiritsa ntchito zimene wachinyamata walemba komanso zithunzi zomwe waika pa Intaneti n’kudziwa zambiri zokhudza wachinyamatayo. Mwachitsanzo angadziwe kumene iye amakhala, kumene amaphunzira komanso nthawi imene anthu a kwawo sakhala pakhomo.

Achinyamata ena sadziwa kuopsa koika zinthu pa Intaneti. Munthu akaika zinthu pa Intaneti, zimakhala pompo kwa nthawi yaitali. Pakapita nthawi anthu ena amatha kupeza zomwe munthu analemba pa Intaneti komanso zithunzi zake. Mwachitsanzo, mabwana angafufuze mbiri ya munthu amene akufuna kumulemba ntchito ndipo akhoza kupeza zinthu zimenezi.

Komabe dziwani kuti, Intaneti payokha si yoipa. Koma imakhala yoipa ngati ikugwiritsidwa ntchito molakwika.

 ZIMENE MUNGACHITE

M’phunzitseni mwana wanuyo kugwiritsa ntchito bwino nthawi. Wachinyamata ayenera kuphunzira kumachita kaye zinthu zofunika kwambiri ndipo zimenezi zidzamuthandiza akadzakula. Kucheza ndi anthu a m’banja lake, kulemba homuweki komanso kugwira ntchito zapakhomo ndi zinthu zofunika kuposa kusewera pa Intaneti. Ngati mukuona kuti mwana wanu akutha nthawi yambiri ali pa Intaneti, muikireni nthawi yoti azigwiritsa ntchito Intaneti ndipo nthawi imeneyo ikatha, azichokapo.—Lemba lothandiza: Afilipi 1:10.

M’phunzitseni mwana wanuyo kuti aziganiza kaye, asanaike zinthu pa Intaneti. Muthandizeni kuti azidzifunsa mafunso awa: Kodi zimene ndikufuna kulembazi zingakhumudwitse ena? Kodi chithunzichi chichititsa kuti anthu azindiona bwanji? Kodi makolo anga kapena anthu ena ataona zimene ndalembazi kapena chithunzi changachi, ndingachite manyazi? Kodi ataona zinthu zimenezi, angandiganizire zotani? Munthu wina atalemba zimenezi kapena kuika pa Intaneti zithunzi zoterezi, ineyo ndingamuone kuti ndi wotani?—Lemba lothandiza: Miyambo 10:23.

M’phunzitseni mwana wanuyo kuti aziyendera mfundo za m’Baibulo pa moyo wake. Simungathe kudziwa chilichonse chimene mwana wanu akuchita. Komanso udindo wanu monga kholo sikuuza mwana wanuyo chochita nthawi zonse. Udindo wanu n’kumuthandiza kuti azitha ‘kugwiritsa ntchito mphamvu zake za kuzindikira ndi kuphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’ (Aheberi 5:14) Choncho cholinga chanu chachikulu chizikhala kuphunzitsa mwana wanuyo kuti aziyendera mfundo za m’Baibulo, m’malo momangotsindika malamulo amene mukufuna kuti aziyendera komanso chilango chomwe mungamupatse. Kodi akufuna kuti anthu azimudziwa kuti ali ndi mbiri yotani? Cholinga chanu chikhale kumuthandiza kuti azisankha zinthu mwanzeru, kaya inuyo muli pompo kapena ayi.—Lemba lothandiza: Miyambo 3:21.

“Ana amadziwa zambiri zokhudza zipangizo zamakono koma makolo amadziwa zambiri zokhudza zochitika pa moyo”

Mofanana ndi kuyendetsa galimoto, kugwiritsa ntchito Intaneti kumafuna kuti munthu azisankha zinthu mwanzeru. Sikuti munthu amene amadziwa kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono, ndiye kuti basi, angasankhe zinthu mwanzeru. Choncho makolonu muli ndi udindo waukulu wothandiza mwana wanu. N’chifukwa chake katswiri wina wodziwa za kugwiritsa ntchito bwino Intaneti, dzina lake, Parry Aftab, anati: “Ana amadziwa zambiri zokhudza zipangizo zamakono koma makolo amadziwa zambiri zokhudza zochitika pa moyo.”