Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Musamagwiritse Ntchito Zipangizo Zamakono Monyanyira

Musamagwiritse Ntchito Zipangizo Zamakono Monyanyira

Amayi ena azaka 40, dzina lawo a Jenni omwenso ali ndi ana 4, amakonda kusewera magemu pakompyuta. A Jenni anati: “Ndimasewera magemu kwa maola 8 pa tsiku ndipo ndikuona kuti zafika poipa.”

A Dennis, omwe ali ndi zaka 49, pa nthawi ina anayeserapo kuti kwa masiku 7 asagwiritse ntchito zipangizo zamakono kapena Intaneti. Koma analephera moti pasanathe masiku awiri anayambanso kugwiritsa ntchito zipangizozi.

Zitsanzozi zikusonyeza kuti si achinyamata okha omwe ali ndi vuto logwiritsa ntchito zipangizo zamakono monyanyira.

KODI nanunso mumagwiritsa ntchito zipangizo zamakono? * Anthu ambiri amagwiritsa ntchito zipangizozi ndipo ena amazigwiritsa ntchito pa zinthu zofunika kwambiri. Munthu angathe kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono pogwira ntchito, pocheza ndi anzake komanso pochita zosangalatsa.

Koma monga zilili ndi a Jenni ndi a Dennis, anthu ambiri amagwiritsa ntchito zipangizozi mopitirira muyezo. Mwachitsanzo, mtsikana wina wazaka 20 dzina lake Nicole anati: “Foni yanga ndimaikonda kwambiri moti ndimaiona ngati mnzanga wapamtima. Nthawi zonse ndimaonetsetsa kuti ili pafupi. Ndimangokhalira kuyang’ana pafoni yanga kuti ndione ngati pabwera meseji. Moti ndikakhala kudera lomwe kulibe netiweki, ndimavutika kwambiri. Ndimadziwa kuti limeneli si khalidwe labwino, koma ndimalephera kusiya.”

Anthu ena amachita kudzuka usiku kuti aone ngati alandira meseji. Anthu amenewa amadwala akatha tsiku asanagwiritse ntchito foni, tabuleti kapena chipangizo chawo china. Munthu akafika pamenepa amakhala kuti sangathe kukhala popanda zipangizo zamakono.

Izi zikusonyeza kuti zipangizo zamakono, kupanda kusamala nazo zingathe kubweretsa mavuto ambiri. Mwachitsanzo zingapangitse kuti anthu m’banja asamacheze kapena kuchitira zinthu limodzi. Mtsikana wina wazaka 20 anadandaula kuti: “Bambo anga sadziwa chilichonse chomwe chikundichitikira. Amalankhula nane uku akulemba maimelo pafoni pawo. Safuna kusiyana ndi foni yawo. N’kutheka kuti amandikonda, koma zochita zawo zimaoneka ngati sandikonda kwenikweni.”

Zimene Ena Achita Pofuna Kuthetsa Vutoli

Pofuna kuthandiza anthu amene amagwiritsa ntchito zipangizo zamakono monyanyira, mayiko a China, South Korea, United Kingdom ndi United States anakhazikitsa malo oti anthu omwe ali ndi vutoli azipitako. Anthuwa akakhala kumalowa satha kugwiritsa ntchito Intaneti kapena zipangizo zamakono kwa masiku angapo. Cholinga chimakhala choti aziiwale n’kusiya kuzigwiritsa ntchito monyanyira. Mwachitsanzo, mnyamata wina dzina lake Brett, ananena kuti pa nthawi ina ankasewera magemu pa Intaneti kwa maola 16 pa tsiku. Brett anati: “Ndikayamba kusewera gemu pa Intaneti, zinkandivuta kuti ndisiye.” Vutoli linafika poipa kwambiri moti Brett anaganiza zopita kumalowo n’cholinga choti asiye kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono monyanyira. Koma pa nthawiyi n’kuti ntchito itamuthera, akuoneka wauve komanso anzake ambiri atasiya kucheza naye. Ndiye kodi mungatani kuti zoterezi zisakuchitikireni?

GANIZIRANI MMENE MUKUGWIRITSIRA NTCHITO ZIPANGIZO ZAMAKONO. Dzifunseni mafunso otsatirawa, kuti muone ngati kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono kukubweretsa mavuto pa moyo wanu.

  • Kodi ndimakwiya Intaneti ikakhala kuti sikugwira kapena ngati sindikutha kugwiritsa ntchito foni yanga, tabuleti kapena chipangizo china?

  • Kodi ndimagwiritsabe ntchito Intaneti kapena chipangizo chamakono, nthawi imene ndinadziikira kuti ndizikhala nditasiya kuchigwiritsa ntchito itadutsa?

  • Kodi ndimalephera kugona bwinobwino chifukwa choti ndimadzukadzuka kuti ndione ngati ndalandira meseji?

  • Kodi ndimalephera kucheza ndi banja langa chifukwa choti ndimatha nthawi yambiri ndikugwiritsa ntchito zipangizo zamakono? Kodi zimene ndingayankhe pa funsoli, anthu a m’banja langa angaone kuti n’zoona?

Ngati mukuona kuti zipangizo zamakono zikukulepheretsani kuchita “zinthu zofunika kwambiri” monga kusamalira banja lanu, yesetsani kuti musinthe. (Afilipi 1:10) Ndiye kodi mungatani?

DZIIKIRENI NTHAWI. Chinthu chabwinobwino chimakhala choipa ngati chikugwiritsidwa ntchito monyanyira. Choncho kaya mumagwiritsa ntchito chipangizo chamakono pogwira ntchito kapena pongofuna kusangalala, mungachite bwino kudziikira nthawi ndipo nthawiyo ikakwana muzisiya.

Tayesani izi: Uzani munthu wina wa m’banja lanu kapena mnzanu kuti akuthandizeni pa vuto lanu. Baibulo limati: “Awiri amaposa mmodzi, chifukwa . . . mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.”—Mlaliki 4:9, 10.

Musamagwiritse ntchito zipangizo zamakono monyanyira

Zipangizo zamakono zikuthandiza kuti anthu azipita pa Intaneti pomwe angathe kupeza ndi kutumiza zinthu zambiri mosavuta komanso mwachangu. Zimenezi zikupangitsa kuti anthu ena aziwononga nthawi yambiri akugwiritsa ntchito zipangizozi. Koma inuyo musalole kuti zimenezi zikuchitikireni. Muzidziwa kufunika ‘kogwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.’ (Aefeso 5:16) Izi zingakuthandizeni kuti musamawononge nthawi yambiri mukugwiritsa ntchito zipangizo zamakono.

^ ndime 5 Zipangizo zamakono zimene tikunena m’nkhaniyi ndi monga mafoni komanso zipangizo zonse zomwe tingathe kugwiritsa ntchito kutumizirana maimelo, mameseji, mavidiyo, nyimbo kapena zithunzi.