Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO

Mafunso Atatu Omwe Anthu Amafuna Atafunsa Mulungu

Mafunso Atatu Omwe Anthu Amafuna Atafunsa Mulungu

WOLEMBA mabuku wina, dzina lake Susan, anayamba kudzifunsa mafunso okhudza Mulungu ali wamng’ono. Ali ndi zaka 7 mnzake wina wa zaka 9, dzina lake Al, anadwala matenda a poliyo ndipo anagonekedwa m’chipatala china. Al ankalephera kupuma moti anaikidwa m’chimashini chothandiza kupuma. Susan analemba nkhani imeneyi m’nyuzipepala ina ya ku America ya pa January 6, 2013.—The New York Times.

Susan atapita kukaona mnzakeyo, anafunsa mayi ake kuti: “Kodi Al walakwa chiyani kuti Mulungu amupange zimenezi?”

Koma mayi ake anamuyankha kuti: “Sindikudziwa. Komanso ngati titafunsa wansembe akhoza kungotiuza kuti akudziwa ndi Mulungu yekha.”

Koma m’chaka cha 1954, dokotala wina dzina lake Jonas Salk anatulukira katemera wa mankhwala a poliyo. Pa nthawiyi n’kuti patatha zaka ziwiri Al atagonekedwa m’chipatala. Zimenezi zitachitika, mayi ake a Susan ananena kuti: ‘N’kutheka kuti ndi Mulungu amene wathandiza dokotalayu.’

Koma Susan anafunsa kuti: ‘Nanga n’chifukwa chiyani Mulungu samawathandiza madokotalawa nthawi yonseyi? Mwina akanawathandiza msanga, Al sakanaikidwa m’chimashini.’

M’nyuzipepala ija, Susan analembanso kuti: “Al anamwalira patadutsa zaka 8 zokha kuchokera pa nthawi imene mankhwala aja anapezeka. Pa nthawiyi n’kuti nditayamba kale kukhulupirira zoti kulibe Mulungu.”

Palinso anthu ena amene akumanapo ndi mavuto oopsa komanso amene aonapo anthu ena akuvutika. Anthuwa amakhala ndi mafunso ambiri okhudza Mulungu koma sapeza mayankho ake. Chifukwa cha zimenezi, ena afika posiya kukhulupirira kuti Mulungu alipo. Palinso anthu ena amene satsutsa zoti Mulungu alipo, kungoti amakayikira ngati alipodi.

Anthu ambiri amene amakayikira komanso amene sakhulupirira zoti kuli Mulungu, amakhala oti poyamba ankapemphera ndithu. Koma zimene anaona m’zipembedzo zawo n’zimene zinawachititsa kuti asiye kukhulupirira Mulungu. Amaona kuti zipembedzo zimalephera kuyankha mafunso ofunika kwambiri. Ndipo chodabwitsanso kwambiri n’choti, ngakhale anthu amene amati amakhulupirira Mulungu amadzifunsanso mafunso omwewa. Tiyeni tikambirane mafunso atatu amene anthu ambiri amalakalaka atafunsa Mulungu komanso mayankho amene Baibulo limapereka.

1 “N’CHIFUKWA CHIYANI MUMALOLA KUTI TIZIVUTIKA?”

Chifukwa chake anthu amafunsa funso limeneli

Ambiri amaona kuti ngati Mulungu ndi wachikondi, si bwenzi akulola kuti tizivutika.

TAGANIZIRANI IZI: Nthawi zina timadabwa ndi zikhalidwe komanso zimene anthu ochokera kudera lina amachita. Mwachitsanzo, m’zikhalidwe zina amaona kuti ukamalankhula ndi munthu umafunika uzimuyang’ana nkhope posonyeza kuti ukunena zoona. Pomwe m’zikhalidwe zina, amaona kuti kuchita zimenezi n’kupanda ulemu. Choncho tikakhala kuti sitikumvetsa bwino zokhudza anthu ena, ndi bwino kuphunzira ndi kudziwa bwino chikhalidwe chawo, m’malo mowaweruziratu kuti ndi anthu opanda khalidwe.

Zimenezi n’zofanananso ndi zimene zingachitike ngati sitikumvetsa zinthu zina zokhudza Mulungu. Anthu ena amanena kuti mavuto amene tikukumana nawowa ndi umboni woti Mulungu kulibe, chifukwa akanakhalako bwenzi mavutowa atawathetsa. Komabe anthu amene amamvetsa chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti tizivutika, sakayikira zoti Mulungu aliko.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Maganizo a Mulungu ndi osiyana kwambiri ndi maganizo athu. (Yesaya 55:8, 9) Chifukwa cha zimenezi nthawi zina zimativuta kumvetsa chifukwa chake Mulungu amalola kuti zinthu zinazake zizichitika.

Komabe, Baibulo silitiuza kuti tizingoyendera maganizo a anthu ena omwe amanena kuti: “Palibe amene angamvetse zochita za Mulungu.” Koma limatilimbikitsa kuti tiziphunzira kuti timudziwe bwino. Zimenezi zingatithandize kuti tizimumvetsa komanso kuti akhale mnzathu. *Yakobo 4:8.

2 “N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU AMBIRI OPEMPHERA AMACHITA ZACHINYENGO?”

Chifukwa chake anthu amafunsa funso limeneli

Anthu ena amaona kuti ngati Mulungu amafuna kuti anthu azikhala okhulupirika, si bwenzi m’zipembedzomu anthu achinyengo ali tho!

TAGANIZIRANI IZI: Tiyerekeze kuti mwana wina wakana kutsatira malangizo a bambo ake ndipo akuchoka pakhomo n’kukayamba moyo wolowerera. Ngakhale kuti bambowo sakugwirizana ndi maganizo a mwanayo, akumulola kuchita zomwe akufuna. Kodi zingakhale zomveka anthu atamanena kuti mwanayo analowerera chifukwa chakuti bambo ake ndi oipa? Kapena kodi zingakhale zomveka atamanena kuti mwanayo alibe bambo ake? Ayi. Mofanana ndi bamboyu, Mulungu amawapatsa anthu ufulu wosankha zomwe akufuna kuchita. Komanso sitinganene kuti Mulungu ndi woipa kapena kuti kulibe, chifukwa cha zachinyengo zimene anthu opemphera amachita.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Ngakhale kuti Mulungu amapatsa anthu ufulu wochita zimene akufuna, amanyansidwa kwambiri ndi zinthu zachinyengo zomwe anthu opemphera amachita. (Yeremiya 7:29-31; 32:35) Ndipotu anthu ambiri omwe amanena kuti amakhulupirira Mulungu, amangotsatira ziphunzitso komanso mfundo zachipembedzo zomwe anthu anakhazikitsa okha.—Mateyu 15:7-9.

Koma mosiyana ndi anthu amenewa, anthu amene ali m’chipembedzo chimene Mulungu amasangalala nacho sachita zachinyengo. * Yesu ananena kuti: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yohane 13:35.) Ndipo Baibulo limanena kuti chikondi chimenechi ‘chisamakhale chachiphamaso.’ (Aroma 12:9) Anthu ambiri omwe ndi opemphera satsatira zimenezi. Mwachitsanzo, pa nkhondo yomwe inachitika ku Rwanda mu 1994, anthu ambiri opemphera anapha anthu achipembedzo chawo chifukwa chosiyana mitundu. Koma a Mboni za Yehova sankachita zimenezi. Ankaika moyo wawo pangozi pofuna kupulumutsa a Mboni anzawo komanso anthu ena. Zimene ankachitazi zikusonyeza kuti pali anthu ena opemphera omwe ndi opanda chinyengo.

3 “N’CHIFUKWA CHIYANI MUNATILENGA?”

Chifukwa chake anthu amafunsa funso limeneli

Anthu ambiri amadabwa kuti: ‘N’chifukwa chiyani timangokhala ndi moyo zaka 80 kapena 90 zokha basi? N’chifukwa chiyani moyo wathu uli waufupi chonchi?’

TAGANIZIRANI IZI: Ngakhale kuti anthu ena sakhulupirira Mulungu, komabe amagoma kwambiri akaona mmene chilengedwechi chilili. Amaona kuti dziko lapansili, mwezi komanso mapulaneti ena zimayenda mwadongosolo, zimene zimathandiza kuti padzikoli pazikhala zamoyo. Amaonanso kuti padzikoli sipakanakhala chamoyo chilichonse zikanakhala kuti mapulaneti sayenda mwadongosolo.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Anthu ena amaona kuti chifukwa chakuti moyo wathu ndi waufupi, ndiye kuti kulibe Mulungu. Komabe pali zinthu zambiri zomwe timaziona m’chilengedwechi zimene zimasonyeza kuti kuli Mulungu. (Aroma 1:20) Zimasonyezanso kuti Mulungu anali ndi cholinga chinachake polenga zinthuzi. Iye analenga zinthu zonsezi n’cholinga choti anthu adzakhale ndi moyo wosatha padzikoli ndipo cholinga chakechi sichinasinthe.—Salimo 37:11, 29; Yesaya 55:11.

Kuganizira zimene Mulungu analenga kungatithandize kuti tizikhulupirira zoti alikodi komanso kuti timudziwe bwino. Komabe sikuti chilengedwechi chingatithandize kudziwa zonse zokhudza Mulungu komanso zimene amafuna. Mulungu anatipatsa Mawu ake Baibulo n’cholinga choti tidziwe zimene amafuna komanso chifukwa chimene anatilengera. * A Mboni za Yehova akukupemphani kuti muziphunzira nawo Baibulo kuti mudziwe mfundo zina zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.

^ ndime 17 Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu amalola kuti tizivutika, onani mutu 11 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli ndi lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.dan124.com/ny

^ ndime 23 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 15 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova. Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.dan124.com/ny.

^ ndime 29 Kuti mudziwe zambiri, onani mutu 3 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova. Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.dan124.com/ny.