Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 15

Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza

Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
  • Kodi zipembedzo zonse zimachita zimene Mulungu amakondwera nazo?

  • Kodi chipembedzo choona tingachidziwe bwanji?

  • Kodi ndi ndani masiku ano amene akulambira Mulungu m’njira yovomerezeka?

1. Kodi tingapeze madalitso otani tikamalambira Mulungu m’njira yovomerezeka?

YEHOVA MULUNGU amatikonda kwambiri ndipo amatitsogolera n’cholinga choti zinthu zitiyendere bwino. Ngati timamutumikira m’njira yovomerezeka tingakhale osangalala komanso tingapewe mavuto ambiri. Kuwonjezera pamenepo Yehova akhoza kutidalitsa komanso kutithandiza. (Yesaya 48:17) Komabe pali zipembedzo zambirimbiri zimene zimati zimathandiza anthu kumudziwa Mulungu molondola. Komatu zimene zipembedzo zimenezi zimaphunzitsa zimasiyana kwambiri pa nkhani yakuti Mulungu ndi ndani ndipo amafuna kuti tizichita zotani.

2. Kodi tingadziwe bwanji njira yoyenera yolambirira Yehova, nanga ndi chitsanzo chiti chimene chingatithandize kumvetsa zimenezi?

2 Kodi mungadziwe bwanji njira yoyenera yolambirira Yehova? Simukufunikira kuchita kuphunzira zimene zipembedzo zonse zimaphunzitsa kenako n’kuona kuti zolondola ndi ziti. Mukungofunikira kuphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni pa nkhani ya chipembedzo choona. Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiyerekezere motere: M’mayiko ambiri anthu amapezeka ndi ndalama zachinyengo. Ngati mutapatsidwa ntchito yoti mufufuze ndalama zachinyengozo, kodi mungatani kuti muzitha kuzizindikira? Kodi mungafunikire kuloweza mmene ndalama iliyonse yachinyengo imaonekera? Ayi, kuchita zimenezi kungakhale kungowononga nthawi. Mungachite bwino kungodziwa mmene ndalama yeniyeni imaonekera. Kudziwa mmene ndalama yeniyeni imaonekera kungakuthandizeni kudziwa mosavuta ndalama yachinyengo. Mofanana ndi zimenezi, tikadziwa chipembedzo choona, tingathenso kuzindikira mosavuta chipembedzo chonyenga.

3. Malinga ndi zimene Yesu ananena, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti kulambira kwathu kukhale kovomerezeka?

3 Kulambira Yehova m’njira imene amavomereza n’kofunika kwambiri. Anthu ambiri amakhulupirira kuti zipembedzo zonse zimakondweretsa Mulungu, koma si zimene Baibulo limaphunzitsa. Komanso kungonena kuti ndiwe Mkhristu sikokwanira. Yesu anati: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa Ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.” Choncho kuti Mulungu avomereze kulambira kwathu, tiyenera kuphunzira zimene amafuna n’kumazichita. Yesu ananena kuti anthu amene sachita zimene Mulungu amafuna ndi “anthu osamvera malamulo.” (Mateyu 7:21-23) Mofanana ndi ndalama zachinyengo, zomwe zilibe ntchito iliyonse, nachonso chipembedzo chonyenga sichingathandize munthu. Ndipotu zipembedzo ngati zimenezi n’zoopsa.

4. Kodi mawu a Yesu onena za misewu iwiri amatanthauza chiyani, nanga kodi misewuyi ndi yopita kumalo amodzi?

4 Yehova anapereka mwayi kwa wina aliyense padziko lapansi woti akhoza kupeza moyo wosatha. Komabe, kuti tidzakhale ndi moyo wosatha m’Paradaiso, tiyenera kumalambira Mulungu m’njira yoyenera komanso kumachita zinthu zimene amasangalala nazo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri safuna kuchita zimenezi. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Lowani pachipata chopapatiza. Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuchiwonongeko, ndipo anthu ambiri akuyenda mmenemo. Koma chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Chipembedzo choona chimathandiza anthu kuti adzapeze moyo wosatha. Koma chipembedzo chonyenga chimasokoneza anthu zomwe zidzachititse kuti adzawonongedwe. Yehova samafuna zoti munthu wina aliyense adzawonongedwe, ndipo n’chifukwa chake akupereka mwayi kwa anthu onse kuti amudziwe. (2 Petulo 3:9) Choncho zimene timachita polambira Mulungu zikhoza kuchititsa kuti tidzapeze moyo wosatha kapena tidzawonongedwe.

KODI CHIPEMBEDZO CHOONA TINGACHIDZIWE BWANJI?

5. Kodi anthu amene ali m’chipembedzo choona tingawadziwe bwanji?

5 Kodi tingachidziwe bwanji chipembedzo choona, kapena kuti msewu wolowera ku moyo? Yesu ananena kuti tingadziwe chipembedzo choona poyang’ana zimene anthu amene ali m’chipembedzocho amachita. Iye anati: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. . . . Mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino.” (Mateyu 7:16, 17) M’mawu ena tinganene kuti anthu amene ali m’chipembedzo choona tingawadziwe poona zimene amakhulupirira komanso khalidwe lawo. Ngakhale kuti nawonso ndi ochimwa, anthu amene ali m’chipembedzo choona amayesetsa kuchita zimene Mulungu amafuna. Tiyeni tikambirane zinthu 6 zimene zingatithandize kudziwa anthu amene ali m’chipembedzo choona.

6, 7. Kodi atumiki a Mulungu amaliona bwanji Baibulo, nanga Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani imeneyi?

6 Zimene atumiki a Mulungu amaphunzitsa zimachokera m’Baibulo. Baibulo limanena kuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera bwino ndi wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteyo 3:16, 17) Mtumwi Paulo analembera Akhristu anzake kuti: “Pamene munalandira mawu a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandire monga mawu a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu.” (1 Atesalonika 2:13) Choncho, zinthu zimene anthu amene ali m’chipembedzo choona amakhulupirira komanso kuchita zimachokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Iwo sachita zinthu pongotsatira maganizo a anthu, kapena chikhalidwe cha m’dera lawo.

7 Yesu Khristu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi chifukwa zonse zimene ankaphunzitsa zinkachokera m’Mawu a Mulungu. Pamene ankapemphera kwa Atate ake, ananena kuti: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yohane 17:17) Yesu ankakhulupirira Mawu a Mulungu, n’chifukwa chake zilizonse zimene ankaphunzitsa zinkagwirizana ndi mfundo za m’Malemba. Nthawi zambiri Yesu ankanena kuti: “Malemba amati.” (Mateyu 4:4, 7, 10) Akatero ankatchula mawu a palemba linalake. Mofanana ndi zimenezi, anthu a Mulungu masiku ano saphunzitsa zinthu za m’maganizo mwawo. Iwo amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu, ndipo zonse zimene amaphunzitsa zimachokera m’Baibulo.

8. Kodi kulambira Yehova kumaphatikizapo chiyani?

8 Anthu amene ali m’chipembedzo choona amalambira Yehova yekha ndiponso amauza ena za dzina lake. Yesu ananena kuti: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.” (Mateyu 4:10) Choncho, atumiki a Mulungu amalambira Yehova yekha basi. Zimenezi zimaphatikizapo kuthandiza anthu kuti adziwe dzina la Mulungu ndiponso makhalidwe ake. Lemba la Salimo 83:18 limati: “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” Yesu ankathandizanso anthu kudziwa Mulungu, n’chifukwa chake ananena m’pemphero kuti: “Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndawadziwitsa dzina lanu.” (Yohane 17:6) Potsatira chitsanzo chimenechi, atumiki a Mulungu masiku ano amaphunzitsa anthu ena dzina la Mulungu, zolinga zake ndiponso makhalidwe ake.

9, 10. Kodi Akhristu oona amasonyezana chikondi m’njira ziti?

9 Atumiki a Mulungu amasonyezana chikondi chenicheni, osati chachinyengo. Yesu ananena kuti: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yohane 13:35) Akhristu oyambirira ankasonyezana chikondi choterechi. Chikondi chenicheni chimathandiza anthu kuti azigwirizana ngakhale atakhala kuti ndi osiyana mitundu, chikhalidwe, maphunziro ndiponso kapezedwe ka chuma. Iwo amagwirizana kwambiri ngati anthu a banja limodzi. (Werengani Akolose 3:14.) Koma anthu a m’zipembedzo zonyenga sagwirizana choncho. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Iwo amaphana chifukwa chosiyana mitundu kapena mayiko. Koma Akhristu oona satenga zida kuti akaphe Akhristu anzawo kapena wina aliyense. Baibulo limanena kuti: “Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyerekezi amaonekera bwino ndi mfundo iyi: Aliyense amene sachita zolungama sanachokere kwa Mulungu, chimodzimodzinso amene sakonda m’bale wake. . . . Tizikondana, osati ngati Kaini, amene anachokera kwa woipayo n’kupha m’bale wake.”—1 Yohane 3:10-12; 4:20, 21.

10 Komatu chikondi chenicheni sichimatanthauza kungopewa kupha anthu ena. Akhristu oona sadzikonda, moti amagwiritsa ntchito nthawi yawo, mphamvu zawo ndi chuma chawo pothandiza ndiponso kulimbikitsa anzawo. (Aheberi 10:24, 25) Iwo amathandizana pa nthawi ya mavuto komanso amakhala oona mtima. Akhristu oona amatsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Tiyeni tichitire onse zabwino.”—Agalatiya 6:10.

11. N’chifukwa chiyani tifunika kukhulupirira kuti Yesu Khristu ndi njira ya Mulungu yotipulumutsira?

11 Akhristu oona amakhulupirira kuti Yesu Khristu ndi njira ya Mulungu yopulumutsira anthu. Baibulo limanena kuti: “Chipulumutso sichipezeka mwa munthu wina aliyense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo, limene laperekedwa kwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 4:12) Monga mmene tinaonera m’Mutu 5, Yesu anapereka moyo wake ngati dipo n’cholinga choti apulumutse anthu omvera. (Mateyu 20:28) Kuwonjezera pamenepa, Yesu anasankhidwa ndi Mulungu kukhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba womwe udzalamulire dziko lonse lapansi. Ndipo Mulungu amafuna kuti tizimvera Yesu komanso kutsatira zimene amaphunzitsa ngati tikufuna kudzakhala ndi moyo wosatha. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: “Wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha. Wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu.”—Yohane 3:36.

12. Kodi kusalowerera m’zochitika za dziko kumatanthauza chiyani?

12 Akhristu oona salowerera nawo m’zochitika za m’dzikoli. Pamene ankazengedwa mlandu pamaso pa Pilato, Yesu ananena kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Kaya amakhala m’dziko liti, Akhristu onse oona ndi nzika za Ufumu wakumwamba, choncho salowerera nawo ndale za m’dziko limene amakhala. Iwo salowereranso m’mikangano ya ndale. Komabe atumiki a Yehova saletsa anthu ena amene akufuna kulowa chipani chinachake, kupikisana nawo pa chisankho kapena kuvota. Komanso, ngakhale kuti salowerera nawo m’ndale, iwo amamvera malamulo a boma. Iwo amachita zimenezi chifukwa Mawu a Mulungu amawalamula kuti “azimvera olamulira akuluakulu,” kapena kuti boma. (Aroma 13:1) Koma nthawi zina malamulo amene boma limakhazikitsa amatsutsana ndi zimene Mulungu amafuna. Zikatero, Akhristu oona amatsatira chitsanzo cha atumwi, omwe ananena kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”—Machitidwe 5:29; Maliko 12:17.

13. Kodi otsatira oona a Yesu amauona bwanji Ufumu wa Mulungu, ndipo amachita chiyani?

13 Akhristu oona amalalikira zoti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungathetse mavuto omwe anthu akukumana nawo. Yesu ananeneratu kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) M’malo molimbikitsa anthu kudalira atsogoleri awo kuti ndi amene angawathetsere mavuto, otsatira oona a Yesu Khristu amalalikira kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetse mavuto onse a anthu. (Salimo 146:3) Yesu anatiphunzitsa kuti tizipempherera Ufumu umenewu pamene ananena kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Mawu a Mulungu ananeneratu kuti Ufumu wakumwamba umenewu “udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo [amene alipowa], ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”—Danieli 2:44; Chivumbulutso 16:14; 19:19-21.

14. Kodi ndi gulu liti lachipembedzo limene mukuona kuti limachita zonse zofunika pa kulambira koona?

14 Malinga ndi zimene takambiranazi, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi chipembedzo chiti chimene chimaphunzitsa mfundo zochokera m’Baibulo zokhazokha ndiponso kuthandiza anthu kudziwa dzina la Yehova? Komanso ndi chipembedzo chiti chimene anthu ake amasonyezana chikondi chenicheni, amakhulupirira Yesu, salowerera nawo m’zochitika za m’dzikoli komanso amalalikira kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungathetse mavuto amene anthu akukumana nawo? Pa zipembedzo zonse zimene zili padziko lapansili, ndi chipembedzo chiti chimene chimachita zonse zomwe takambiranazi?’ Umboni ukusonyezeratu kuti ndi Mboni za Yehova.—Werengani Yesaya 43:10-12.

ZOMWE MUYENERA KUCHITA

15. Kuwonjezera pa kukhulupirira kuti Mulungu aliko, kodi iye amafunanso kuti tizichita chiyani?

15 Kungokhulupirira kuti kuli Mulungu sikokwanira kuti Mulunguyo azisangalala nafe chifukwa ngakhale ziwandanso zimakhulupirira kuti Mulungu aliko. (Yakobo 2:19) Koma ngakhale zimakhulupirira kuti Mulungu aliko, sizichita zimene Mulungu amafuna ndipo iye sasangalala nazo. Kuti tikondweretse Mulungu, sitiyenera kungokhulupirira kuti aliko koma tiyeneranso kuchita zimene amafuna. Tiyeneranso kutuluka m’chipembedzo chonyenga, n’kulowa m’chipembedzo choona.

16. Kodi tiyenera kuchita nawo miyambo ya chipembedzo chonyenga?

16 Mtumwi Paulo anasonyeza kuti sitiyenera kugwirizana ndi chipembedzo chonyenga. Iye analemba kuti: “‘Tulukani pakati pawo, lekanani nawo,’ watero Yehova. ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa,’ ‘ndipo ndidzakulandirani.’” (2 Akorinto 6:17; Yesaya 52:11) Choncho Akhristu oona amapewa chilichonse chokhudzana ndi kulambira konyenga.

17, 18. Kodi “Babulo Wamkulu” n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani muyenera kutulukamo mwamsanga?

17 Baibulo limasonyeza kuti “Babulo Wamkulu” amaimira zipembedzo zonse zonyenga. * (Chivumbulutso 17:5) Dzina limeneli limatikumbutsa za mzinda wakale wa Babulo komwe kunayambira kulambira konyenga pambuyo pa Chigumula cha nthawi ya Nowa. Zinthu zimene chipembedzo chonyenga chimaphunzitsa komanso zimene anthu ake amachita zinayamba kalekale mumzinda wa Babulo. Mwachitsanzo, milungu imene anthu a ku Babulo ankalambira inkakhala itatuitatu. Masiku anonso, zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi. Koma Baibulo limaphunzitsa momveka bwino kuti kuli Mulungu woona m’modzi yekha, yemwe ndi Yehova, ndipo Yesu Khristu ndi Mwana wake. (Yohane 17:3) Ababulo ankakhulupiriranso kuti mzimu wa munthu sufa munthuyo akamwalira. Iwo ankanena kuti munthu akamwalira mzimu wake umatuluka ndipo umatha kupita kumalo ena komwe umakazunzika. Masiku anonso zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti munthu ali ndi mzimu umene sufa ndipo umatha kukazunzika kumoto.

18 Popeza miyambo ya chipembedzo imene anthu a ku Babulo ankachita inafalikira padziko lonse lapansi, n’zomveka kunena kuti panopa Babulo Wamkulu akuimira zipembedzo zonse zonyenga. Mulungu ananeneratu kuti zipembedzo zonsezi zidzatha mwadzidzidzi. Mwina pamenepa mukuona chifukwa chake ndi bwino kusiyiratu kugwirizana ndi Babulo Wamkulu. Yehova Mulungu akufuna kuti ‘mutulukemo’ mwamsanga nthawi idakalipo.—Werengani Chivumbulutso 18:4, 8.

Mukamatumikira Yehova limodzi ndi anthu ake, mudzapeza madalitso ambiri kuposa zimene mungataye

19. Kodi mungapeze madalitso otani chifukwa chosankha kutumikira Yehova?

19 Ngati mutasiya kugwirizana ndi chipembedzo chonyenga, anthu ena akhoza kusiya kucheza nanu. Koma kugwirizana ndi anthu amene amatumikira Yehova, kungachititse kuti mupeze madalitso ambiri oposa zinthu zimene mungataye. Mofanana ndi ophunzira a Yesu amene anasiya zinthu zawo n’kuyamba kumutsatira, mudzapeza anthu ambiri amene azidzakukondani ngati achibale anu enieni. Mudzalowa m’gulu lalikulu la Akhristu oona omwe amakondana kwambiri ngati anthu a banja limodzi. Gulu limeneli likupezeka padziko lonse lapansi. Kuwonjezera pamenepa, mukhoza kudzakhala ndi moyo wosatha ‘nthawi imene ikubwerayo.’ (Werengani Maliko 10:28-30.) N’kutheka kuti m’tsogolo anthu amene angasiye kucheza nanuwo akhoza kudzaphunzira zimene Baibulo limanena nawonso n’kuyamba kulambira Yehova.

20. Kodi anthu amene ali m’chipembedzo choona zinthu zidzawayendera bwanji?

20 Baibulo limaphunzitsa kuti posachedwapa Mulungu awononga dziko loipali ndipo lidzalowedwa m’malo ndi dziko latsopano lolungama limene lizidzalamulidwa ndi Ufumu wake. (2 Petulo 3:9, 13) Limenelitu lidzakhala dziko labwino kwambiri. M’dziko limeneli mudzakhala chipembedzo chimodzi chokha, chomwe ndi chipembedzo choona. Choncho kodi simukuona kuti ndi nzeru kutuluka m’chipembedzo chonyenga panopa n’kulowa chipembedzo choona?

^ ndime 17 Kuti mumve chifukwa chake Babulo Wamkulu amaimira zipembedzo zonse zonyenga, onani Zakumapeto, tsamba 219-220.