GALAMUKANI! Na. 1 2019 | Kodi Tingadzakhaledi Otetezeka Padzikoli?

Werengani magaziniyi kuti mudziwe mavuto ena omwe tikulimbana nawo komanso zomwe zingadzathandize kuti dzikoli lidzakhale malo abwino komanso otetezeka.

Zomwe Zikuchititsa Kuti Tikhale Osatetezeka

Panopo m’pamene tikukhala mosatetezeka kwenikweni poyerekeza ndi m’mbuyomo. Kodi pali njira yothetsera vutoli?

Kudziwa Chimene Chikuyambitsa Mavuto

Mavuto ambiri omwe timakumana nawo, amachitika chifukwa chakuti anthufe ndi ochimwa. Koma kodi ndi ndani angatithandize?

Maphunziro Okhudza Makhalidwe Abwino

Makhalidwe abwino angatithandize kuti tikhale pamtendere ndi anzathu komanso kukhala otetezeka

Nkhani ya Ricardo ndi Andres

Poyamba Ricardo ndi Andres ankasowetsa anthu ena mtendere koma panopo amalimbikitsa anthu kukhala pa mtendere ndi anzawo. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene Baibulo linasinthira moyo wawo.

“Ndipo Mtendere Sudzatha”

Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?

Ufumu wa Mulungu Ukamadzalamulira “Padzakhala Mtendere Wochuluka”

Ufumu wa Mulungu udzabweretsa mtendere komanso mgwirizano padziko lonse lapansi.

Kodi Munayamba Mwadzifunsapo?

Kodi mungapeze bwanji mayankho a mafunso amene mumakhala nawo?