Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Munayamba Mwadzifunsapo?

Kodi Munayamba Mwadzifunsapo?
  • Ngati Mulungu amatikondadi, n’chifukwa chiyani amalola kuti tizivutika ndipo n’chifukwa chiyani sakuthetsa mavutowa mpaka pano?

  • Kodi tingatsimikize bwanji kuti tikukhaladi m’masiku otsiriza?

  • Kodi timadziwa bwanji kuti zimene Baibulo linalonjeza zokhudza Ufumu wa Mulungu zidzachitikadi?

  • Kodi mfundo za m’Baibulo zingatithandize tikamasankha zochita panopa?

Mlengi wathu amatikonda kwambiri ndipo watithandiza kupeza mayankho a mafunso amenewa ndi enanso ambiri. Kuti mupeze mayankhowa pitani pawebusaiti yathu ya jw.org. Webusaitiyi inakonzedwa ndi cholinga chothandiza anthu kuphunzira Baibulo.

Pawebusaitiyi mungathe kupezaponso mavidiyo, zinthu zongomvetsera, zochitika pa moyo wa anthu ena, mabuku osiyanasiyana komanso Baibulo. Mungathe kupanga dawunilodi zinthu zonsezi kwaulere.