Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pafupifupi anthu a m’zipembedzo zonse amakhulupirira kuti munthu ali ndi mzimu umene suufa

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI BAIBULO LIMANENA ZOTANI PA NKHANI YA IMFA?

Kodi Munthu Akamwalira Amakakhalanso Ndi Moyo Kwinakwake?

Kodi Munthu Akamwalira Amakakhalanso Ndi Moyo Kwinakwake?

ANTHU ali ndi maganizo osiyanasiyana pa zimene zimachitika munthu akamwalira. Ena amaganiza kuti munthu akafa, amakapitirizabe kukhala ndi moyo kwinakwake kapena amasanduka chinachake. Pomwe ena amaganiza kuti munthu akafa amakabadwanso kwina. Ndiye pali enanso amene amakhulupirira kuti munthu akafa, ndiye kuti basi zonse zathera pomwepo.

Mwina inunso muli ndi zimene mumakhulupirira pa nkhaniyi potengera kumene munakulira komanso chikhalidwe chanu. Monga taonera, anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira. Ndiye funso n’kumati: ‘Kodi pali munthu kapena buku limene lingatithandize kudziwa zolondola pa nkhaniyi?’

Kwa zaka zambiri atsogoleri azipembedzo akhala akuphunzitsa kuti munthu ali ndi mzimu umene suufa. Pafupifupi anthu a m’zipembedzo zonse zikuluzikulu, monga Chikhristu, Chihindu, Chiyuda komanso Chisilamu, amakhulupirira kuti munthu akafa mzimu wake umapita kudziko la mizimu kapena kumwamba. Pamene Abuda amakhulupirira kuti munthu akafa amabadwanso kambirimbiri mpaka kenako amakhala ndi moyo wopanda nkhawa womwe amautchula kuti Nirvana.

Ziphunzitso zimenezi zachititsa kuti anthu ambiri padziko lonse azikhulupirira kuti imfa ndi chiyambi cha moyo wina. Ambiri amaona kuti imfa imayenera kuchitika ndithu pa moyo wa munthu, ndipo Mulungu ndi amene anakonza zoti anthu azifa. Koma kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi? Tikukupemphani kuti muwerenge nkhani yotsatira kuti mupeze yankho la funsoli. Mungadabwe ndi zimene Baibulo limanena.