Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kudziwa Dzina la Mulungu Kumatanthauza Chiyani?

Kodi Kudziwa Dzina la Mulungu Kumatanthauza Chiyani?

KODI dzina lanu lili ndi tanthauzo linalake? M’mayiko ena anthu amakonda kupatsa mwana dzina latanthauzo. Dzinalo lingasonyeze zimene makolo ake amakhulupirira, zimene amakonda komanso zimene akuyembekezera kuti mwanayo adzachite m’tsogolo.

Kupatsa ana mayina atanthauzo sikunayambe lero. Kale kwambiri, Baibulo likulembedwa, anthu ankapatsidwa mayina chifukwa cha tanthauzo la dzinalo. Dzina la munthu linkasonyeza zimene munthuyo adzachite m’tsogolo. Mwachitsanzo, Yehova pouza Davide zimene mwana wake Solomo adzachite m’tsogolo, ananena kuti: “Dzina lake lidzakhala Solomo [kuchokera ku mawu otanthauza “Mtendere”]; ndipo ndidzapatsa Isiraeli mtendere ndi bata masiku ake.”​—1 Mbiri 22:9.

Nthawi zina Yehova ankasintha dzina la munthu chifukwa cha udindo watsopano umene wam’patsa. Mwachitsanzo mkazi wa Abulahamu, amene anali wosabereka, anam’patsa dzina lakuti Sara, kutanthauza “Mfumukazi.” N’chifukwa chiyani anam’patsa dzina limeneli? Yehova anafotokoza kuti: “Ndidzam’dalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzam’dalitsa iye, ndipo adzakhala amake a mitundu, mafumu a anthu adzatuluka mwa iye.” (Genesis 17:16) Kumvetsa udindo watsopano umene Sara anapatsidwa kungatithandize kumvetsa chifukwa chake Sara anapatsidwa dzinali.

Nanga bwanji za dzina lakuti Yehova limene ndi lofunika kwambiri kuposa mayina ena onse? Kodi dzinali limatanthauza chiyani? Mose atafunsa Mulungu dzina lake, Yehova anayankha kuti: “Ine ndine yemwe ndili ine.” (Eksodo 3:14) Palembali, Baibulo la New World Translation limati: “Ndidzakhala amene ndidzafune kukhala.” Dzina la Yehova limasonyeza kuti Mulungu angagwire ntchito zosawerengeka. Kuti timvetse mfundo imeneyi taganizirani za mayi. Iye angakhale ndi ntchito zambiri patsiku zoti achite posamalira ana ake. Angafunike kukhala nesi, wophika, kapenanso mphunzitsi, malinga ndi zimene zikufunika panthawiyo. N’chimodzimodzinso Yehova. Komabe iye amachita zambiri kuposa mayi. Kuti akwaniritse zimene amafuna kuchitira anthu chifukwa chowakonda, iye angathe kukhala aliyense amene angafune kukhala. Choncho kudziwa dzina la Yehova kumatanthauza kumvetsa ndiponso kulemekeza ntchito zake zambiri zimene amachita.

Chomvetsa chisoni ndi chakuti, anthu sadziwa makhalidwe abwino a Mulungu chifukwa chakuti sadziwa dzina lake. Koma kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni kudziwa maudindo a Yehova monga Mlangizi wanzeru, Mpulumutsi wamphamvu, komanso Mulungu amene amatipatsa zimene timafuna. Dzina la Yehova limatanthauza zambiri ndipo zimenezi zimatichititsa kuti tizimulemekeza kwambiri.

Komabe, nthawi zina kudziwa dzina la Mulungu kumakhala kovuta. Nkhani yotsatira ifotokoza chifukwa chake.