Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’zotheka Kulidziwa Dzina la Mulungu?

Kodi N’zotheka Kulidziwa Dzina la Mulungu?

Munthu waudindo akakuuza kuti uzimutchula dzina lake lenileni umakhala mwayi waukulu. Kawirikawiri anthu olemekezeka amaitanidwa ndi mayina monga “A Pulezidenti,” “Bwana,” ndiponso “Olemekezeka.” Choncho munthu wina waudindo waukulu atakuuzani kuti, “Uzinditchula dzina langa,” mukhoza kuona kuti wakulemekezani kwambiri.

MULUNGU woona amatiuza m’Mawu ake, Baibulo, kuti: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli.” (Yesaya 42:8) Mulungu ali ndi mayina ambiri omulemekezera monga, “Mlengi,” “Wamphamvuyonse,” ndiponso “Ambuye Mfumu.” Koma iye nthawi zonse amalemekeza atumiki ake okhulupirika powalola kuti azimutchula dzina lake lenileni.

Mwachitsanzo, panthawi ina Manowa pochonderera kwa Mulungu anayamba ndi mawu akuti: “Yehova, ndikupemphani.” (Oweruza 13:8) Ku Yerusalemu, pa mwambo wopereka kachisi kwa Mulungu, Mfumu Solomo inayamba pemphero lake ndi mawu akuti: “Yehova Mulungu.” (1 Mafumu 8:22, 23) Ndiponso pamene mneneri Yesaya anapemphera kwa Mulungu m’malo mwa Aisiraeli, ananena kuti: “Inu Yehova ndinu Atate wathu.” (Yesaya 63:16) Zimenezi zikusonyezeratu kuti Atate wathu wakumwamba amafuna kuti tizimutchula dzina lake lenileni.

Ngakhale kuti kumutchula Mulungu dzina lake lakuti Yehova n’kofunika, pamafunika zambiri kuti timudziwe bwino. Ponena za munthu amene amakonda ndi kukhulupirira Mulungu, Yehova amalonjeza kuti: “Ndidzam’kweza m’mwamba [Ndidzamuteteza], popeza adziwa dzina langa.” (Salmo 91:14) Zimenezi zikutanthauza kuti kudziwa dzina la Mulungu kumafuna zambiri chifukwa ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri kuti azititeteza. Ndiyeno kodi inuyo mufunikira kuchita chiyani kuti mumudziwe bwino Yehova?