Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ANTHU AMENE ANAMWALIRA ADZAKHALANSO NDI MOYO?

Kodi Akufa Angadzakhalenso ndi Moyo?

Kodi Akufa Angadzakhalenso ndi Moyo?

Kodi akufa angadzakhalenso ndi moyo?

YANKHO LA M’BAIBULO: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake [a Yesu] ndipo adzatuluka.”Yohane 5:28, 29.

Pa lembali, Yesu ankalonjeza kuti akadzayamba kulamulira monga Mfumu padzikoli, adzaukitsa anthu amene anamwalira. Fernando amene watchulidwa m’nkhani yapitayi anati: “Nditawerenga koyamba lemba la Yohane 5:28, 29, ndinasangalala kwambiri. Lembali linandithandiza kukhala ndi chikhulupiriro chakuti akufa adzakhalanso ndi moyo ndipo ndinayamba kuganizira kwambiri mmene moyo udzakhalire wosangalatsa mtsogolo.”

Yobu ankakhulupirira kuti akamwalira, Mulungu adzamuukitsa. Iye anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” Yobu anayankha yekha funsoli ndipo anati: “Ndidzadikira masiku onse a ntchito yanga yokakamiza [nthawi yomwe ndili m’Manda], mpaka mpumulo wanga utafika. Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha.”—Yobu 14:14, 15.

Nkhani ya kuukitsidwa kwa Lazaro, imatitsimikizira kuti akufa adzakhalanso ndi moyo

Marita, yemwe anali mchemwali wake wa Lazaro, ankadziwa kuti akufa adzakhalanso ndi moyo. Mwachitsanzo, mchimwene wake Lazaro atamwalira Yesu anamuuza kuti: “Mlongo wako adzauka.” Marita anayankha kuti: “Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza.” Kenako Yesu anamuuza kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo. Aliyense wokhulupirira mwa ine, ngakhale amwalire, adzakhalanso ndi moyo.” (Yohane 11:23-25) Yesu atangomaliza kunena zimenezi, anaukitsa Lazaro. Nkhani yosangalatsayi ikutithandiza kudziwa kuti mtsogolomu anthu ambiri adzaukitsidwa. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kudziwa kuti anthu akuukitsidwa padziko lonse lapansi.

Kodi ena adzapita kumwamba?

YANKHO LA M’BAIBULO: Mawu a Mulungu amasonyeza kuti kuuka kwa Yesu n’kosiyana kwambiri ndi kwa anthu 8 omwe anatchulidwa m’Baibulo. Zili choncho chifukwa chakuti anthu 8 aja ataukitsidwa, anakhalanso padzikoli. Koma ponena za kuukitsidwa kwa Yesu, Baibulo limati: “Yesu Khristu . . . ali kudzanja lamanja la Mulungu, pakuti anapita kumwamba.” (1 Petulo 3:21, 22) Kodi ndi Yesu yekha amene anali woyenera kupita kumwamba? Yesu asanamwalire, anauza otsatira ake kuti: “Ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengerani kwathu, kuti kumene kuli ineko inunso mukakhale kumeneko.”—Yohane 14:3.

Yesu anapita kumwamba ndipo anakakonzera malo ophunzira ake ena. Anthu omwe amaukitsidwa n’kupita kumwamba, onse pamodzi adzakwana 144,000. (Chivumbulutso 14:1, 3) Kodi anthu amenewa azikatani kumwambako?

Anthuwa akakhala ndi ntchito yaikulu. Baibulo limanena kuti: “Wodala ndi woyera ndiye aliyense wouka nawo pa kuuka koyamba. Pa iwo, imfa yachiwiri ilibe ulamuliro. Koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.” (Chivumbulutso 20:6) Choncho anthu amene adzapite kumwamba adzakhala ansembe ndi mafumu ndipo azidzalamulira dzikoli limodzi ndi Yesu Khristu.

Kodi palinso ena amene adzaukitsidwe?

YANKHO LA M’BAIBULO: Baibulo limafotokoza mawu amene mtumwi Paulo ananena kuti: “Ndipo ine ndili ndi chiyembekezo mwa Mulungu, chimenenso anthu awa ali nacho, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”Machitidwe 24:15.

Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti anthu ambiri omwe anamwalira adzakhalanso ndi moyo

Kodi ndi anthu otani omwe ali m’gulu la “olungama” amene Paulo ananena kuti adzaukitsidwa? Taganizirani zimene zinachitikira Danieli yemwenso anali munthu wokhulupirika. Iye atatsala pang’ono kumwalira Yehova anamuuza kuti: “Udzapuma. Koma udzauka kuti ulandire gawo lako pa mapeto a masikuwo.” (Danieli 12:13) Kodi Danieli akadzauka akakhala kuti? Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Yesu ananenanso kuti: “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Danieli ndi anthu ena okhulupirika adzaukitsidwa kuti adzakhalenso ndi moyo padziko lapansi mwinanso kwamuyaya.

Nanga ndi anthu otani amene ali m’gulu la “osalungama”? Ndi anthu ambirimbiri amene anakhalapo ndi moyo n’kumwalira koma analibe mwayi wophunzira Baibulo ndi kugwiritsa ntchito zimene Malemba amanena. Anthu amenewa akadzaukitsidwa, adzakhala ndi mwayi wodziwa Yehova * ndi Yesu. (Yohane 17:3) Amene adzasankhe kutumikira Mulungu adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wopanda malire padziko lapansi, mofanana ndi Yehova.

Amene adzasankhe kutumikira Mulungu adzasangalala ndi moyo wopanda malire komanso wathanzi

Kodi zinthu zidzakhala bwanji padzikoli?

YANKHO LA M’BAIBULO: Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Chivumbulutso 21:4) “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.”—Yesaya 65:21.

Ganizirani mmene mudzasangalalire kukhala moyo woterewu limodzi ndi achibale anu amene adzaukitsidwe. Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti akufa adzakhalanso ndi moyo?

^ ndime 15 Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.