Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Mabuku a Zilembo za Anthu Osaona Akuthandiza Kwambiri

Mabuku a Zilembo za Anthu Osaona Akuthandiza Kwambiri

1 OCTOBER, 2021

 Nsanja ya Olonda ya June 1, 1912 inanena kuti: “N’kutheka kuti ambiri mwa owerenga athu akudziwapo anthu osaona. Anthu amenewa akhoza kupeza mabuku aulere. . . . Mabukuwa amalembedwa ndi timadontho timene anthu osaona akhoza kuwerenga.” Nsanja ya Olonda imeneyo inapitiriza kuti: “Anthu ambiri osaona amayamikira kwambiri uthenga wonena kuti posachedwapa tidzalandira madalitso ochuluka padziko lapansi pano.”

 Panthawi imene mawu amenewa analembedwa n’kuti anthu asanakhazikitse njira imodzi yolembera mabuku a anthu osaona m’Chingelezi. Ngakhale zinali choncho, Mboni za Yehova zinali zitayamba kale kufalitsa choonadi cha m’Baibulo m’mabuku a zilembo za anthu osaona. Ndipo tikupitirizabe kuchita zimenezi. Panopa mabuku a zilembo za anthu osaona akupezeka m’zinenero zoposa 50. Kodi mabukuwa amapangidwa bwanji?

Zilembo za anthu osaona zimapangidwa ndi timadontho timene timakhala pakagulu kooneka ngati kabokosi kamakona 6. Chilembo chilichonse chikhoza kukhala ndi kadontho kamodzi mpaka timadontho 6. Kadontho kalikonse kamakhala ndi malo akeake m’kabokosika

Kusindikiza Pamapepala Apadera

 Popanga mabuku a anthu a vuto losaona, amayamba n’kusintha zilembo kuti zikhale timadontho tokhuthala timene anthu osaona amawerenga ndi zala. Michael Millen, amene amagwira ntchito mu Dipatimenti Yopanga Mabuku ku Patterson, New York, anati: “Kale, tinkagwiritsa ntchito mapulogalamu apakompyuta opangidwa ndi makampani ena popanga timadontho ta zilembo za anthu osaona, koma vuto linali lakuti analibe zinenero zina zimene ifeyo tinkafuna. Panopa timagwiritsa ntchito pulogalamu yathuyathu ya Watchtower Translation System imene imatha kupanga mabuku a anthu osaona m’zinenero pafupifupi zonse. Sindikuganiza kuti pali pulogalamu inanso imene imatha kuchita zimenezi.”

 Mabuku a zilembo za anthu osaona amakhala ndi nkhani zosiyanasiyana komanso mawu ofotokozera zithunzi. Mwachitsanzo, chithunzi chimene chili pachikuto cha buku lakuti Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale chinafotokozedwa motere: “Mzibambo akuyamba kuyenda panjira yokhotakhota. M’mphepete mwanjirayi muli maluwa okongola komanso mapiri osiyanasiyana.” Jamshed ndi mtumiki wothandiza komanso mpainiya. Iye ali ndi vuto losaona ndipo anati: “Mawu ofotokozera zithunziwa amandithandiza kwambiri.”

 Akatha kusintha zilembo kuti zikhale timadontho, amatumiza zimenezi ku maofesi a nthambi amene amasindikiza mabuku a zilembo za anthu osaona. Zilembozi zimasindikizidwa pamapepala olimba oti sangabowoke posindikiza komanso sangakwinyike ngakhale atagwiritsidwa ntchito kwa nthawi yaitali. Kenako amasonkhanitsa mapepalawo, kuwamanga pamodzi ndi zingwe zolimba, n’kuwatumiza kumpingo limodzi ndi mabuku ena, kapena amawatumiza paokha kwaulere ngati dipatimenti yotumiza makalata yam’dzikomo imalola kutumiza mabuku a anthu osaona kwaulere. Nthawi zina, maofesi a nthambi amatumiza mabukuwa pogwiritsa ntchito njira zachangu zotumizira katundu kuti abale osaona kapena amene amaona movutikira alandire mwamsanga mabukuwa n’kuyamba kuwagwiritsa ntchito pamisonkhano ya mpingo.

 Zonsezi kuti zitheke zimatenga nthawi yaitali komanso pamafunika ndalama zambiri . Mwachitsanzo, ku ofesi yathu yosindikiza mabuku ku Wallkill, New York, kusindikiza mabaibulo awiri okha a zilembo za anthu osaona kumatenga nthawi yofanana ndi imene amasindikizira mabaibulo wamba okwana 50,000. Baibulo lililonse lachingelezi la zilembo za anthu osaona limakwana mavoliyumu 25 ndipo ndalama zogulira zinthu zimene zimafunika kuti apange mavoliyumu 25 amenewa ndi zochuluka maulendo 123 kuposa zimene zimafunika kuti apange Baibulo wamba limodzi. * Zikuto zokha za mavoliyumu 25 a Baibulo limodzi limeneli mtengo wake ndi pafupifupi madola 150 a ku United States.

Baibulo la Dziko Latsopano la zilembo za anthu osaona limakwana mavoliyumu 25!

 Kodi anthu amene amagwira nawo ntchito yopanga mabuku a zilembo za anthu osaona amaiona bwanji ntchito yawo? Nadia, amene amatumikira pa ofesi ya nthambi ya ku South Africa, anati: “Abale ndi alongo athu osaona amavutika kwambiri, choncho ndimaona kuti ndi mwayi wapadera kuwapangira chinthu choti chiwathandize. N’zoonekeratu kuti Yehova amawakonda kwambiri.”

Phunzirani Kuwerenga Zilembo za Anthu Osaona

 Nanga bwanji ngati munthu wosaona satha kuwerenga zilembo za anthu osaona? Zaka zingapo zapitazo, tinatulutsa kabuku kachingelezi komwe kali ndi zilembo za anthu osaona komanso za anthu oona (Learn to Read Braille). Kanakonzedwa m’njira yoti munthu woona ndi wosaona aziwerengera limodzi. Kabukuka ndi kamodzi chabe ka zida zimene zinakonzedwa kuti zizithandiza anthu osaona kuphunzira kulemba zilembo za anthu osaona. Munthu amene akuphunzira kulemba zilembo za anthu osaona amagwiritsa ntchito zida zimenezi kuti azitha kulemba yekha chilembo chilichonse. Akamaphunzira kulemba zilembo za anthu osaona mwanjira imeneyi, amaziika mosavuta m’maganizo mwake ndipo amazizindikira msanga akamawerenga ndi zala zake.

“Sindifuna Kuwasiya”

 Kodi abale ndi alongo osaona kapena ovutika kuona athandizidwa bwanji ndi mabuku amenewa? Ernst, yemwe amakhala ku Haiti, ankapita kumisonkhano ya mpingo, koma analibe mabuku alionse a zilembo za anthu osaona. Choncho ankafunika kuloweza chilichonse pamtima kuti athe kukamba nkhani za m’sukulu kapena kuti apereke ndemanga pa nthawi ya mafunso ndi mayankho. Koma iye anati, “panopa, ndimatha kukweza dzanja n’kuyankha nthawi ina iliyonse imene ndafuna. Tsopano ndimadzimva kuti ndikuyenderadi limodzi ndi abale ndi alongo anga. Tonse tikulandira chakudya chauzimu chofanana.”

 Jan ndi mkulu ku Austria ndipo amachititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda komanso Phunziro la Baibulo la Mpingo, koma amavutika kuona. Iye anati: “Mabuku athu amamveka bwino kwambiri kuposa mabuku ena a zilembo za anthu osaona amene ndawerengapo. Mwachitsanzo, mabuku athu amakhala ndi manambala a masamba, mawu a m’munsi osavuta kupeza, ndiponso mawu ofotokozera bwino zithunzi.”

 Seon-ok ndi mpainiya ku South Korea ndipo ali ndi vuto losaona komanso losamva. Kale pamisonkhano ankadalira kuti munthu wina azimasulira m’chinenero chamanja uku akugwira manja ake, koma tsopano amawerenga yekha mabuku ophunzirira Baibulo a zilembo za anthu osaona. Mabuku ena a zilembo za anthu osaona amavuta kuwerenga chifukwa mwina amakhala kuti madontho ena palibepo, mizere yake ndi yokhota, kapena mapepala ake ndi opyapyala kwambiri. Koma a Mboni za Yehova amagwiritsa ntchito mapepala olimba komanso timadontho take timakhala tikulutikulu, tosavuta kuwerenga.” Iye anapitiriza kuti: “Kale, kuti ndiwerenge mabuku ofotokozera Baibulo ndinkadalira anthu ena. Koma tsopano ndimawerenga ndekha. Ndimasangalala kwambiri chifukwa ndimatha kukonzekera komanso kuyankha pa misonkhano yathu yampingo yamlungu ndi mlungu. Ndimawerenga mabuku athu onse a zilembo za anthu osaona, ndipo amandikomera zedi moti ndikayamba kuwerenga sindifuna kuwasiya.”

 Mofanana ndi mabuku athu ena onse, m’mabuku athu a zilembo za anthu osaona muli mawu akuti: “Bukuli sitigulitsa. Timalipereka ngati njira imodzi yophunzitsira anthu Baibulo padziko lonse ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo.” Tikukuyamikirani chifukwa chopereka ndalama zimenezi m’njira zimene zinafotokozedwa pa webusaiti yathu pa tsamba lakuti donate.dan124.com. Kuwolowa manja kwanu kukuthandiza kuti anthu osiyanasiyana azipeza chakudya chauzimu, kuphatikizapo anthu osaona komanso ovutika kuona.

^ In some braille systems, words are shortened to save space. In grade-two braille, for example, common words and letter combinations are abbreviated. Therefore, a book in grade-two braille is smaller than the same book in grade-one braille.