Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 136

Yehova “Akulipire Mokwanira”

Yehova “Akulipire Mokwanira”

(Rute 2:​12)

  1. 1. Yehova amadziwa anthu onse

    Omwe amam’tumikira.

    Amadziwa bwino mavuto awo

    Ndi zomwe amadzimana.

    Ngati mwasiya abale ndi nyumba,

    M’lungu akudziwa zonse.

    Watipatsa abale ndi alongo,

    Adzatipatsanso moyo.

    (KOLASI)

    Yehova akupatseni mphoto.

    Akulipireni mokwanira.

    Mubisale m’mapiko ake.

    Ndi M’lungu woona, iye sanama.

  2. 2. Nthawi zina timakhala ndi nkhawa

    Poganizira moyowu.

    Mwinanso kupeza zofunikira

    Kungamakhale kovuta.

    M’lungu akudziwa zofunikazo,

    Amamvanso mapemphero.

    Mawu, mzimu wake ndi anzathunso

    Angamatilimbikitse.

    (KOLASI)

    Yehova akupatseni mphoto.

    Akulipireni mokwanira.

    Mubisale m’mapiko ake.

    Ndi M’lungu woona, iye sanama.