NYIMBO 97
Mawu a Mulungu Amatithandiza Kukhala Ndi Moyo
-
1. Moyo umafunikira
Mawu a Mulungu
Kuti atitsogolere
M’zonse timachita,
Ndipo timasangalala
Ndi kudalitsidwa.
(KOLASI)
Chakudya chofunikira
Ndi Mawu a M’lungu.
Moyo umafunikadi
Mawu a Mulungu.
-
2. M’mawuwo timawerenga
Za anthu akale
Omwe anatumikira
Mokhulupirika.
Tikawerenga nkhanizi
Zimalimbikitsa.
(KOLASI)
Chakudya chofunikira
Ndi Mawu a M’lungu.
Moyo umafunikadi
Mawu a Mulungu.
-
3. Tikamawerenga Mawu
Tsiku lililonse,
Tidzathadi kupirira
Mayesero onse.
Ndiye tizikumbukira
Zomwe tawerenga.
(KOLASI)
Chakudya chofunikira
Ndi Mawu a M’lungu.
Moyo umafunikadi
Mawu a Mulungu.
(Onaninso Yos. 1:8; Aroma 15:4.)