Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 96

Baibulo Ndi Chuma

Baibulo Ndi Chuma

(Miyambo 2:1)

  1. 1. Pali buku limene mawu ake

    Amatibweretsera chimwemwe.

    Mfundo zake zodabwitsa n’zamphamvu,

    Limapatsa nzeru owerenga.

    Bukuli ndi Baibulo loyera.

    Olilemba anauziridwa.

    Ankakonda Yehova M’lungu wawo,

    Mzimu wake unawathandiza.

  2. 2. Analemba zokhudza chilengedwe,

    Mmene M’lungu anachilengera.

    Analembanso za Paradaiso

    Ndiponso za mmene anathera.

    Analemba za mngelo winawake

    Amene ananyoza Yehova.

    Anabweretsa mavuto pa anthu

    Koma Yehova adzapambana.

  3. 3. Masiku ano tikusangalala

    Ufumu wa Mulungu wayamba.

    Tiuze anthu uthenga wabwino

    Ndi madalitso omwe abwere.

    M’Baibulo muli zosangalatsa.

    Chakudya chochuluka kwambiri.

    Limatipatsa mtendere wambiri,

    Tiyesetse kumaliwerenga.