Pitani ku nkhani yake

Ntchito Yomasulira M’chinenero Chamanja

Ntchito Yomasulira M’chinenero Chamanja

A Mboni za Yehova amasulira mabuku ndi zinthu zina zofotokoza Baibulo zachingelezi m’zilankhulo zoposa 900. Kumasulira nkhani yomwe yachita kulembedwa kuti ikhale m’chilankhulo chinanso cholembedwa, si kophweka. Koma pamakhala ntchito inanso yowonjezera pomasulira zinthu m’chinenero chamanja. Anthu ambiri amene ali ndi vuto losamva amagwiritsa ntchito manja ndi nkhope polankhula, choncho anthu omasulira m’chinenero chamanja akamasulira mawu, amajambula mavidiyo a zimene amasulirazo. Pogwiritsa ntchito njirayi, a Mboni amasulira mabuku ndi zinthu zina m’zinenero zamanja zoposa 90.

Kodi ndi ndani amene amagwira ntchito yomasulirayi?

A Mboni omwe amamasulira m’zilankhulo zina amadziwa bwino kwambiri zilankhulozo, ndipo zilinso chimodzimodzi ndi a Mboni omwe amamasulira m’chinenero chamanja. Ambiri mwa anthuwa ali ndi vuto losamva ndipo anakula akulankhula chinenero chamanja, pomwe ena alibe vutoli koma anakulira m’banja la anthu a vuto losamva. Anthu omasulirawa amakhalanso akhama kwambiri pophunzira Baibulo.

Omasulira atsopano amaphunzitsidwa mokwanira mfundo zoyenera kutsatira pa ntchito yomasulira. Mwachitsanzo, Andrew ananena kuti: “Ngakhale kuti ndili wamng’ono ndinkapita kusukulu ya anthu a vuto losamva komanso ndinkalankhula m’chinenero chamanja, maphunziro a ntchito yomasulira andithandiza kumvetsa malamulo a chinenero chamanja. Omasulira anzanga anandiphunzitsa mmene ndingamagwiritsire ntchito bwino manja, nkhope komanso thupi langa kuti ndizitha kufotokoza zinthu molondola.”

Amamasulira bwino kwambiri

Pogwira ntchito yomasulira, omasulira amakhala m’magulu ndipo aliyense pagulupo amapatsidwa mbali yoti achite. Wina amakhala womasulira, wina amaonetsetsa kuti zamasuliridwa molondola ndipo wina amaona ngati zikugwirizana ndi mmene anthu amalankhulira komanso kuti malamulo a chinenero chamanja atsatiridwa. Kenako, amasankha anthu a vuto losamva ochokera m’madera osiyanasiyana n’kuwaonetsa zomwe amasulira kuti anene maganizo awo. Zimene anthuwo anena amazigwiritsa ntchito pokonza zimene amasulirazo. Kuchita zimenezi kumathandiza omasulirawo kuonetsetsa kuti mmene agwiritsira ntchito manja ndi nkhope m’vidiyoyo, zikugwirizana ndi mmene ziyeneradi kugwiritsidwira ntchito, komanso kuti uthenga wa m’vidiyoyo ndi wolondola komanso womveka bwino.

Omasulira M’chinenero Chamanja cha ku Finland akukambirana zoti amasulire

Omasulira m’chinenero chamanja amasonkhana limodzi ndi mipingo ya chinenero chamanja. Nthawi zambiri amaphunzira Baibulo ndi anthu a vuto losamva amene si a Mboni. Akamachita zimenezi, omasulira amadziwa bwino mmene anthu akulankhulira m’chinenero chamanja.

Womasulira M’chinenero Chamanja cha ku Brazil akujambula vidiyo ya zimene angomasulira kumene

N’chifukwa chiyani amachita khama lonseli?

Baibulo limasonyeza kuti anthu ochokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse” adzamvetsera uthenga wotonthoza komanso wopatsa chiyembekezo womwe uli m’Baibulo. (Chivumbulutso 7:9) Anthu amene amalankhula m’chinenero chamanja nawonso ali m’gulu la anthu omwe atchulidwa palembali.

Omasulira m’chinenero chamanja amasangalala kugwiritsa ntchito nthawi ndi maluso awo pogwira ntchito yofunika kwambiri imeneyi. Tony yemwe amagwira ntchito yomasulira ananena kuti: “Chifukwa choti ndili vuto losamva, ndimatha kumvetsa bwino mavuto omwe anthu a vuto losamva anzanga amakumana nawo. Nthawi zonse ndakhala ndikulakalaka kwambiri kufikira anthu a vuto losamva ochuluka komanso kuwauza za chiyembekezo chabwino chopezeka m’Baibulo.”

Amanda yemwenso amagwira ntchito limodzi ndi gulu lomasulira m’chinenero chamanja anati: “Ndimamva kuti ndikugwira ntchito yofunika kwambiri ndikamamasulira mabuku komanso zinthu zina zofotokoza uthenga wa m’Baibulo za anthu a vuto losamva kuposa mmene ndinkamvera pa nthawi yomwe ndinkagwira ntchito yolembedwa.”

Kodi mungapeze bwanji mavidiyo a m’chinenero chanu chamanja?

Pitani pa webusaiti ya jw.org ndipo muona mbali yokuthandizani mmene mungapezere mavidiyo a chinenero chamanja pa gawo lakuti: “Find Sign-Language Content.”